Friday, February 20, 2015

21 FEBRUARY: TSIKU LOKUMBUKIRA ZIYANKHULO ZATHU PADZIKO LONSE

Alick Kadango Bwanali Zomba

Chiyankhulo ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimapereka chizindikiro kwa anthu ngati mtundu. Mtundu uliwonse umadziwika ndi chiyankhulo kapena ziyankhulo zawo powonjezera pa zinthu zina monga zizolowezi ndi makhalidwe. Chiyankhulo ndi njira imodzi imene timaonetseranso zikhalidwe zathu. Motero kuti popanda chiyankhulo ndikovuta kuti mtundu wa anthu udziwike bwinobwino. Padziko lonse lapansi pali ziyankhulo pafupifupi 7,106 malinga ndi kafukufuku wa bungwe la Ethnologue. Ku Africa kuno tili ndi ziyankhulo zambiri ndipo sichachilendo kuti dera limodzi likhale ndi ziyankhulo zingapo. Uku ndi kudala kwakukulu kwa Africa ndipo tiyenera kukhala onyadira kuti tili ndi ziyankhulo zankhaninkhani. Ku Malawi kokha kuno tili ndi ziyankhulo pafupifupi khumi ndi zisanu ndi chimodzi (16). Koma kungokhala ndi ziyankhulo zochuluka sikokwanira. Funso ndi lakuti kodi ziyankhulozi zikugwira ntchito yanji pa chitukuko cha moyo wanu, dera lanu komanso dziko lathu lino.

Ziyankhulo zosiyanasiyana zimagwira ntchito zosiyanasiyana m’dziko. Zina zimagwiritsidwa ntchito m’sukulu, zina m’maofesi, zina m’mabwalo a milandu ndi malo ena ambiri. Koma kodi udindo wosankha chiyankhulo/ziyankhulo zimene tizigwiritsa ntchito m’magawo osiyanasiyana ndi wa yani? Kodi malamulo oyendetsera dziko amanena chiyani pa za ufulu wa ziyankhulo? Malamulo a dziko lino mu Gawo IV ndime 26 amamena kuti “munthu aliyense ali ndi ufulu wogwiritsa ntchito chiyankhulo chimene akufuna….” Kodi ufulu umenewu anthu wamba timaudziwa? Ngati timaudziwa, timaugwiritsa ntchito? Ngati sitiugwiritsa ntchito, ndi chifukwa chiyani? Kodi chiyankhulo chathu chikutengapo gawo lanji pa moyo wathu, pa chitukuko cha dera lathu komanso dziko lathu? Kodi tikukhutira ndi momwe ziyankhulo zathu zikugwirira ntchito?

21 February ndi tsiku lokumbukira ziyankhulo zamakolo padziko lonse lapansi. Cholinga cha tsikuli ndi chakuti anthu komanso mayiko azitha kuzindikira ndi kulingalira bwino za ubwino kapena phindu lokhala ndi zikhalidwe komanso ziyankhulo zosiyanasiyana. Dziko la Malawi monganso mayiko ambiri mu Africa muno komanso padziko lonse, lili ndi anthu a mitundu yosiyanasiyana amene ali ndi zikhalidwe komanso ziyankhulo zosiyanasiyana. Ichi ndi chinthu chabwino chomwe tiyenera kuchinyandira kwambiri. Koma timaona kuti pazifukwa zosiyanasiyana maboma ena monga boma la Malawi amangosankha chiyankhulo chimodzi kapena zingapo kuti ndizo zizigwiritsidwa ntchito m'sukulu kapena pantchito zina zaboma. Kawirikawiri china mwa ziyankhulozi chimakhala chakunja monga Chingelezi. Zoterezi zimachititsa kuti ziyankhulo zathu zina zimene sizinasankhidwe zizioneka ngati zopanda ntchito ndipo anthu amene amaziyankhula salabadiridwa n’komwe. Choncho, kumakhala kovuta kwa anthu oyankhula ziyankhulozi kuti azitha kuchita nawo zinthu zothandiza kukweza miyoyo yawo kapena dziko lawo monga pa maphunziro chifukwa alibe njira yoperekera maganizo awo. Kugwiritsa ntchito chiyankhulo chakunja sikolakwika koma monga malamulo akunenera, ziyankhulo zathu zizipatsidwanso danga lokwanira.

Kodi tsiku la 21 February linakhazikitsidwa bwanji? M'chaka cha 1952 m'dziko lomwe lero lili Bangladesh koma panthawiyo linali gawo la dziko la Pakstani ophunzira a m'sukulu zosiyanasiyana makamakama mayunivesite anachita zionetsero zofuna kuwumiriza boma kuti lilole kuti chiyankhulo cha Bengali chipatsidwe mwayi wogwiritsidwa ntchito m'sukulu. Panthawiyo n’kuti boma litagamula kuti chiyankhulo cha Urdu ndicho chikhale chiyankhulo cha fuko. Izi zinakwiyitsa anthu ambiri amene ankayankhula chiyankhulo cha Bengali. Pazionetsero zokwiya ndi maganizowa ophunzira angapo a ku yunivesite ya Dhaka anaphedwa pamene anali kulimbana ndi apolisi pabwalo la milandu la mu mzinda wa Dhaka. Kuphedwa kwa ophunzirawa kukungotsimikizira za kufunika kolemekeza ziyankhulo zathu ndipo kuti munthu aliyense ali ndi ufulu woonetsatsa kuti chiyankhulo chake sichikuponderezedwa ngakhale chitakhala kuti anthu amene amachiyankhula ndi ochepa mwa mtundu wanji.

Pozindikira za kufunika kwa ziyankhulo zathu, m'chaka cha 1999 bungwe la UNESCO linakhazikitsa tsiku la 21 February kuti likhale lokumbukira ziyankhulo zamakolo padziko lonse. Powonjezera apo, m'chaka cha 2009 bungwe la mgwirizano wa mayiko onse la United Nations linapempha mayiko kuti ayesetse kulimbikitsa ndi kuteteza ziyankhulo zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito ndi anthu. Bungweli linachita izi pofuna kugwirizana ndi zija anachita ophunzira a ku Bangladesh m'chaka cha 1952. Choncho, chaka ndi chaka mayiko komanso mabungwe okhudzidwa ndi maphunziro komanso chikhalidwe amakonza zochitikachitika pofuna kulimbikitsa ziyankhulo zathu. Zina mwa zochitikazi zimakhala zionetsero zosonyeza zikhalidwe komanso ziyankhulo zosiyanasiyana zimene zikupezeka m'mayiko kapena m'madera a dziko lonse lapansi.

Tsikuli likuyenera kutikumbutsa ife Amalawi za ziyankhulo zathu ndikuti tiyenera kuchitapo kanthu pothandiza kuti ziyankhulozi zisafe komanso kuti tizizigwiritsa ntchito m'sukulu komanso m'ntchito zina zambiri. Udindo wowonetsetsa kuti ziyankhulo zathu zikupatsidwa danga pa chitukuko cha dziko lino uli m'manja mwa eni ake chiyankhulo. Ngati sitichitapo kanthu ziyankhulo zathu zidzafa ndipo chikhalidwe chathu chidzafanso. Tisalole kuti ziyankhulo zathu ziponderezedwe ayi. Tikayamba ife kunyadira ndi kugwiritsa ntchito chiyankhulo chathu ena adzazindikira kufunika kwa chiyankhulocho ndikuchitenga ngati chiyankhulo china chilichonse. Tikumbukire kuti palibe chiyankhulo choposa chinzake.

Dziko la South Africa linakhazikitsa ziyankhulo khumi ndi chimodzi (11) ngati ziyankhulo za fuko ndi cholinga chofuna kulimbikitsa umodzi pakati pa nzika za dzikoli. M’chaka cha 2013, yunivesite ya KwaZulu-Natal ku South Africa konko inalamula kuti kuyambira chaka cha 2014 ophunzira ONSE a m’chaka choyamba pa yunivesiteyi aziphunzira chiyankhulo cha isiZulu ndi cholinga chofuna kumanga mtundu komano kutukula ziyankhulo zonse zam’dzikoli. Kodi zimenezi zingachitike ku Malawi kuno? Ophunzira a ku yunivesite angalole kuphunzira Cisena kapena Kyangonde? Mayiko ambiri a ku Ulaya ali ndi ziyankhulo zawozawo zimene amagwiritsa ntchito m’sukulu, m’mafakitale ndi ntchito zina zosiyanasiyana. Angelezi ali ndi chawo Chingelezi, Afalansa ali ndi chawo Chifalansa, Majelemani ali ndi chawo Chijelemani, ku Netherlands kuli Chidatchi, ku Japan ali ndi chawonso. Ku Malawi kuno tinasankha Chingelezi cha Angelezi ndi Chichewa pang’ono kuti ndizo tizigwiritsa ntchito pa ntchito zaboma. 21 February izitikumbutsa kuti Ciyawo, Citumbuka, Ellomwe, Cisena, Citonga, Kyangonde Cindali, Cisukwa, Cilambya, Cimambwe, Cinyakyusa, Cinyiha, Chichewa, Cingoni, Cinamwanga, Cisenga ndi ziyankhulo zina zonse zimene zikupezeka m'dziko muno nazo ndi zofunikira ndipo tsiku lina ngati eni akefe titachitapo kanthu zingathe kudzaphunzitsidwa m'sukulu zathu. Udindo ndi wathu, Amalawi. Ndi Ufulu wathunso.

Friday, April 4, 2014

Mikatoni: Mnzanga Wakalekale

Ine paja ndinafotokoza kale kuti kwathu n'ko Mbuna. Chinthu chimodzi chimene chimandipukwitsa kwathu kapena kuti ndizikonda ndikunyadira kwathu ndi anzanga ndi abale amene ndinakula ndi kusewera nawo limodzi.Ngakhale kuti chaka chimene ndinakhalako kwathu ndili wamkulu ndi wozindikira ndi pamene ndinali ndi zaka 12 zakubadwa ndipo ndipahunzirako sukulu materemu awiri, ndili ndi anzanga ambiri amene ndimawakumbukira mpaka lero. Ena a m'mudzi wathu komanso a midzi ina makamaka amene ndinadziwana nawo ku sukulu kwa Kaundama. Miston Chambadzana ndi mnzanga wakalekale. Iyeyu ngakhale sindinauzidwe kuti pali ubale wanji ndi ine koma ndimadxiwa kuti ndi mbale wanga ndithu chifukwa nyumba yawo inali kuseli kwa nyumba yathu panthawi imeneyo ndipo ife timadziwa kuti anthu onse a mudzi umodzi ndi pachibale. Amayi ake a Mistoni anamwalira iye ali wamngóno kwambiri ndipo enafe sitinawaone kapena kuwadziwa. Malinga ndi mwambo wa chikamwini, chifukwa chakuti bambo a Mistoni sanali a m'mudzimo atamwalira amayi ake iwo anachoka kubwerera kwawo. Choncho Mistoni anakula ngati mwana wamasiye ngakhale kuti bambo ake analipo. Mistoni anakula ndi achemwali ake akulu. Koma mwatsoka anamwaliranso mwadzidzidzi Mistoni ali wachichepere. Akuluakulu akamati umphawi siupha, ndimakhulupirira popeza ndinaonera Mistoni. Ndipo moyo wa Mistoni umandizizitswa kwambiri ndikumasinkhasinkha kuti kodi nçhifukwa chiyani Namalenga amalola kuti anthu ena azivutika moyo wawo onse pamene ena akukhala mu ulemerero. Chimene chimandisangalatsa ndiponso chimene ndimaphunzirapo kuchokera kwa moyo wa Mistoni ndi kusadandaula ndi mavuto. Masiku ano timamva za anthu akulowa m'mavuto ena aakulu monga lkulowerera chifukwa cha umphawi. Ena amalorera kuchotsa moyo wawo chifukwa cha mavuto. Koma Mistoni snalabadire za mavuto ake ndipo anali munthu wachimwemwe tsiku lililonse. Akadzuka sanali kudziwa kuti kodi tsikulo adya chani kapena avala chani. Mistoni ankadya chililichonse. ndikuti chilichonse chimene wachipeza. Komatu sanali wa misala. Mutamuona Mistoni akudya kamphiripiri wamuwisi wodzadza chikhato chake simukanaona kawiri. Koma tsabola anali chakudya cha Mistoni. Mistoni akalawa nsima anali deya wopemphetsa m'makomo mwa anthu kapena kudyana nawo kwa amene amuyitanira. Mistoni ndiye anali mnzanga wosewera naye mpira komanso phada. pakhomo pawo panali njira komanso bwalo lomwe ana ambiri tinkasewerapo. Nthawi yovuta kwambiri imene inkamusautsa Mistoni chifukwa cha mnyozo wa anzakefe inali yosewera mpira. Tikakhalapo ana ambiri ofukwa kusewera chikumasi (chikulunga) tinkagawa matimu awiri. Kuti tithe kuzindikirana tinkagwirizana kuti timu ina ivule malaya. Amene anali timu ya Mistoni ankalimbikira kuti iwo ndi amene avule malaya. Mistoni sankakhala ndi zovala nthawi zambiri makamaka malaya. Ankangoyenda mimba pamtunda. Nthawi zina ankakoleka kansalu ka kolala ndi momangamo mabatani kamene kanali ngati kotsalora malaya onse atatha. Sindidziwa ngati pogona ankavula koma tsiku lililonse amapezeka nako mkhosi. Ikafika nthawi yampira tinkamuvulitsa kuti tizitha kumuzindikira. Chinali chipongwe chabe ndipo ambuye azitikhululukira. Komatu Mistoni sankatekeseka nazo, iye kwakwe kunali kumwetulira ndipo ankachotsa ndikukayika potero, mpira ukatha nkukavalanso. Masiku nkumapita. Masiku amenewo a mishoni ankathandizako ana amasiye ndi zovala. Kawirikawiiri Mistoni ankalandra jekete lalikulu. Ndiye lomwelo limakhala gombeza lomwelo malaya. Tikamasewera mpira ngati ali mu timu yavala malaya ndiye kuti Mistoni ankasewera ali ndi jekete m'thupi. Koma monga ndafotokozera zimenezi sizinkamukhudza Mistoni. Tinkatha kulisintha dzina lake kukhala Mikatoni kapena Mikabodo koma iye sankalabada. Mistoni anayamba sukulu ngakhale sanapite nayo patali. Koma anadziwa kulemba ndi kuwerenga motero kuti anachitanso maphunziro a Sunday school ndi kalasi nabatizidwa. Ndimahulupirira kuti chinthu chinyaditsa kwambiri m'moyo mwake chinali kumangitsa ukwati woyerea. Kwathu masiku amenewo ukwatitsa ukwati wa pa mpingo chinali chinthu chamtengo wapatali. Anyamata ambiri ankalolera kupita ku maesiteti ku Kasungu kwa a Khondowe kuti akapeze ndalama yodzachitsira ukwati. Ndipo Mistoni anachita chimodzimodzi mpaka anakwatitsa ukwati wake ku Nkhoma madyerero anachitikira kwawo kwa mkazi m'mudzi mo Mphonde. Posachedwapa nditakumana naye anandiuza kuti ukwatiwu unatha moti anali kuwunguza kamsoti kena koti atenge chifukwa akuvutika kukhala yekha. Ine ndi Mistoni timacheza ndithu. Ngakhale kuti umphawi sunamuchokee kwenikweni Mistoni amadziwabe kuti ine ndi mnzake wakalekale. Akangomva kuti ndabwera amathamanga kuti mwina apeze ya sopo. Chinthu chimene chimandisangalatsa ndi chakuti sanatengeke ndi khalidwe lomwa mowa kapena kusuta fodya. Mistoni amapempherabe mpaka pano ndipo anandiuza kuti ndi mtsogoleri. Koma chisamaliro chapathupi ndiye chimamuvutirapo moti tikakumana chokhacho ndi chimene chimasonyeza kusiyana kwathu. Koma Mikatoni ndi mnzanga ndithu wakalekale!

Kwathu

Muno m'tawuni timangowonana. Anthufe tonse tli n'kwathu. Ena kwawo n'kumagomo, ena kwawo n'kunyanja, ena kwawo n'kuthegere, ena kwawo n'kuntherero kwa jiko, ena kwawo n'kumusha, ena kwawo n'kuthoni. Nthawi zina kwawo kwa munthu kumapanga munthu kuti akhale momwe alili. N'chifukwa chake nthawi zina ukadabwa ndi momwe akuchitira zinthu kapena momwe munthu wina akuyankhulira timafunsa ndithu kuti kwanu n'ku? Nanga inu kwanu n'ku. Ine kwathu n'kumsewu, ko Mbuna. Nkhani ya kwanu pena pake imakhala yovuta pa zifukwa zosiyanasiyana. Anthu amasintha kwawo pa zifukwa zosiyanasiyana: kusamuka, maphunziro, ntchito, ndale, malonda, banja ndi zina zambiri. Ife zonsezo tadutsamo koma kwathu sikunasinthe. Kwathu n'ko Mbuna. ndipotu kwanu ndi kwanu, ngakhale kutaoneka kosasangalatsa m'maso mwa anthu ena, kwanu ndi kwanu basi. Ine kwathu n'ko Mbuna, ku Mpenu ko Mazengera ku Nkhoma. Mudzi wathu uli m'mphepete mwa msewu waukulu wochokera ku Lilongwe kupita ku Blantyre pa mtunda wa makilomita 40 kapena mamayilosi 25 kuchokera mumzinda wa Lilongwe. Mudzi wathu wayandikana ndi midzi ina monga Bokonera, Mng'ona ndi Mdzinga. Kukhala pafupi ndi msewu waukuluwu ndi chinthu chimodzi china chimene timachinyadira kwambiri pa zifukwa zambiri. Mwachitsanzo, mayendedwe sizovuta. Kungokhala m'mbali mwamsewu nthawi ina iliyonse upeza galimoto yokwera kupita komwe ukufuna. Kulibe kabaza kwathu! Chokhacho ndimachinyadira kwambiri. Tikafuna kukamba za malonda a mumsewu ndiye pali nkhani koma siyabwalo lino! Mwina ena n'kumangomangonena za kwawo chikhalilenicho kwawoko sanakhaleko. Ife kwathu tinakhalako ndipo tikukudziwa bwino. Ine kwathu ndinakhalako ndithu ndipo ndimapitako zedi. Pa ubwana wanga ndinakhalako pamene ndinaphunzira sukulu, sitanadede 1 kenako pamene ndinali sitandede 5. Sitandede 1 ndinaphunzira pa sukulu ya Kaundama yomwe masiku a m'mbuyomo makamaka cha m'ma 1980 inali yotchuka kwambiri ndikusankhitsa ana opita ku ku sekondale. ndi zinthu zochepa zimene ndimazikumbukira pamene ndinali mu Sitandede 1 chifukwa mwina ndinali wachichepere. Koma pamene ndinabwereranso kumudzi kukaphunzira Sitandede 5 pali zinthu zambiri zimene zinakhazikika m'mutumu. Zina ndi monga anzanga amene ndinkasewera nawo kunyumba komanso kusukulu, zakudya ntchito komanso zosangulutsa zina monga zilombo! hahahahahaha! Pali anzanga ambiri amene ndinadziwana nawo nthawi imeneyo amene ngakhale pano timacheza kwambiri. Mnzanga woyamba ndi malemu Tenderetu (Sosten)... mzimu wake uziusa mumtendere. Za iyeyu ndinalemba kale. Tenderetu anali msuwani wanga amene anandilandira nditangofika kumudzi. Kuchokera tsiku limenelo tinkayenda ngati inswa. Ndidzamukumbukira mpaka kale Tenderetu! Amayi anga ndi Omama (mukafika kwathu adzakuwuzani kuti Omama ndani. Olipo omodzi basi). M'bele mwawo anabadwa ana asanu, amuna atatu, akazi awiri (Omama ndi Omayi). Panopa amayi anga amakhala ku Mchinji pa Boma m'mudzi mwa Robert. Koma ngakhale makolo anasamukira ku Mchinji mçhaka cha 1995, kwathu ndi ko Mbuna ndithu. Ngakhale mudzi wathu sukuoneka kusintha kapena kutukuka, ndimanyadirabe kuti ndiko kwathu ndipo ndimakhulupirira kuti sindikadakhala momwe ndilili chipanda kubadwira ko Mbuna.Tikafika kwathu amati kwabwera Oyaliki kapena o ku Zomba. Kwathu ko Mbuna. Inu kwanu nku?

Friday, February 22, 2013

Amalume Ndakhoza

Zinthu zimasinthadi. Kale silibwerera. Kodi lero mwana akakhoza mayeso a sitandede 8 makolo amachita chiyani? Ndikudziwa kuti kholo lililonse limasangalala mwana akakhoza. Mwana wanzeru asangalatsa makolo, atero Malemba. Komatu mwina makono kukhoza mayeso opitira ku sekondale kudasuluka! Simwakalenso ayi. Mumvere ife. Kaletu kukhoza mayeso a 8 siinali nkhani ya masewera. Chinali chinthu chopambana kwambiri pamoyo wamunthu! Ku Sekondale kunali kumwambatu, kopita owerengeka okha. Ena amapita atayimba sitandede 8 ka 8 kamene ena ka 14. Ee olipo kwathu odayamba 8 ife tisanabadwe, tidayamba sukulu mpaka kukawapeza. Ndi aphunzitsi omwe kumachita kuwalemekeza powaitana, oLove, oBatison! M'dziko muno mudali masekondale ochepa kwambiri. Ma MCC anali ang'onong'ono kwambiri mwinanso osakwana 10. Anthu amachoka kummwera kukaphunzira kumpoto - ku Borero MCC kapena ku Chawa MC kwa Lobi ku Dedza kapenanso ku Bilira ku Ntcheu. Ndiye ukalakwa mayeso a 8 panali zinthu ziwiri zoyenera kuchita. Kusiya sukulu kapena kubwereza basi. Kunalibe sukulu za wanthu zangoti mbwee lerozi. Zina zophunzitsira m'chilabu! Masiku amenewo kubwereza sitandede 8 sichinali chachilendo. Ndipo tinkakhulupirira kuti palibe angakhoze mayeso chaka choyamba. Koma mwina chaka chachiwiri kapena chachitatu. Ndiye kwinako tinkangosewera dala. Tikanavutikiranji ochimwene, omalume okadali m'kalasi momwemo ndiye iwe ukawapose? Kupanda ulemutu! Ndidafotokoza kale za kwathu - mopaza momwemo. Koma lero ndifuna ndilanduleko za kumtima. Nkhani imene nthawi zina imakhetsa tsozi komanso imandipatsa phwete. Mavutowa amationetsa zambiri - zopimitsa moyowu. Ndinalemba mayeso anga a sitandede 8 kachiwiri mchaka cha 1988. Pameneo nkuti mkulu wanga ali folomu 3 ku Dzenza. Malipiro a sukulu inali nkhani yaikulu kwambiri. Ndaiwala kuti zinali ndalama zingati. Mwina K10 mwinanso osakwana. Koma wopeza K1 anali mwana wamunthu - pwepwete mponda matiki. Mchimwene wangayu ankamulipiria ndi Ochimwene - kafunseni kwathu kuti Ochimwene ndani? Olipo omodzi okha mudzi wonse. Paja ndidanena kale kuti Omayi, Omama oliponso omodzi okha. Mukawapeza! Ochimwene odali ophunzitsi o ku MCC. Pa Malawi pano mphunzitsi ndi mphunzitsi. Nthawi imeneyo Malemu mchimwene Richard analinso fomu 3 olipirianso nkukhala Ochimwene omwe aja. Ndiye ine ndikalowenso pomwepo? Koma nanga ndikadatani munthu nzeru ndili nazo! Ndinali wanzerutu ine. Mukafunse a Maliko ku Dzalanyama akakuwuzani "N'dadziwatu ine kuti m'dzadziwa; tsono m'dadziwira ku?" hahahahahaha! Ine ndidadziwadi chaka chimenecho ndipo ndidadziwira ku Mtendere, kwa Malirana. Lidali lachisanu pa 14 October 1988. Sabata yathunthu yatha chilengezereni mayeso a sitandede 8. Ife osamva kuti mayeso anayenda bwanji. Titatsakamira m'nkhalango ya Dzalanyama. Lamya kunalibe. Kukaona mayeso ndiye kuti wina apite ku tawuni (100Km). Galimoto kunalibe. Ndiye kumangodzikhalira ngati makedzana. Tsiku limeneli linatalika kwambiri. A Hedi anapeza mwayi wokwera nawo galimoto ya Folositi kupita ku tawuni kukaona mayeso. Galimoto ikapita ku tawuni inali chaka isanapotoloke. Mbuzi mukaimasula sikumbuka kubwerera m'khola. Galimoto ikapamita kutawuni masiku amenewo imadzaza - opita kuchipatala, kuchigayo, ena akalaweko kazibeki, ena wa kwawo, ena obwerera. Galimoto inali imodzi. Timadziwa kulira kwake. Tinkaizindikira ngakhale ili mitunda isanu. Nthawi inali cha m'ma 4koloko masana. Tinamva mzizima wa landrover kuti yafika ku ofesi. Kaya chinachitika ndi chiyani kuti ifike masana tsiku limenelo? Nthawi yake inali 10 koloko usiku zingavute chotani. Ine ndi mnzanga Innocent tinangodzambatuka kusiya mpira, wautali. Pakanakhala mphoto za mpikisano wothamanga tsiku limenelo tikanalandirako. Tikuti tizifika pa chipata cha ofesi, atulukira adalayivala bambo Lipenga, anzawo a bambo anga. Ndimacheza nawo kwambiri masiku ano. Munthu wopanda zibwana. Makofi saumira. "Ndiye mukuthamangira kuti ana opanda nzeru inu. Ntchito kumangosewera mpira ndikudya maula!" Anakalipa maso ali psu ndi ukali! Jega! Thukuta lonse gwa! Maso phethipethi! Nkhope zyoli -thupili silinalinso langa. ndinamuyang'ana Innocent! Anayamba kusisima! Thanthwe long'ambikatu ndibisale momwemo! Lili kuti? Lindimeze ine lero, dziko landida! "Ndikunamatu mwakhoza pitani kwa a hedi anu akakuwuzeni." Timve ziti? Mulungu aziwakhululukira ndithu! Pa 14. Pakatikati pamwezi! Osati kuti masiku ena amakhala ngati pa 27 pakhomo pathu ayi. Ife nthawi zone panali pa 14. Koma nanga pa 14 khobidi ukabwereka kwa yani? Kwada! Tinakhala pakhonde.Pa siwa. Chimwemwe chija chinali chisoni. Ngati nthanotu! Aliyense kumangosisima. Kodi ndinalakwa kukhoza mayeso. Sukulu yonse tinakhoza anthu atatu okha ine ndekha wosankhidwira ku sukulu ya National, ya Katolika! Mulungu akandikondera bwanji kuposa pamenepa? Ndinawayang'ana amama. Anali chete. Ndinadziwa chimene chinali mumtima mwawo. Mwezi umenewo ndinali nditawasungitsa K20 (ananena kuti andisungire). Koma sanasunge. Anagula chakudya inenso ndinadya nawo! Mlandu wathu. Amama anali ndi manyazi mumtima! Musadandaule amama! Komatu ine ndalamazi ndinkakonzekera kudzapitira ku sekondale chifukwa chikhulupiriro ndinali nacho ndithu. Kumene ndinazipeza ndalamazi ndi nkhani ina. Komatu ine sindinali manjalende. Ukaipa dziwa nyimbo. Ndinkapeza kangachepe kothandizira pakhomo ngakhale ndinali wamng'ono. Zikomo madala pondiphunzitsa ntchito zanu zaluso. "Komatu paja amalume ako anati ukakhoza udzapite ku Kasungu akakupatsa fizi" Anatero amayi. Koma ku Kasungu ndipita ndi miyendo. Sikolira ndalama ya basi. Madala anali phee ngati sizikuwakhudza. M'thumba mwangamu munali K8. Ingakafike ku Kasungu? Usiku umenewo amama anayenda khomo ndi khomo kusakasaka khobi, olo! Chisoni chinakula. Ndakhozeranji ine? Lachiwiri pa 18 sukulu zatsekulira. Anzathu alowa m'kalasi. Ife tikadali kosaka makobidi oyendera kupita ku Kasungu m'malo molowera mtunda wa Dedza. Mwana wamwamuna n'kabudula mbambadi. Ndi K8 yanga pathumba ndinanyamuka ku Dzalanyama pa lole yonyamula nkhuni yaulere! Pamwamba neng'a! Alemekezeke wamwambamwambayo. M'mene imati 9 koloko mnyamata wafika mu Lilongwe, K8 yake pathumba, khadi la Kongiresi mbali inayi, wa ku Kasungu. Ndinafika ku ofesi ya Khondowe pafupi ndi depoti ya basi - Khondowe wake yemweyu mukumudziwayu. Anali bwana wa amalume anga. Kumene kuja ndinafunsa ngati kunali galimoto yopita ku Esiteti imene amagwirako ntchito amalume anga. "Ayi kulibe koma ilipo ina yopita esiteti ina ku Kasungu komweko. Utha kukwera nawo ukatsikira pa Bua usanafike pa Kasungu kwinako ukakwera matola kapena basi" anatero alonda! Palibe vuto. M'mene imati 10 koloko wanyamuka mnyamata kusiyana ndi Lilongwe kuloza Kasungu. Galimoto yaulelenso iyo! M'mutumu maganizo khumi ndi asanu. Mulungu sataya wake. Khalekhaleni uyo tafika pa Bua. Akuti basi ife tikukhotera uku. Inu mupeze matola kufika paboma kwinako mukakwera basi yopita kwa Wimbe. M'mimbamu njala ndiye yayamba kuluma. Koma K8 ndikayamba kugulira nzimbe pano ndikafika nayo? Ndinalingalira amayi anga m'mbuyomu. Ndinadziwa kuti anadziona iwo olakwa pogwiritsa ntchito ndalama zimene anandisungira. Koma akanachita chiyani munthu wa mayi ana ali ndi njala. Akanasunga bwanji ndalama pakhomo palibe ufa. Amama musadandaule. Mulungu atisamalira tonse. Ali makono bwenzi nditawaimbira foni amama kuti ndili pa Bua kudikira matola, ndayenda bwino. Ha! 1988! Kwii yaima ya polisi. Landrover yakuda ija. "Ukupita kuti ayise?" Yaulelenso? Kwera, ulipira 30tambala! Dziko ili sungalimvetse. Mphindi zochepa ndafika pa Kasungu, ndatsala ndi K7.70 yanga. Wimbe via Mtunthama! Chitero chikwangwani cha bsi pa Kasungu! Ndaipeza basi ija ili khirikhirikhiri! Mwana wamunthu atakungana pa depoti ya Kasungu. Thupi lonse tsembwe. Basi ndiye ndi imeneyi, koma ndikwera? Chipwirikiti chinali pakhomo la basicho n'nali n'sanachipenyeko m'moyo wanga. Mantha anandigwira. Kodi ikandisiya basi imeneyi ndikagona kuti? Ndiyenda bwanji? Ndiwauza bwanji amama? Amalume sakudziwa kuti ndikubwera. Mwina akadadzandichingamira pa boma pano. Poyang'anitsitsa ndinaona kuti pakhomo la basi paja panali mayufi, amene anali ndi khadi ndi amene amaloledwa kulowa. Inetu monga nzika yokhulupirika khadi ndinali nalo. Ndilephereranji kukwera basi. Ndinalimba mtima. Ndafika pakhomo, K7.70 yanga m'thumba khadi langa m'manja. "Talowa iwe!" Ine selelu, dyadyamphireni! Posakhalitsa wakhulula buleki dalayivala! Wapsa wa kwa Wimbe. Khadi langa m'thumba ndalama pamanja kuti kondakitala akafika ndimve kuti ananena kuti ndalama zingati? Kaya zikwana? Zikaperewera ndidandaula. Ndimuuza kuti ndangokhoza mayeso ndikukapempha fizi ko Malume. Monga samvetsa? Mtunthama, ikadali chidzadzire basi. Dzidzidzi, Wimbe Trading Centre! Masitolo ali ndandanda. Yafika basi. Insipekitale, kondakitala sadzaoneka! Ine tsikuu, ze! Kupisa m'thumba, ilipo K7.70. Khadi mbali inayi. Ndafikatu ine kwa Wimbe. Ndalipira 50tambala kuchoka ku Dzalanyama kuja kudzafika kwa Wimbe. Kulipiranso ku galimoto ya polisi. Lili lero ndikanati ndipereka umboni pa zazikulu zomwe Mulungu anandichitira. Ku Dzalanyama kuja tinali ndi abwana a Banda amene kwawo kunali ku Kasungu ndipo ndi amene anandiuza momwe ndingayendere. Akazi awo anali aphunzitsi anga ndipo anandiuza kuti ndikafika pa Wimbe ndikapite ku sukulu komwe bambo awo a Kayembe ankaphunzitsa. Fikani kumene kuja, chisomo chokhachokha. "Ugone, Moses akabwera akuperekeza ku Kabuma mawa m'mawa sipatali." anatero mayi ake a Moses. Kwiyo yalira nkhukhu. Mwana wakhoza. Ambuye azilemekezeka ndithu. Usiku umenewo tinachezera kucheza ndi Moses. Moses anali mnzanga pamene ankakhala ndi achemwali ake ku Dzalanyama kuja koma tsopano anali kutchuthi kwa makolo ake. M'mawa tinayenda pansi mitunda ingapo kundiperekeza kwa amalume anga. Kungondiona amalume, sichimwemwe chakecho. Moyo wanga unasinthiratu. Chimvereni zotsatira za mayeso kanali koyamba kuonetsa nkhope ya chimwemwe. Chisoni chonse chinatha. Koma amama kaya anali ali bwanji? Ulendo wa ku sukulu sunalinso wachewuchewu. K300 pathumba - Leather and Luggage, gombeza, nsapato, patapata, sitonkeni. Mungawadziwe Oyaliki? Kufika kusukulu, kulipira fizi yunifolomu zonse kukwana K104. Chenji chambirimbiri! Ambuye azilemekezeka ndithu! Uwuse mu mtendere mzimu wa amalume, Harrison Bauleni Kuchiudza (HBK)!

Wednesday, February 6, 2013

Madala: Mphawi Wachimwemwe

Kodi ndi chiyani chimakupatsani chimwemwe m'moyo mwanu? Chuma? Ntchito? Mkazi? Mwamuna? Maphunziro? Nzeru? Anzanu? Chiyani? Aliyense ali ndi chinthu chake chimene chimamupatsa chimwemwe komanso chimene amadana nacho kwambiri. Ena akapata ndalama sasowa, amafuna aliyense amupatse moni ndipo adziwe kuti zinthu zikuyenda. Anthu otere akapsa m'thumba ndi nkhope yomwe imakhala ya makwingwirima. Ndalama zimabweretsa anansi. Zikatha, anansinso amathawa. Komanso nthawi zina ndalama zimabweretsa adani. Kunja kunotu kuli kaduka kapena nkhwidzi. Wina asakwete, walakwa, avala ufiti kapena umbava. "Akusolola" timatero! Moyo wa masiku ano ndi wovuta, popanda ndalama, dziko limayima, ulemu umatha. Angakulemekeze ndani ulibe makobidi? Umasanduka chitselekwete! Koma bwanji ukangosanja? "Yes wamkulu, Zoona abwana, eetu achikulire, shuwatu big" mayina mbwee chifukwa cha ndalama. Koma kodi munthu angakhale wosangalala popanda ndalama? Enafe tidakulira m'mavuto oposa a Majoti. Nkhani ya Majoti ndi yopeka koma yathu ndiyolula ndithu! Mutha kukamba za mavuto amtundu uliwonse amene munthu padziko lapansi pano amakumana nawo. Tadutsamo. Tatulukamo. Mukamationa kusalalaku sikuti tidakulira ku Nyambadwe! Ngakhale kwa Ntopwa kumene sikungayandikireko! Koma chinsinsi cha Mulungu amachidziwa ndani? Thupili sikuti ndi chambiko chalerochi. Ndilobadwa nalo. Takula nalo. M'mavuto omwewo. Koma chinthu chimodzi chimene ndidakula nacho ndicho kupeza chimwemwe m'mavuto! Simkuluwiko! Umphawi supha munthu! adatero madala! adalasa penipeni. Bwenzitu enafe titatsogola. Malemu Opapa (madala mzimu wanu uwuse mu mtendere), ndiye chitsanzo chabwino cha munthu wosangalala pamavuto, pamtendere. Simisala. Koma kusalitsanza dziko. Kwa anthu amene amatidziwa bwino kubanja kwathu, kuseka sitiumira, ndichizolowezi. Kodi ndimayesa kuseka ndiulele, sochita kugula! Ndikumbuka masiku amenewo tikukula, titadya mgawiwa wamadzulo opapa ndi omama otafatsa kutilakatulira nthano za pa ubwana wawo, za ku sukulu, za ku Joni.. ife tikuseka chikhakhali. Uku ndiko kudali kukhala kwawo, kukula kwathu. Kuseka sikunkalira ndalama. Osati kuseka kwa masiku ano kopemphera khobidi! Lero ndapukwa opapa: Richman Bwanali Kadango kwawo ku Chitundu kwa Che Tambala m'mudzi mwa a Chawala. Myawo wapaphata kukakwatira mchewa wa ko Mbuna ku Mpenu ko Mazengera ndikusiya Chisilamu n'kuyamba kudya kapado, mbewa, kupapira masese nkukathera mu Utimiki wa Dutch! Nthawi zina makolo akamapereka mayina kapena tikamadzipatsa mayina kaya chimakhala chiyani. Inetu bambo anga pobadwa anapatsidwa dzina loti Che Madayika. Koma atakula andziwika ndi dzina loti Richman! Kaya anali matemberero kaya. Anafa osauka. Koma wosangalala, wonjoya. Bambo anga atasiya sukulu anapita ku Joweni kukasewenza ku mgodi. Pobwera kumeneko ndipamene ankabwera ko Mbuna kenako nkukayamba ntchito ku Chongoni, ku nkhalango, ife nkumabadwa. M'banja mwathu tilipo ana asanu ndi anayi, onyamata osanu ndi mmodzi ndi otsikana otatu. Tonse tilipo. Anaigwiratu makolo. Koma sizinali zachibwana kusamalira mbumba yonseyi. Madala anali munthu wolimbikira ndi wogwiragwira. Kaya ntchito zinazi anazidziwa bwanji kaya? Kaya inali mphamvu ya uchawa kaya? Komatu ankatha chilichonse: kusoka, kusema, kuluka, kukhoma! Chilichonse chochita ndi manja. Mgaiwa ukapezeka magwero ake anali amenewa. Tikavala nkhani yake inali yomweyo. Luso lina tinaphunzirako - koma izi n'zatsiku lina. Analipo masiku owawitsa ndithu nthawi imeneyo. Kudikira madala kuti abweretse chimanga kapena ufa mpaka pakati pa usiku, tulo titachita chipongozi, nkhani zitatha, m'mimba mukubangula. Akafika munthu wamwamuna khosi litalowa mkati ndi chibinyira, kusaukira mbumba nkumati adandaula, ayi ndithu! Ayambepo kukuyalirani nthano za zimene waziona tsikulo, inu njala yonse kutha nkuseka! M'mawa sikuti agonereza ayi, buli wa kuntchito! Akasakenso. masiku n'kumapita, ana nkumakula. Madala anali ndi anzawo ankhaniankhani! Akakhala pagulu, kwawo kunali kuseka ndi kuseketsa. N'kuti kulibe anzawo? Sianzawo a ku Mchinji aja adakonzetsa thupi lawo kuti lisaonongeke pa 20 July paja? Sitinalandire ulemu ndi mphatso kwa anzawo chifukwa cha kucheza kwawo? "Atate wanu nanzanga zedi, timacheza zedi anga munthu ni mphwake" ankaterotu anzawo. Ukapita kukawayendera ku Mchinji uko adasamukira atapuma pantchito amakuyendetsa benchi iliyonse mumsika kukuonetsa kwa anzawo, "mwana wanga wa ku Zomba uja ndi ameneyu". Palibe chimene chinkawasangalatsa madala koposa kunyadira ana awo. Kodi sitinapeze malo chifukwa cha anzawo? Kodi lero ku Mchinji sikwathu chifukwa cha anzawo? Kodi lero kuti tipite ku Chongoni, kwa Kankhomba, kwa Chiphazi, ku Mpalale, kwa Ndemela, kwa Nthenda sakatilandira? Suja adatikankhira galimoto ulele titatitimira ku Dzalanyama kuja atangodziwa kuti uyu ndi mwana wa Angozo (mifunda ndiye inalipo yankhaninkhani koma munthu anali mchawa)? Lero ndikamaganizira za moyo wa bambo anga chimene ndimalingalira kwambiri ndikukhala wokondwa nthawi zonse mavuto angakule maka! Chachikulu bola uli ndi moyo ndipo moyo ndi waulele. Ukadakhala wogula bwenzi ife kulibe. Chimwemwe chili mumtimamu! Umphawi supha munthu. Ngati uli ndi moyo, manja ndi miyendo uli nazo yamika Namalenga, gwira ntchito upeze chakudya lero, usakwiyire ena ngati andiwo adakulodza. Usani mumtendere opapa. Munatiphunzitsa zazikulu!

Tuesday, January 8, 2013

Tachilowa nawo

Masiku atheradi kuchitseko. Anga bodza kuti tagonera. Ndife sundwe. 2012 tatseka tione kuti 2013 wafungatanji? Koma tisanathe mtunda mu 2013 tiyang'aneko kumbuyo. Chilumika chimenechi chinali ndi zake zosayiwalika. Pali zinthu zingapo zimene zidzandikumbutsa za chaka cha 2012, zabwino ndi zoipa zomwe. Paja amati zimakhala bwino kuyambira zabwino. Kabaza M'mwezi wa February ndinagula njinga yanga ku 5 Miles - AfriCycle. Ndiyamika Nijo mnyamata amene anandisankhira njinga imeneyi. Maso kunyoza. Atandilozera njinga imeneyi ndinkaona ngati wandisankhira chikhokhololo! Koma ayi ndithu Nijo anandisankhira Mlalu weniweni! Mlalu wanga wandionetsa malo m'chaka chimenechi. Mwa malo amene ndidzawakumbikire chifukwa cha mlaluwu ndi Mwandama (kuja kunakafika Mlembi wa Bungwe la Mgwirizano wa Mayiko onse a Ban Ki- Moon, ku Zomba kuno, mudzi wa Kansonga m'chigwa cha pakati pa mapiri a Zomba ndi Malosa - malo okongola kwambiri mudzi umene ukudyetsa tawuni ya Zomba ndi zipatso, komanso ku Phalombe. Mlaluwu wandionetsa Chingale, Mayaka, Ulumba ndi malo ambiri mu Zomba muno. Imfa ya Bingu 2012 chinali chaka chosautsa kudziko lathu lino. Nthawi zina ukamaona momwe atsogoleri athu amatumbwira akakhala pampando maganizo amayamba kubwera kuti mwina n'takhala ine zimenezi zingathe. Koma zikuoneka kuti aliyense akakhala pachimpando chimenechi amaona ngati iye ndiye namalenga wa tonsefe. Komatu kumwambako Chisumphi alipo ndithu ndipo dongosolo lake palibe angalimvetse ngakhale amene mukuyti ndi aneneri olulawa! Iye ndi tsidya lina. Chili kuti lero chitsulo cha njanji? Mwina chidakathera pachipala! Achinyenyanyenya? Amayi samalani. Kuno ndi kunja kudayanja lichero! Richard (uwuse mu mtendere mzimu wako) M'bele la amayi wanga munabadwa akazi awiri, Omama ndi Omayi. Mukafuna kudziwa za mayina amenewa pitani kwathu ko Mbuna mukafunse. Akakuwuzani kuti Omama ndi Omayi ndani. Richard anali womaliza kubadwa m'nyumba moMayi. Ndi ine tinangosiyana zaka zochepa kwambiri pobadwa. Tinakulira ndi kusewera limodzi makamaka pamene tonse makolo athu ankagwira ntchito ku Ngoma (Nkhalango ya Chongoni). Atatsiriza maphunziro ku Kongwe analowa ntchito ya polisi ndipo anakwera pamaudindo mpaka kufika pa Superintendent. Koma m'mwezi wa August, Richard anatisiya kuchipatala cha Nkhoma, kwathu. Komatu dzikoli ndilovutadi kulimvetsa. Zambiri ndidzakambabe koma pano tizingopemphera kuti Mulungu asamalire ana ake, Anne, King, Tiya, Shireen ndi Yankho komanso mayi awo. Yaounde Chakachi ndinachitsendera ndi ulendo wa ku Cameroon ku msonkhano wokambirana za ziyankhulo za mu Africa makamaka pa ntchito yochita kalondolondo wa chiwerengero cha ziyankhulozi, chiwerengero cha anthu oziyankhula ndi malo amene zikuyankhulidwa mu Africa muno. Unali ulendo wosangalatsa kwa ine chifukwa chakuti kanali koyamba kupita dziko limene anthu ambiri amayankhula Chifaransa mu Africa muno. Inetu Chifaransa ndinachiphunzirapo kalekale ndili mu fomu 1 ku Mtendere zaka zimenezo. Pierre et Seydou woloweza yemwe uja anatipulumutsa mpaka ife kuoneka dolo madoda oyankhula Chingerezi chokha akulephera kunena chakudya chimene akufuna kudya mu resitilanti! Sindikunena munthu ine! Koma zinali zosangalatsa kwambiri. Pamene imatha sabata ayi ndithu ife tinali titalolera Chifalansa chokwanira kufunsira (njira). 2013 wolowa chiyimirire Ngati ndikulemba lero pa 8 Januwale ndiye kuti ndalowa nawo. Koma sindinachiyambe bwino kwenikweni. Kaya ndi Namalenga kaya ndi Dyabu kaya koma ndinapezwa ndithu munthune. Pa 31 tinapita kwa anzathu kuti tikachilowere limodzi. Ndiyetu kunali kutafuna ndikukhwasula. Dansi inathyoledwa mosaona kuti apa pali mwana wanga kapena apa pali obaba ndi omama. Tangoganizani mabanja awiri ndi ana awo onse aliyense akuthyola sitepe! Panavutatu. M'mene imati 2kaloko m'mawa woyamba wa 2013 tinanyamuka wa kunyumba. Komatu chongoti lowu, pakama thasa, inu! Namo m'mimba dzambatuku! Poyerayeratu! Kuyesa kutembenukira uku, kapena uku, kapena chafufumimba, pola, nikisi! Madzi akumwa kapena? - ndiye kukolezera! Kuyesa kukanyonyomala pamtondo, kuti mwina mpweya wokha, ayi tele kuli zii! Tetetete! Kokoliko! Ukutu nkuti mnzanga wapamphasa akungouliza wa mtendere uja! Ndipite kuchipatala? Ndi adiimiti kale! Nanga zoona kuchipatalako buku tikachite kulitsekulitsa pa 1 januwale? Ndiyetu kunali gubidigubidi kuwunguza mtela. Wapezeka panadolo. Mpwintheni! Kuyesa kugona, ayi tele, tazemberatu tulo. 6 Koloko kwacha, wa kuchanjausi kukadzithira madzi kuti mwina kapena. M'mene imati 7:30 ndafika pakhomo la chipatala. Chikwangwani chikuti lero latchuthi amatsekula 8:30! Mtsonyo wakewo! Kubwerera kunyumba, mnzanga wadzuka akujijirika ndi zanyuwele! Mpamene ndimaulula kuti bwanawe mnzakone sindidatinyanthe tanyuweletu! Anangoti kukamwa yasa! Ndiyetu masana onse kunali kuliza mkonono! Koma ayi lero suyu tikupumayu! Koma wachewuchewu! Talowa ndithu ndipo tiyamika Lezayo kuti watikondera, Chichewa cha lero! Ticheza m'chaka chimenechi!

Thursday, July 19, 2012

July 20, 2011: Tsiku Losayiwalika m'Moyo Mwanga

Kulemba nkhani sichinthu chapafupi! Nthawi zina mtima umakhala ukufuna koma thupi limakhala lolefuka, nthawi imakhala yochepa, zosokoneza zimakhala zambiri. Nanji masiku ano a facebook, twitter, nyasatimes ndonzawo wokhala pansi n'kulemba nkhani kapena ndakatulo ndi munthu. ndimalakalaka ndithu nditamalemba pafupi[afupi ndipo nkhani ndi zambiri m'mutumu koma danga lochitira zimenezi ndilo lisowa ndithu. Choncho tsamba lino lakhala lili mbe chifukwa chotangwanika ndi zina ndi zina. Zina zaphindu, zina zopanda mpake pomwe. Chatsitsa dzaye ndi malingaliro amene ndakhala nawo sabata imeneyi. Kwa ine ndi onse a kubanja kwathu sabata ino chaka chatha (2011) inali nthawi yowawitsa chifukwa bambo athu anali ali m'chipatala. Mwezi wa June chaka chatha ndinapita ku Mchinji kukaona abambo anga nditamva kuti sanali kupeza bwino. Pobwerera ku Zomba chiyembekezeo ndinali nacho kuti adzapeza bwino. Patapita sabata zingapo, m'mawa wa pa 18 July ndinalandira lamya kuti madala agonekedwa m'chipatala. Mantha anandigwira chifukwa aka kanali koyamba m'moyo mwanga komanso mwa madala kugonekedwa m'chipatala. Kutacha ndinanyamuka wa ku Mchinji. Nditafika kuchipatala madala anauzidwa kuti ndafika ndipo anandiyang'ana. Ndinawayandikira kuti ndithe kuwafunsa momwe akumvera m'thupi mwawo, ndinaona pamaso pawo chilakolako chofuna kundiyankhula koma ndinadziwa kuti thupi linali lofowoka. Sindidziwa kuti madala anafuna kundiuza chiyani! Ndinawagwira dzanja koma sanasonyeze kuti ndawagwira! patapita mphindi pang'ono ndinachoka n'kukhala pambali n'kulonjerana ndi amayi komanso abambo aang'ono amene anali kudwazika matendawo. Anandipatsa uthenga wachilimbikitso koma sichinakwanire. Madala akadandiyankhula mwina ndikadalimba mtima kuti akupeza bwino. Usiku ndinapita kunyumba kukagona mtima uli wosweka ndithu. Unali usiku wautali. M'mawa kutacha pa 19 ndinapita kukawazonda. Sindinaopne kusintha kwenikweni. Mantha anandigwira ndipo ndinadziwa kuti madala sadzandiyankhulanso. Usiku wa pa 19 unandisautsa kwambiri. Sindinagone. M'mawa pa 20 July. Kutacha m'mawa ndinamva mauthenga akuti dziko la Malawi lili pamoto. Anthu anali kuchita zipolowe zosonyeza kukwiya ndi ulamuliro wa dziko lino. Mkazi wanga anali ali ku Mzuzu ndipo anandiuza kuti wakwera basi m'mawa koma akulephera kutuluka mumzindawu chifukwa cha mfuti zimene zinali kulira. Nkhawa inandigwira. Ndinamvanso kuti ku Lilongwe, ku Blantyre ndi maboma ena zinthu sizinali bwino. M'tawuni ya Mchinji munali bata ngakhale kuti m'misewu munali apolisi ochuluka kuposa nthawi zonse. 12 Koloko Masana Nthawi yowonera odwala itakwana cham'ma 12 ndinanyamuka kuti ndikazonde madala. nditatsala pang'opno ndinamva foni ya amayi kundiuza kuti ndifulumire. Mtima wanga unagunda, thupi linachite tsembwe! chongofika m'chipinda momwe munagona madala nkhope ya amayi inandiuza zonse. "Aliki bambo ako ulendo uwu"! Inali nthawi yowawitsa m'moyo mwanga! Ndinayandikira ndikuwagwedweza madala koma sanasunthe ngakhale pang'ono! Apita madala! Tsopano chaka chaka chatha. Madala anagona ku Mchinji mwakufuna kwawo. Sanafune kubwerera kwawo ku Chitundu ku Dedza. Ku Mchinji anasamukirako 1995 atapuma pantchito. Ku Mchinji kuanasanduka kumudzi kwawo, kumudzi kwathu. Anali ndi abale andi abwenzi ambiri. Onse anachitira umboni patsiku lowasunga madala pamene anafika mu unyinji wawo. Kufika kwa unyinji umenewu kunandikumbutsa ndipo kudzapitiriza kundikumbutsa moyo wa madala - kuseka ndi aliyense! Madala anali munthu wokondwa nthawi zonse ndipo ndiyamika Mulungu chifukwa cha mphatso imeneyi. Akanakhala wopanda mphatso imeneyi mwina bwenzi pano tikukamba nkhani ina. Ndi chikhumbokhumbo changa kuti ndikumbukire moyo wa bambo anga pofotokoza zina zimene zinawathandiza kukhala moyo wosangalala ngakhale atakumana ndi mavuto amtundu wanji pamoyo wawo. Tinakhalapo moyo wovutika kuthupi koma mu mtima mokha tinali anthu osangalala, achimwemwe nthawi zonse chifukwa cha madala. Mzimu wanu uziusa mumtendere Madala ndipo ngati kumene muliko ngati n'kotheka kuchita nthabwala nkumaseka, pitirizani mpaka tidzaonanenso nkusekera limodzi!

Thursday, June 9, 2011

TABWERANSO

Pepani kwambiri abale amene mwakhala mukutsatira tsamba lino kuti tinakhala ngati tati zii, osalemba kalikonse. Tinachita kuyiwala chizimba cholowera bwalo lino. Koma ndifuna kukulonjezani kuti tsopano bwalo lino talitsekulanso ndipo pakhala pakukambidwa nkhani zambiri. Masiku apitawa tinayenda kwambiri ndipo pali nkhani zosangalatsa zofunika kugawana. Ingopitirizani kuwerenga ndikupereka ndemanga. Tilandireni

Monday, July 19, 2010

Mwana wanzeru akondweretsa makolo




Kutsiriza maphunziro ndicho chinthu chimodzi chopambana m'moyo wa munthu. Iyi ndi nthawi imene munthu amatsiriza osangoti maphunziro okhawo ayi, komanso gawo la moyo limene wakhalamo nthawi yaitali ndithu. Komanso ndi nthawi imene munthu amayembekezera kuyamba moyo watsopano. Iyi imakhalanso nthawi yodziwunika ndikudzisanthula pamene unachita bwino komanso pamene sunachite bwino kuti mwina m'moyo wina umene ukukawuyambawo ukachite mosiyana ndi m'mbuyomo. Komanso imakhala nthawi yolingalira za moyo watsopano uli nkudza. Pachifukwachi ena amakhala ndichimwemwe poganizira kuti mwina tsopano asiyana ndi moyo wovuta ndipo akukayamba moyo watsopano. Koma ena amakhalanso ndi nkhawa kuti mwina akukayamba moyo wovuta kusiyana ndi wam'mbuyomu.

Ndikumbuka kuti pamene ine ndinali kutsiriza moyo wa ku sekondale, ndinali ndi chimwemwe kuti tsopano sindidzasambanso madzi ozizira m'mawa ndipo ndizidzadzuka nthawi imene ndikufuna. Panthawiyi ndinaona kuti tsopano ndapeza ufulu wochuluka ndipo moyo wa ku sukulu ndinawuona ngati ukapolo. Komabe ngakhale izi zinali chomwechi, ndinalibe ndi nkhawa pa za moyo wam'tsogolo. Choyamba chinali chakuti kodi mayeso ndikhoza? Nanga ndikhoza bwanji? Ngati sindikhoza bwino, ndidzachita chiyani? Kodi ndidzapeza mwayi wa ntchito? Idzakhala ntchito yanji? Ndizidzalandira ndalama zingati? Nanga ngati ndikhoza bwino, ndidzasankhidwa kupita ku Yunivesite? Kodi ndikasankhidwa kupita ku Yunivesite ndikachita maphunziro anji, nanga adzandipatse malipiro a sukulu ndani? Kodi ndikakhoza n'kudzapeza ntchito yapamwamba? Ndikhukupirirra awa ndi ena mwa mafunso amene achinyamata amene akukonzekera kutsiriza maphunziro awo nthawi ino akulimbana ndi kupeza mayankho ake.

Dzana Loweluka pa 17 July linali tsiku lotsanzikana ndi ophunzira a Fomu 4 pasukulu ya Mlanda ku Ntcheu. Tinayitanidwa ndi mwana wathu Priscilla kuti tikhale nawo pamwambowu. Sitinachione chofunikira kuti tichoke ku Zomba kukafika ku Ntcheu chifukwa cha mwambo umenewu chifukwa panthawi yathu makolo sankaitanidwa ku mwambo wamtunduwu. Komansotu panthawiyi ophunzirawa amakhala asanalembe mayeso awo ndipo sakudziwa ngati adzakhoze kapena ayi. Koma mwanayu anachonderera ndithu kuti ife tipite ndithu tikaonelere mwambowu.

Ndinanyamuka ku Zomba cham'ma 8 koloko m'mawa pamodzi ndi Onyamata ndipo tinafika ku Mlanda cham'mapasiti 10. Titangofika Priscilla anatithamangira akusekerea kudzatilonjera. Apatu n'kuti akukonzekera kulowa mu Holo imene mumachitikira mwambowu. Kenaka mtsikana wina anabwera kudzatitenga n'kutilowetsa muholomo. Kunabweratu makolo ambiri komanso anthu oyimira magulu osiyanasiyana monga mafumu (a T/A Masasa anali kumeneko), a mpingo komanso abizinesi. Mwambo wake unali wosangalatsa kwambiri. Kunali magule, kuyimba, masewero ndi zochitikachita zambiri. Alendo onse pamodzi ndi ophunzira analandira chakudya ndipo chinthu chosangalatsa makolo kudyera limodzi ndi ana awo kusukulu.


Ine ndinasangalala koposa kuona kuti mwana wathu anali mmodzi wochita nawo masewero. Mwana wathu ndi wofatsa kwambiri moti sitinkayembekezera kuti angathe kuyima pagulu la anthu n'kukamba zomveka. Koma ayi ndithu patsikuli iye anali kuchita gawo lowulutsa mawu kunyumba ya mphepo ya Zodiak! Ndinakondwera kwambiri. Koma nthawi yopambana kwambiri imene ine ngati kholo sindidzayiwala chifukwa ndinazizwa kwambiri inali pamene anali kupereka masatiketi kwa ana amene anachita zinthu zopambana panthawi imene anali pasukulupa. Masitifiketi oyamba anaperekedwa kwa mwana aliyense amene anali kutsiriza maphunziro ake pa sukulupa. Koma gulu lachiwiri la masatifiketiwa linali operekedwa kwa okhawo amene anachita bwino kuposa anzawo mu gawo lina lake monga pa phunziro lililonse, mavalidwe, mayimbidwe, ndi zina. Zinali zoseketsa ndizosangalatsa kumva kuti wina anasankhidwa kukhala wolawirira pochita china chilichonse, komanso wina anasankhidwa kukhala munthu wokonda kulangiza anzake. Panalinso mwana wina amene anasankhidwa kuti amakonda kumwetulira ndi kusekerera nthawi zonse. Mwana ameneyu ndi wachimwemwe ndipo kwake nkuseka basi. Mayi ake ndimawadziwa ngatinso munthu wokonda kuseka ndikuseketsa moti sindidadabwe nditamva kuti anasankhidwa kukhala munthu womwetulira nthawi zonse. Panalinso kamtsikana kamene kanasankhidwa munthu wodziwa kuyimba. Mwana ali ndi nthetemya uyo. Atalandira satifiketi yake anapemphedwa kuti angotilawitsako pang'ono luso lake. Holo yonse inamumbera m'manja mwanayu atangoyimba ndime imodzi yokha.

Tsopano olengeza mayina anali kufika kumapeto wa mndandanda ndipo ine ndinali kuganiza zonyamuka poganiza kuti mwambo wopereka masatifiketi tsopano watha. Kenaka ndinangomva kuti “wophunzira amene anachita bwino kuposa onse mu phunziro la Chingerezi, Priscilla Chimtolo.” Ine mtimawu unangoti myuuuu! Ndinadzidzimuka koposa ndipo sindinakhulupirire. Nditacheukira pamene anakhala Priscilla ndinangoona kamwana kanga kakubwera kali mwee kudzandikupatira. Ndinali ndi chimwemwe chodzadza tsaya. Ndinali ngati ndikulota. Ndinaonanso kuti naye ali wosangalala kwambiri kuti anapata mphoto imeneyi komanso chifukwa chakuti ine ndinafika kudzachitira umboni mwambo umenewu. Pamene ndimanyamuka ndinali munthu wosangalala ndipo njira yonse ndinayenda ndi chimwemwe chokhachokha. Ndili ndi chikhulupiriro kuti zimenezi zimuthadiza Priscilla komanso ana ena onse amene anachita bwino kuti alimbikire kuti pamayeso awo otsiriza adzachitenso chimodzimodzi. Mwana wanzeru akondweretsa makolo.

Wednesday, July 14, 2010

Mnzanga, Happy Wapita

Dzulo madzulo nditaweluka kuntchito monga mwachizolowezi ndinapita kokachita masewero olimbitsa thupi. Ndinabwerako cha m'ma7koloko usiku. Nditafika kunyumba ndinanyamula chisusu changa kuti ndikadzithire madzi kuchotsa chitungu. Polowa kuchipinda chogona ndinasangalala koposa chifukwa ndinapeza a Nyagondwe akundisitila zovala. Nditangolowa kubafa ndinamva kuyitana kuchokera kwa mayi. Ndinatuluka kuti ndikamve kuyitanako.

"Kodi paja Happy dzina la abambo ake ndani? anandifunsa nditangosuzumira pakhomo la kuchipindako. "Nyirenda?" Anapitiriza kufunsa ndisanayankhe funso loyamba lija.

"Ee, bwanji?" ndinafunsa ndi chidwi.
"Wamwalira, akulengeza pa wayilesi kuti Happy Chokoma Nyirenda wa ku Nkhatabay amene amadwala kuchipatala cha Zomba wamwalira."

"Hiii Happy inu. Mpaka wamwalira ndi mutu womwe uja" Ndinasendera ndikukakhala pa bedi kuti mtima ukhazikike.

Happy anali mnzanga ndipo tinadziwana m'chaka cha 2003 kuno ku Zomba. Tinadziwana chifukwa cha mnzanga wina Jonah Mphanda amene ine ndinaphunzira maye ku sekondale ku Mtendere. Panthawiyo Jonah ndi Happy ankagwira ntchito ku Interaide. Kenaka awiriwa anasiya ntchito ku Interaide ndipo Happy anayamba kugwira ntchito ku Spar.

Sabata zitatu zapitazo, Jonah anandiyimbira foni kundifotokozera kuti Happy wagonekedwa kuchipatala ndipo akudandaula mutu. Tsiku lomwelo ndinapita kukamuona ndipo tinacheza nandifotokozera kuti mutu ndi umene ukumusautsa koposa. Ndakhala ndikukamuona koma zimaoneka kuti matendawa sanasinthe mpaka pamene dzulo chakum'mawa amamwalira.

Happy amachokera ku Nkhatabay. Ndidzamukumbukira Happy chifukwa chokonda kuseka ndi nthabwala. Tikakumana timakonda kukamba zoselewula ndipo mwa dzina lake iye anali wosangalala nthawi zonse.

Mzimu wako uwuse mu Mtendere Happy.

Friday, July 9, 2010

oTenderetu


Nthawi zina ndikakhala phe, nzeru zimandithera ndikaganiza kuti kodi imfa imabwera bwanji pamoyo wamunthu ndipo kuti kodi analenga imfa ndani? Nanga kodi munthu akafa amapita kuti? Mwina nthawi zambiri pamene tili ndi moyo wangwiro, zonse zili myaaa timayiwalako zoti kunja kuno anthu amafa n'kutsikira kuli chete osadzamutemanso gaga. Koma zovutazi zikagwa pakati pathu mpamene timadzidzimuka n'kumati kodi paja moyowu umatha ndithu. Ine ndimaona kuti nthawi imene mnzathu akuyikidwa m'manda ndiyo nthawi yowawitsa chifukwa umakhala umboni woti basi mnzathuyu apa lake watseka. Nthawi zambiri ikafika nthawi imeneyi misozi imatsika ndithu ngakhale malirowo akhale kuti sakundikhudza kwenikweni. Imfa imene mpaka pano imandipweteka kwambiri ndi yamzanga, msuwani wanga, mchimwene wanga, Tenderetu (Tiyenderetu). Imfa imeneyi imandipatsa maganizo ndi mafunso ambiri amene mpaka lero sinditha kupeza mayankho ake.

Ine ndi Tenderetu tinadziwana m'chaka cha 1983 kumudzi kwathu ko Mbuna ku Lilongwe. Chaka chimenecho makolo anga anaganiza zoti mayi anga pamodzi ndi ine komanso mng'ono wanga Gregory ndi alongo anga Jestina ndi Chisomo tipite kumudzi kuti amayi akayang'anire ntchito za kumunda ndipo ife tikaphunzire sukulu komweko. Iyi ndi nthawi ina yowawitsa m'moyo mwanga chifukwa mpaka pano sindimvetsa chimene makolo anga anachitira zimenezi, kutisiyitsa sukulu yapamwamba, nyumba ndi moyo wabwino kupita kumudzi. Iyitu inalinso nthawi imene kunabadwa abale anga ena awiri amapasa, Symon ndi Sibongire. Kubadwa kwa ana amenewa sindidzakuyiwala chifukwa ine ndi amene ndinali mlezi wothandiza amayi anga. Lachitatu lililonse ndinkajomba kusukulu kuwaperekeza amama kusikelo ya anawa ku Chipatala cha Nkhoma chomwe chili pamtunda wa makilomita pafupifupi 10 kuchokera kwathu.

Titangofika kumudzi ko Mbuna kuchokera ku Dzalanyama Forest komwe bambo anga ankagwira ntchito panthawiyo, tinaona zinthu zambiri zosintha chifukwa aka kanali koyamba kwa ife kukhala kumudzi motero sitinasangalale nkomwe kuti tizigona m'nyumba ya udzu, kukakhala pansi kusukulu pamene tinasiya abambo okha m'nyumba yabwino ya malata. M'mawa kutacha ndinapita kukakhala pakhonde la nyumba ya agogoa anga okondedwa, Onganga (mzimu wawo uziwusa mumtendere ndipo ndidzalembanso za gogo ameneyu, amene ndimamukumbukira nthawi zonse chifukwa cha mtimwa wake wachifundo. Timakusowani Onganga). Ndikuothera kadzuwa pakhonde paja ndinaona kamnyamata kamsinkhu wanga katakhala pakhonde la nyumba ya Omayi (achemwali a amayi anga). Maso athu atangoti tha, tonse tinamwetulirana chifukwa tinazindikirana.

Tenderetu anali mphwawo wa bambo anga aakulu. a Mapondera (amuna a Omayi, achemwali a amama). A Mapondera ankachokera ko Mdzinga mudzi umene uli tsidya lina la mudzi wathu kungodumpha msewu wawukulu. Iwowa anali kukhala m'mudzi mo Mbuna ngati kuchikamwini. Amayi a Tenderetu anamwalira pakati pa 1980 ndi 1981. Choncho atangomwalira mayi ake, amalume akewo, aMapondera, anamutenga iye pamodzi ndi abale ake Nana ndi Maseko kuti azikakhala nawo ku Chongoni Forest ku Dedza komwe iwo ankagwira ntchito panthawiyo. Abambo anga anagwirakonso ntchito ku Chongoni ndipo ndikumene ine ndinabadwira koma tinasamukako 1980 kupita ku Dzalanyama. A Mapondera atapuma ntchito 1982 anakakhala kumudzi ko Mbuna pamodzi ndi mwana wawo Richard ndi aphwawo aja, Tenderetu, Nana ndi Maseko.

“Alick” anandiyitana Tenderetu nandikodola. Nthawi yomweyo ndinapita kukamupatsa moni ndikumufunsa kuti ali kalasi yanji. Iye anali sitandede 3 pamene ine ndinali sitandede 5. M'zaka zakubadwa iye anali wamkulu ndi zaka ziwiri koma tinali ofanana misinkhu. Kuchokera tsiku limenelo Tenderetu anali mnzanga waponda apa ine mpondepo. Sitinkasiyana kulikonse. Kusukulu tinkapitira limodzi, kuwelukira limodzi, kusewerera limodzi, kudyera komanso kugonera limodzi. Nthawi imeneyo tinkagona kumphala pamodzi ndi amalume anga aChadza. Usiku pogona tinkafunda bulangete limodzi, ndipo nthawi zambiri timacheza mpaka mwina aChadza kumachita kutiletsa kuti tigone. Panthawiyi n'kuti iwowo anali mu sitandede 8 koma anali kubwereza kachisanu ndi katatu. Tikakondwa kwambiri tinkafika pomaphaphalitsana makofi kapena kutibulana zibakera ndithu mpaka wina athawe. Izi zinkangokhala zosewera ndipo sitimadana ngakhale wina atamenya mnzake kwambiri. Nthawi yamango itakwana ine ndi Tenderetu tinasula timipeni kuchokera ku misomali ya 12 ichesi kuti tizikasendera maboloma. Timati tikangokonza kuti lero tikakhaulitsa mango timayambira ku Bathe (kumunda kwathu), kuchoka apo tili ku kuseli kwa Bathe (kumunda kwa Omayi) mpaka kukamalizira ku Dondo (kumunda kwa amalume ake a Tenderetu). Tikamabwera kumeneko mimbazi zili mzuu, kukhuta, pakamwapa pali noninoni, m'manja monsemu midondolozi ya madzi a mango italemberera. Tikatero ndiye kuti nsima yamadzulo kumangokhala kuyikandakanda basi usiku kumangogeya ndi kutuluka panja kukataya madzi.

Kumapeto a chaka chimenecho titatsekera sukulu komanso titakolola dzinthu abambo anga ananena kuti tonse tibwerere ku Dzalanyama. Inali nthawi yovuta kwa ine kuti ndisiyane ndi mnzanga wapamtima. Komabe sindafune kuphunziranso kumudzi. Nditafika ku Dzalanyama ndinamulembera Tenderetu kalata kumufotokozera momwe ndinayendera. Koma nthawi imeneyo kunali kovuta kuti tizilemberana makalata pafupafupi chifukwa tinali pamsinkhu umene sitinkatha kudzipezera ndalama zogulira masitampa. Kwa zaka zitatu ine sindipitenso kumudzi ndipo sindinaonanenso ndi Tenderetu.

M'chaka cha 1986 abambo anga ananditenga kuti akandionetse kwawo ku Chitundu ku Dedza. M'banja mwathu palibe amene ankadziwa kwawo kwa abambo anga ndipo amayi akuti anapitako kotsiriza m'chaka cha 1976. Choncho ine ndinasangalala kuti ndidzapita kukaona kwawo kwa abambo anga chifukwa kunali abale awo amene ankakonda kudzationa koma ife tinali tisanaone kumene ankachokera. Popita kumeneko tinayima kumudzi ko Mbuna. Aka kanali koyamba kuonana ndi Tenderetu m'zaka zitatu. Pochoka ku Chitundu ine ndinatsalira kumudzi kuti ndichezeko ndi mnzanga. Tonse tinali titakula tsopano, zosewera zathu zinali zitasintha. Panalibenso zomenyana. Tsopano timangosewera mpira basi. Panthawiyi n'kuti Tenderetu atasintha dzina, kukhala Sosten. Komanso anali atameta kugule ndye ena ankamuyitana kuti oTenderetu kapena oSositeni monga mwa mwambo wake. Amalume ake anamwalira chaka chomwecho (1986) m'mwezi wa March. Koma pamene ankamwalira n'kuti atamupatsa ndalama yoyambira bizinesi yogula mafuta a galimoto kwa magalimoto odutsa mumsewu popeza mudzi wathu uli m'mbali mwamsweu wawukulu wa Blantyre-Lilongwe. Iyi inali bizinesi imene inali yolula oanthawi imeneyo. Panthawiyi nkuti amalume ake atasamuka m'mudzi ndikukamanga nyumba yaikulu m'mbali mwa msewu. Amalume ake asanamwalire anapempha oMayi kuti iwo akadzamwalira adzasunge ana onse atatu amasiye) Tenderetu, Nana ndi Maseko). Choncho Tenderetu anapitiriza kukhala ndi oMayi komanso msuwani wake weniweni, Richard. Ndinapemha kuti chaka chimenecho ndiphunzire kumudzi komweko koma abambo anga anandikaniza. Nditacheza kwa mwezi umodzi ine ndinabwerera ku Dzalanyama kukapitiriza sukulu. Nditalemba mayeso a Sitandede 8 mu 1987 ndinapempha kuti ndikachitenso tchuthi kumudzi ndipo anandiloleza. Chaka chimenecho tinacheza kwambiri ndi Tenderetu. Apatu tsopano iye anali kupeza ndalama zambiri chifukwa cha bizinesi ija. Nthawi zina ndinali kumuthandiza kukochola magalimoyo komanso kupopa ndikunyamula mafuta. Chaka chotsatira ine ndinasankhidwa kupita ku Mtendere secondary school ku Dedza. Uwu unali mwayi wanga chifukwa ulendo uliwonse popita ndipobwerera kusukulu ndimayima kumudzi kwathu kwa masiku angapo ndipo izi zinandipatsa mwayi womacheza ndi Tenderetu pafupipafupi mpaka nditamaliza maphunziro anga mu 1992. Nthawi zina popita kusukulu ankandipatsako ndalama zokadyera ndipo ulendo wina anandigulirako malaya. Ndinanyadira koposa.

Nditangolemba mayeso anga a Fomu 4 ndinapempha makolo anga kuti ndikadikire mayeso kumudzi. Iwo anandilora ndipo ndinasangalala kwambiri. Nthawi imeneyi ndinamuthandiza kwambiri Tenderetu pa bizinesi yake ya mafuta. Analinso kugula ndi kugulitsa mbewu, ufa ndi zinthu zabiri zopezeka m'magalimoto odutsa. Tenderetu sanasowe chilichonse. Anali kusamalira pakhomopo tsopano ndiye. Anali wopatsa kwambiri. Mudzi wonse unamudalira. Iye anali wakhama pantchito ndipo samalola zibwana kapena zaulesi. Panthawiyi n'kuti Sadam Husein yemwe anali mtsogoleri wa dziko lija la Iraq atatchuka kwambiri chifukwa chokaputa dziko la Kuwait m'chaka cha 1990. Tenderetu anali munthu wokonda kumvera wayilesi kuti azimva zomwe zikuchitika kunjaku. Kulimba mtima kwa Saddam kunamusangalatsa ndipo chifukwa chakuti naye sanafune kuti anthu azimutola poti ndimwana wolemera anadzitcha kuti Sadam. Iye sikuti anali waukali kapena wokakala moyo ngati Sadam koma anamusilira Sadam chifukwa cholimba mtima. Dzina la Sadam anatchuka nalo kwambiri.

Mayeso anga atatuluka ndinasankhidwa kukapitiriza maphunziro ku Chancelllor College. Apa tsopano ndinadziwa kuti tidzatalikirana ndi Tenderetu. Chaka chomwecho iye anasiya sukulu mu Sitandede 8 ndikupitiriza bizinesi yake. Anapeza malo ake ndikumangapo nyumba. Mu 1995 Tenderetu anakwatira. Ukwati unachitika ndili kusukulu motero sindinathe kukhala nawo. Ndinakhumbira kwambiri. Ngakhale Tenderetu anakwatira, anapitiriza kuthandiza oMayi komanso anthu ambiri am'mudzi mwathu ngakhalenso achilendo. Anapala maubwezi ambiri chifukwa cha bizinezi yake. Analimbikira kulima komanso kugula mbewu zosiyanasiyana. Atazindikira kuti bizinesi ya mafuta inali yosadalilika chifikwa cholondedwa ndi apolisi iye anaganzia zotsekula sitolo. Anamanga sitolo yake yayikulu momwe munali katundu wosiyanasiyana. Anthu ambiri anali kudzagula katundu ena pangongole. Tsiku lina tikucheza nditapita kukamuona kuchokera ku Zomba anandiuza kuti nthawi zina saona kufunika kwa maphunziro chifukwa aphunzitsi amene an'kamuphunzitsa ku pulayimale anali kuvutika kwambiri ndipo kuti ena mwa iwo anali kulephera kubweza ngongole zimene anakatenga musitolo yake. Iye ananena kuti ana sangalimbikire sukulu ngati aphunzitsi akukakongola ndalama kwa anthu amene sanapitirize maphunziro. Pena ndinagwirizana naye makamaka ngati timapita kusukulu kuti tidzakhalae ndi moyo wabwino. Koma nkhani ya aphunzitsi ndi ina yapadera. Tenderetu anali ndi mfundo zake ndipo anali wokonda mtsutso pa nkhani zosiyanasiyana. Chinthu china chimene iye ankakanitsitsa kuti sangachite ndiye kusunga ndalama zake ku banki. Mawu ake anali akuti iye saona chifukwa choti azikakhalira pmazele chifukwa cha ndalama zake zomwe.

Pasitolo pake panali pachibulo. Sipankasowa munthu. Panali posewerera ntchuwa, panali pogulitsira nzimbe, nthochi, panali pomwera fanta, panali powusira anthu apulendo. Ena mwa iwo maka oyenda panjinga kuchokera mitunda ya Chitundu anali kusungitsa njinga zawo n'kukwera magalimoto wa m'tawuni. Tenderetu anali mlerakhungwa chifukwa sanasankhe anthu ocheza nawo, akulu, ana, achinyamata, olemera, osauka, owadziwa, achilendo. Chifukwa cha mtimawu anthu tsopano anamutcha Bakili. Chifukwa cha ichi, anthu anamudalira koposa. Anamusankha kukhala wapampando wa sukulu komiti komanso wapampando wa chipani ku Bathe Area. Uwutu sunali udindo wamba. Nthawi imeneyo phungu woymira derali anali Wolemekezeka a Louis Chimango moti pamene iwowa anali kuyendera derali aakuluakulu ake amene amayenda nawo anali a Tenderetu. Chinali chinthu chopambana kuwona mnzanga atafika pamenepa. Nthawi zambiri tikamacheza anali kukamba nkhani za ndale ndi chidwi ndipo kawirikawiri anali kufuna kudziwa kuti ine ndili mbali iti chifukwa chakuti ndimakhala kummwera. “Ndale zikuyenda bwanji kum'mweraku?” Ankakonda kufunsa choncho tikakumana. Iye ankakonda kupitiriza kunena kuti, “kunotu ndiye ndi Kongiresi basi, ife onzathu ndoChimango basi, tambala wakuda! Ochawa songawine kuno” Tikatere tinkaseka.

M'mwezi wa July, 2004 mwana wanga atagonekedwa kuchipatala . Tsiku lina chakumadzulo ndinkakonzekera kukamuona mwanayu pamene ndinalandira telefoni yochokera kwa mchimwene wanga Richard Mapondera amene ankakhala ku Blantyre. 'Tenderetu wamwaliratu" anatero Richard, mosisima. 'Wagundidwa ndi galimoto..." anapitiriza. Ndinaponya foni pansi n'kulowa kuchipinda. Ndinalira mokweza. Thupi langa lonse linanyowa ndi chitungu cha chisoni ndi mantha. Sindinakhulupirire kuti zingatheke kuti mnzanga Tenderetu n'kumwalira. Patatha ola limodzi ndinatuluka kuchipinda n'kunyamuka kupita kuchipatala kukaona mwana wanga. Nditafika, mkazi wanga anandilandira ndichimwemwe kufuna kunditsimikizira kuti mwana anali kupeza bwino tsopano. Koma anadabwa kuona kuti misozi inali kutsika m'masaya mwanga. Anandigwira n'kundiuza kuti ndisade nkhawa mwana ali bwino ndipo amatulutsa tsiku lotsatira. Ndinamuwuza kuti Tenderetu wamwalira. Sindinathe kuwagwira mawu ndipo izi zinadabwitsa anthu ena onse m'chipatalamo chifukwa anayamba kuganiza kuti mwina mwana uja wamwalira. Tinatuluka panja.

M'mawa, Richard uja anabwera kudzanditenga pa galimoto yake kupita kumudzi. Njira yonse tinayenda mwachinunu. Titangowoloka Diamphwe tonse misozi inayamba kutsika. Galimoto isanayime nkomwe azimayi anali atayiwunjirira uku akuloza tsidya lamsewu akulira mokweza. Zinali zomvetsa chisoni. galimoto yonyamula mowa wa Chibuku imene inatenga moyo wa mbale wanga inali gada! tsidya la msewu moyang'anana ndi siwa. Mtima wanga unasweka ndipo ndinalakala nditakangoyatsa galimotoyo. Azimayi analira mokweza ngati akuti 'chonde kabwezereni ku chigalimotocho.' Titapuma tinakazungulira galimotoyo yomwe tsopano apolisi anali kuyilondola powopa mkwiyo wa anthu.

Imfa ya Tenderetu inali yomvetsa chisoni. Patsikulo, akuti chakum'mawa kunafika galimoto yogulitsa buledi kuchokera ku tawuni ku Lilongwe. Ndipo ogulitsa bulediwo sanamupeze Tenderetu ndipo anangosiya buledi n'kunena kuti ndalama adzatenga madzulo popotoloka kuchokera ku Dedza. Galimotoyo inabweradi madzulo cha m'mapasiti 6. Inamupeza Tenderetu ali m'nyumba ndipo atamva hutala iye anatuluka ndi mwana wake m'manja kukayankhulana ndi wogulitsa buledi uja. Atauzidwa mtengo wa buledi amene anasiyayo iye anabwerera m'nyumba kukatenga ndalama. Pobwerera mwana uja anamusiya ndi amayi ake. Atafika pagalimotopo anaona kuti mbali inayo yamtunda wa Lilongwe kunali kubwera galimoto yonyamula mowa wa Chibuku yomwe inali pa liwiro lalikulu komanso linali litataya mbali yake nkulunjika mbali imene inayima galimoto ya bulediyo. Ataona izi, Tenderetu anaganiza zothawira mbali inayo. Asanamalize n'kudmphira mbali inayo, chigalimoto chija chinamuvungira limodzi, kum'khwekhwereza n'kukamuponya pafupifupi pamtunda wa malipande 100 uku chigalimotocho chikunkhulira mpaka kukagudubuzika m'munda. Mdima n'kuti utagwa. Ndiye kunali kuyitana kwinaku anthu akusaka Tenderetu. Pamene Tenderetu amapezeka kumizele anali atamwalira ndipo thupi lake litanyenyeka kwambiri. Adapita n'chigalimoto Tenderetu.

Kunali namtindi wa anthu patsiku loyika maliro a Tenderetu. Anthu anapereka maumboni a moyo wa Tenderetu. A kumpingo, kusukulu, abizinesi, kuchipani komanso makasitomala. Ena odutsa pamagalimoto awo amati akamva zoti malirowo anali a Tenderetu anali kuyima kukhuza nawo ndikusiya chipepeso. Ambiri anabwera kudzakhala nawo pamwambo woyika malirowo. Mwa anthu ongodutsawo wina anapempha kuti ayankhuleko m'malo mwa anthu ena onse amene ankamudziwa Tenderetu. Iwo anali kungodutsa paulendo wawo wopita ku Lilongwe koma anayima ataona kuti pachitika zovuta. Atamva kuti womwalirayo anali Tenderetu, sanamvetse. M'kuyankhula kwawo iwo anati: “ife tatayika chifukwa cha imfa imeneyi. Ife mwana uyu ankang'unga mnzathu, sankaona kuti tachokera kuti, tavala chiyani, tili ndi chiyani, koma an'kangotilandira n'kumacheza nafe ngati akucheza ndi anzake. Timayima panyumba pakepa n'kumwa madzi, kusungitsa njinga zathu n'kumapita ulendo wa ku Lilongwe, pobwera amatilandira mwaulemu. Ndiye lero n'kumati Tenderetu wamwalira? Tatayika ife! Bakili wathu wapita, ineee! Tikapumira kuti ifeee..." ndiye panabukatu chiliro; “Bakili wathu wapita, Bakili wathu watisiya ife.”

Lero pamalo a Tenderetu ndi pabwinja pomvetsa chisoni. Mkazi wake anabwerera kwawo ndi ana ake atatu ndipo anakwatiwanso ndi mwamwuna wina. Mng'ono wake, Maseko anatsala pamlopo anagulitsa malata zitseko ndi katundu wina yense amene anasiyidwa. Naye anamwalira atamenyedwa chifukwa chakuba. Nyumba zonse zinagwa. Mlongo wake Nana anabwerera kwawo ndipo anakwatiwa. Koma ndidzakumbukira Tenderetu nthawi zonse ndipo palibe amene angafufute Tenderetu m'moyo mwanga. “Ndimakusowa mnzanga Tenderetu. Ambuye asunge mzimu wako mu mtendere.”

Monday, January 4, 2010

Easter 2009 in Dzalanyama Hills







After a heavy work schedule from January to March which saw me traveling between Zomba and Lilongwe almost every week, I decided to use Easter to relax a bit before embarking on another phase. The lake looked a familiar destination. We just wanted a new experience. We therefore decided to head to the mountains and appreciate the other side of Malawi's beauty. I grew up in the forest and mountains and thought tracing my roots wouldn't be a bad idea after all. The boys hadn't been to any thick forest or mountains save for the Liwonde National Park and Mulanje. So I convinced them that Dzalanyama would be an ideal destination but on condition that we would proceed to Mchinji where they wanted to see their granny and cousins. We set off from Zomba on Good Friday and spent a night in the Capital. In the morning we had to make some payments at the Lodge's booking office in Old Town. I discovered my spare tyre was flat and had to ensure I had it in perfect condition before we left. I knew the road we were to use would never be in good condition considering the fact the were still in the rain season. At some point I nearly changed my mind and head back to the lake. I knew the road ahead was one of the worst. But the boys' excitement and my desire to share my past with my family drove us on. So we started off from the Capital at noon after fixing the tyre and refilling the wallet. We took the Chigwiri road, through Maliri, Tanga, and KuDam (Malingunde). Memories! memories! I remembered how at the age of 14 I had to walk 18 miles from Dzalanyama to Malingunde CCAP to do Chisonyezo with my friend Manyozo. I dont know if I would be able to walk that distance again today. It was just normal then.

At Malingunde we took the Phirilanjuzi road and drove to Ndaula, then popularly known as Chimutu, after the then famous Deputy Speaker of Parliamnet and MP for the area, Chimutu Nkhoma. We turned South West to Chiputu, our former trading Centre. From Chiputu the Dzalanyama mountain range engulfed in dark green came into full view. The magnificent Mtsotsolo mountain stood imposingly above the other smaller hills. We drove on to the boundary road until we reached the GATE. A lady came to open the gate for us of course after some enquiries about our purpose of the visit. The face looked familiar to me. I later learnt that we were pupils at the Forest school in the 80s and she was now working as the gate keeper (since 1989). I recalled how she used to star on the running track in the 100 metre race. Her father was a well known Ward Counsellor.
We were 5Km away from our final destination and we drove through the thick lush and nothing seemed to have changed in the sixteen years I had been away except the condition of the road which was almost unusable. Then we came to Katete bridge. Memories memories! It was here on this bridge that friend learning how to ride a bike plunged into the fast flowing river from the bridge. We all ran away leaving him alone to take home the extensively damaged borrowed bike, which was extensively damaged! Pure childishness. I told my Onyamata we used to fish in Katete and Mkantha streams and they looked forward to fishing (we had brought with us some mbedza). We finally got to the Dzalanyama Forest Lodge and were well received by the resident staff. I couldn't wait to re-write history. Immediately we descended on to the stream running below the lodge. There is a 'swimming pool on the river. In all the days I stayed in Dzalanyama we were never allowed to swim in this swimming pool as it was for azungu only who came to the lodge. Now there we were! Azungu! So with Onyamata we partied in the cold Mkantha waters. We later fished upstream. It was so exciting.
In the afternoon we visited my old school. It was so heart breaking. No single desk no single louver on the windows from Standard 1 to 8! Imagine! What a pity! I couldn't believe this was the same school that was the envy of everyone who visited it in its prime. It was modeled on a school in the UK and attracted many tourists. In our days we partnered with Bishop Mackenzie who we considered our equals then. We walked around around and noted that the interior had been renovated and painted and that the flash toilets were operational. I later read in the Lodge's lounge that operators of thelodge had solicited funds to renovate the school and built two boarding hostels. I was delighted with this development. Later in the evening we visited some relatives we left 15 years ago. The most exciting moment came when we visited our old home of 14 years and found our old neighbour of 14 years still in the same house. We had stories to tell each other. None of their children with whom we grew up and played together were there. They were all independent now. There were more surprises to come. As we were chatting under the big tree a familiar face appeared from nowhere, smiling. I couldn't mistake him. He was my standard 3 classmate. We hugged and laughed. I later learnt that he only went up to form 2 with his studies and later picked a job with the forestry department as a Forest Guard. He was a proud father of a form 1 boy. Dziko ili. Wa ife ali Std 3! He bought me four bottles of Coke. Thanks man. We visited my cousin the following morning. She was down with malaria. We were told that she had not taken any medication as the clinic had closed down so many years ago. The nearest clinic was at Ndaula about 15 km away and could not attend to patients on a Saturday. So there she was shivering and sweating just waiting for natural healing! We were also informed the department had no car to service the staff. Worse still, the boss is now based in town, 90km away and only go there when there are important matters. We wondered how people survived under such conditions. We were informed Kabaza is the only mode of transport to the rest of the world. Zachisoni. This is a department that used to have five vehicles at one point. In those days there was a provision for a lorry to take women to the maize mill twice a week and for shopping in town or any market of their choice once a month. All this is gone. All the feeder roads were impassable! Something must be wrong. somewhere. As we left around 11 am on Sunday, I had mixed feelings about the trip. And as if to wind it up in grand style, our truck stuck in the stinking muddy waters on the boundary road. It took 2 hours and ten people to get the car out.
We made a stopover to cleanse ourselves at Diverson's place near Chipitu. Diverson was former schoolmate and had grown into a big man now and doing well. He had parked two cars in front of his his home. We noted solar panel on the roof of his house. He had plenty of tobacco too. He was following his daddy's foot steps. We were very proud of each other. He later introduced me to a woman he claimed to be his sister. I didn't recognize her instantly but later I remembered she was my classmate. She proudly told me her first born was in form four at Chiradzulu Secondary school! Wow! She gave me boiled nsawa and asked us to wait for maungu. We thanked her and Diverson for their hospitality and immediately left for Mchinji. For me it was Easter to be remembered in the years to come.

Monday, August 31, 2009

Odzukulu Power

Two weks ago I found myself in the village for the funeral of my niece's husband. I felt oblidged to attend this funeral despite the fact that the pocket was unwilling to support a trip to the Kapitolo on this date of the month. Firstly, I deeply sympathized with the niece for losing her husband of just three years. Pepa mwana wanga. Secondly, memories of their colourful village wedding are still fresh. It was one the very few weddings I have enjoyed so much in recent years. They got married in 2006 in pure village fashion with a few modifications. Remember the village weddings those days? May be these dyas too in some parts. But in those days there was no Just Married. The only means of transport to the church was a bicycle and in some cases, ngolo or wa Abraham. The ankhoswe were the ones who ferried the couple to the mission. And very often there were reports of bicycle accidents where the bride would fall off the bike and get her dress soiled in the dust! hahahaha! O their return from the church the new couple would be dropped a few hundreds meters away from the village while the ankhoswe rushed to the village to announce their arrival. The whole village would then flock to gate of the village to welcome the new family and that marked the beginning of the celebrations! Simple. No photo session, no convoys, no rings, no champaigns, nothing, but full of fun!

But the eve of the wedding was the most exciting one! That was time for boys and girls to enjoy themselves under the cover of darkness! That also marked the beginning of other marriages! But for most naughty boys that was time to pull a fast one on the unsuspecting women sleeping in the chikhuthe (a temporary grass shed). The chikhuthe is where all the foodstuffs (thobwa, luwende, nthumbwana, nkhuku etc) are stored. It also gives shelter to the women after being exposed to the scorching sun and heat from the fire place. Our women! After a day's hard work and joyous singing and dancing they retire to the chikhuthe for a short nap. And that was the time for boys to play a few tricks. They would prepare a metre long drinking stroll made from reeds. And as the women easily fell into sleep surrounded by drumfulls of freshly prepared thobwa (the main refreshment for the wedding reception), the boys, who must have done a thorough surveying in the afternoon on the positions of the mbiya za thobwa, would launch the assualt. In typical guerilla style, while others danced the night out, the boys quietly tiptoed to the back of the shed, and with great precision dipped their strolls through the loose grass into the clay pots. With utmost care and speed they drained out as much thobwa as they can while making sure noone is choked lest they wake up the women soundly sleeping inside. The women would wake in the morning only to find empty pots. Kalekale. Tikanasankha kale. I was surprized that more than twenty years on, the Tradition has continued. At my niece's wedding a few unlucky boys were caught in the act and fined.

The officiation of this wedding was done at the maginificent Nkhoma CCAP Mission. Onyamata's Bubble Shape proudly escorted the bride. No bikes this time! Driving on the Kamphata -Nkhoma road listening to Mlaka's Usakaiwale sent me back to my childhood days (kale zedi). On the far right, across a stream that runs adjacent to the road, is a foot path I once used when I was about seven or eight on one of the most memorable journeys of that time to the Mission for the third term Sunday School Closing ceremony. In those days it was always a big attraction and a feat every sunday school goer yearned to achieve. Reason? Worshiping in the big Nkhoma church lit with electricy and a piano playing in the background, with several azungus was something everyone from the distant villages longed to experience. Secondly and most importantly, the church served all the sunday school children with rice porridge at the end of the service. And this happened once a year! I am saying Rice! Think of it! It was an early Xmas for many! So we always tried to memorize verses from the Bible so we could make this Pilgrimage! And when the teacher said you were not going because you were too young to walk the 15km journey (one way) you endlessly cried knowing you would have to wait for another year to retry your luck. We all wished we were old! Finally, my day came. it was all smiles knowing I was going to sit in the big church's pew, stand before a big crowd and recite a verse and thereafter enjoy a cupful of rice pprridge. As I negotiated the turns, my eyes remained fixed on the Chilenje mountain on the right. On that July Sunday morning as we climbed up and down the Chilenje mountains bare foot, we sang Yesu chingwe chosaduka nthawi zonse always avoiding any sign of fatique lest they send you back home. We were finally in the church yard and I parked the vehicle just outside and took a stroll around the premises. Everything looked just as then.

The wedding reception was so colourful. A local band entertained the big crowd. There were also mganda and kamude (Chimtali) dancers. The women were always singing as they cooked in the big fires. I enjoyed the band so much.

And when I heard the news about the passing on of my mkamwini I remembered all these things. 2006 is just like yesterday. And today he is gone. I arrived home at 8am. The whole family was there. It was time for a reunion. a Sad one. We updated each other on our lives and ate and slept together. As food was being served around 11 am on that hot Saturday morning news came through that the grave diggers (adzukulu) had abandoned their work and were at the chiefs camp. Apparently the chief was in the company of his cunterparts from the neigbouring villages. It later transpired that a relation to the deceased had insulted the adzukulu by offering to pay them if they prepared a nice resting place for his departed relation. Where I come from you don't just joke with adzukulu or indeed about funerals! He had scratched them on a wrong spot, as we say. In pure jungle justice system, they quickly bundled and tethered the drunken fella to a tree like a goat right in the graveyard. Two more drunken brothers to the hostage appeared on the scene and rescued him. The three quickly vanished but promised to return and avenge their brother's kidnapping!

Incensed by this, the adzukulus decided to refer the issue to the village head where they demanded a 3 goat outright fine before they could return to the graveyad to continue with the work. The chiefs were somehow caught off guard and their negotiating skills eluded them for a good three hours. The adzukulus were later seen treking back to the grave, a kilometre away from kumasiye. Finally the funeral ceremony began at around 3pm during which time most people had abandoned the funeral and left for their homes. Mind you the people had been at the funeral from Thursday and this was Saturday. How would you expect them to be there for three good days when there were weddings in some neighbouring villages which they also felt oblidged to attend. But most importantly (tó them) there was also a gulewamkulu ceremony a few villages away where free beer and enteratinment was on offer which most people found more inviting than waiting for adzukulu and chiefs to agree a ransom. As we sang Kuli dziko lokoma m'mwamba with the mourners leading the procession to final resting place for my nience's husband, the singing was briefly interrupted. From the crowed of mourners appeared three young men with drunken eyes but evidently in excruciating pain. They were in their mid twenties and one of them was donning a DPP shirt. Their arms were tied at the back in the elbows with a rubber (nyakula style). The procession moved, singing Bwinoli, bwinoli tipita tidzaonana m'tsidya lija. Tears of shame and pain treked down their checks as they meandered through crowd to the end of the procession to meet the chiefs. A group of uncompromising adzukulu followed with one boy carrying a velemoti of kachasu, apparently confiscated form the unrully boys. This was to be presented to the chiefs as evidence. As I returned to the village from the graveyard I met the three unrully boys now freed and challenging to deal with the adzukulus for shaming them. I can only speculate what transpired later as I immediately started off for Zomba. Osamasewera ndodzukulu

Wednesday, December 10, 2008

Chitipa, Edeni wa ku Malawi





Pa Chichewa pali mawu akuti khotekhote ngwa njira kwaloza mtima nkomweko. Mawuwa ndimawakumbuka kwambiri panthawi imene ndili paulendo wopita kwathu ko Mbuna kapena kukaya ku Borero. Nthawi zambiri ndikaganizira mitunda imene ndimayenera kuidutsa kukafika kumene ndikupitako mphwayi ndi nkhawa zimandigwira. Koma ndikaganizira kwambiri zomwe ndikukachita komwe ndikupitako ndimakhala ndichilimbikitso. Ndikamapita ko Mbuna ndimayamba kudziwa kuti ndafika ndikayandikira pa Linthipe 1 chifukwa kaphiri ka kwathu ka Bathe kamaonekera monga adaimbira nyimbo ija. Zikangotero ndimayamba kuganizira zomwe ndikapeze ndikafika kumudziko. Ngati ndikukangowona anthu ndimayamba kuganizira za nkhuku yachikuda imene akandiphere. Koma ngati ndikupita kumaliro, tsozi limayamba kutsika.

Boma la Chitipa ndi malo amene ndakhala ndikumva mbiri yake kuchokera kwa anthu ena, pawayilesi komanso manyuzipepala. Chokhumudwitsa ndichakuti nthawi zambiri mbiriyi imakhala yosasangalatsa. Chithunzithunzi chimene chimaperekedwa ndichakuti ku Chitipa ndi kumalo kovuta kufikako chifukwa cha msewu, komanso kuti ndikotsalira chifukwa kulibe zinthu zambiri zamakono. Choncho sindinkakhala ndi chilakolako chopitako kumalowa. Koma tsiku lina mwayi udafika ndipo ndinalimba mtima kuti ndikaonako ku Chitipa.

Unali ulendo wokagwira ntchito ya kafukufuku wa ziyankhulo. Tinafika pa Karonga cham'ma 5 koloko madzulo. Titapuma pang'ono tinauyamba wa ku Chitipa. Inali nthawi yakuti mvula yangosiya kumene, m'mwezi wa April kotero kuti m'malo ena munali chinyezi. Kuyenda kwake kunali kwa pang'onopang'ono chifukwa malo ambiri anali ataonongeka. Mu galimoto yathu tinali ndi anthu awiri amene anali mbadwa za ku Chitipa ndipo anali kutisonyeza malo osiyanasiyana ndi mbiri zake panthawi yonse yaulendowu. M'njiramu tinadutsa galimoto zingapo zimene zinatchona m'matope kapena kuwonongeka kumene. Mdima unagwa koma tinali tisanayende mtunda wautali. Mantha ndi nkhawa zinayamba kutigwira makamaka poganizira kuti mwina nafe sitikanatha kukafika tsiku lomwelo. Komanso tinali ndi nkhawa kuti pofika ku Chitipa sitikapeza malo ogona. Ngakhale unali usiku timatha kuona kuti tikudutsa m'nkhalango zowirira kwambiri komanso m'mapiri. Ena anayamba kugona. Kuyenda kwa usiku ndikovuta kwambiri chifukwa suwona kumene ukupita ndi kumene ukuchokera. Patatha maola angapo tinauzidwa kuti tsopano tatuluka m'boma la Karonga ndipo talowa mu Chitipa. Nkhawa yathu inakula. Ambiri tinaganiza zongogona kuti mwina tisamve kuwawa ndi kutalika kwa ulendo.

Kenana tinauzidwa kuti tsopano tatsala pang'ono kufika. Apa panali pamphambano ya msewu wopita ku Misuku. Tinauzidwanso kuti ku Misuku ndikutali ndipo ndikovuta kupitako. Magetsi anaoneka kuwala. "Kuteroko kuli magetsi?" m'modzi wa ife anafunsa modabwa. Sitinayembekezere kuti ndi momwe anthu amakambira za ku Chitipa komanso ndi mtunda umene tinayenda munkhalango uja tingapeze magetsi. Posakhalitsa tinafika paboma. Ndi maso a usiku kunali kovuta kuti tikhale ndi chithunzithunzi chamalowo. Mwamwayi tinapeza malo ku Do or Die. Tinagona mpaka m'mawa. M'mawa ndinamwa thiyi wa masikono chifukwa anatiuza kuti Buledi kulibe. Mumtima ndinangoti tafikadi ku Chitipa. Tidya chilichonse chimene chipezeke.

Kenaka tinayamba kuyang'ana malo ena abwinoko. Ena anakhalira ku Do or Die koma ena anapeza malo Ku St Kizito ndi Ku Works Guest House. Masana a tsiku limenelo tinayamba kugwira ntchito. Tinalowera chakumpoto chakumadzulo, kwa Mwenekameme. Msewu wopita ku maloko unali wolambula bwino. M'njira monse tinatha kuona kutali ndipo tinaona sese lalikulu mpaka kukafika mumtsinje wa Songwe. Tinaonanso timapiri ta mu Tanzania ndipo tinauzidwa kuti ku Tanzania ndi pafupi. Titafika pa Kameme Trading Centre pomwenso panali Post Agency tinaona nyumba yosanjikizana imene bambo wina anamanga yekha. Inali nyumba yochititsa chidwi. Tinalowa m'nyumbayi mpaka muchipinda chapamwamba pomwe tinatha kuona kutali mpaka ku Tanzania. Tili pa Kameme pompo tinapita pamsika pomwe tinapeza chinaka (chikande). OOOOOh Ndinakumbuka masiku amenewo tikukhala ku Chongoni ku Dedza tikudya chikande. Ndiyetu kunali kulimbirana. Madzulo a tsiku limenelo nkhani inali ya ku Kameme.

Tsiku lotsatira ife tinapita kwa Mwenemwaulambiya pamene gulu lina linagwira ntchito malo ozungulira paboma. Kwa Mwenemwaulambiya ndi chakumpoto chakummawa. Pochoka ku boma mumatenga msewu wa Karonga ndikukhotera chakumpoto pa .... Choyamba kundipatsa chidwi chinali mitengo ya kanjedza imene inamera mosangalatsa m'madambo a m'derali. Titayenda tinadutsa pa... pamene panali msika. Tinagwirizana zopita kaye kwa Mwene ndipo kuti pobwera tidzayime pamsikapo ndikugula chinaka china. Nyumba ya Mwenemwaulambiya ili m'tsinde mwa phiri ndipo m'munsi mwake muli kamtsinje ndipo tsidya linalo kulinso phiri la mitengo yothithikana. Malo osangalatsa kwambiri. Titacheza ndi amfumu tinapitirira ulendo wathu mpaka pa Ifumbo (pali Post Office, koma tinapeza Police itatsekedwa). Tinayenda m'midzi yozungulira derali mpaka tinafika pa sukulu ya .... yomwe ili m'malire ndi Tanzania komanso mapiri a Misuku. Kumeneko tinacheza ndi aphunzitsi komanso ana a sukulu ndipo anthu am'derali amayankhula Cindali. Ku Kameme kuja anthu ambiri amayankhula Cinyiha. Pobwerera tinayima pa Ifumbo Police Unit ndikudya chinangwa chophika ndi mazira chomwe mmodzi mwa anzathu a ku Chitipa aja anaphika kunyumba kwa makolo ake. Titadya tinagwira ntchito m'midzi yozungulira mpaka madzulo tinafika pamsika paja pomwe tinagula chinaka, mapeyala okoma zedi, nthochi ndi zakudya zambiri. Pomalizira penipeni tinadzera kunyumba kwamnzathu wina kumene amayi ake anatizulira chinangwa. Tinali osangalala kwambiri tsiku limenelo chifukwa tinaona mtima wowolowa manja wa anthu a ku Chitipa. Komanso tinamva zinenero zosiyanasiyana: Cinyiha, Cilambya, Cinamwanga, Cindali, Cibemba ndi zina.

Tsiku lotsatira tinalowera mtunda wa ku Wenya makamaka ku Chinsenga, Malawa Ibughulira ndi malo ena. Ibugulira ali pafupi ndi malire a dziko la Malawi ndi Zambia msewu umene inkadutsa basi ya Nakonde yodzera mu Nyika. Kumeneko amayankhula Cinyika chomwe chimafananako ndi Cinyiha cha ku Kameme koma kusiyana kwake ndikwakuti Cinyika chimasakaniranapo ndi Citumbuka.

Titafika pa Malawa sukulu tinapita kunyumba kwa amfumu yomwe inali mtsindetsinde mwa mapiri a Mafinga. Mafinga ndi mapiri okongola kolapitsa. Awa ndi mapiri amene kumachokera madzi amene anthu a m'boma la Chitipa amamwa, madzi ozizira kwambiri. Tinayenda m'midzi yambiri komwe tinapeza madzi a m'mipope, zinthu zomwe sitinkayembekezera kuzipeza ku Chitipa. Tinamwa madzi apampopi m'mudzi mwa Malawa. Tikucheza ndi anthu m'mudziwu kunabwera mvula yamatalala. Tinadzizdimuka kwambiri popeza tinkaganiza kuti mvula inali itasiya. Titayenda mobwerera tinafika pa Chinsenga, malo okongola kwambiri. Nditapatsidwa mwayi wosankhanso kwathu, ndingathe kusankha ku Chinsenga. Chinsenga ndi malo amene ali m'munsi mwa phiri la Mafinga, nyengo yake ndi yozizira, nthaka ndi yachonde ndipo pali mitengo yabwino zedi. Palinso Police ndi tchalitchi zokongola. Pamenepa ndi pamene pali mphambano yopita ku Wenya ndi Nthalire. Chosangalatsa kwambiri ndi malowa ndichakuti ndi malo amene pali anthu oyankhula Cinyika ndi Citumbuka motero kuti kayankhulidwe kake kamakhala kosakaniza ziyankhulo ziwirizi. Pachifukwachi anthuwa akuti amayankhula Citumbunyika. Sindinafune kuchoka malo amenewa ndipo pobwerera tinayima mumsewu ndikumangosirira mapiri a Mafinga. Chilengedwe chokoma!


Madzulo a tsiku limenelo kunali kukambirana za malo amene tikagwire ntchito tsiku lotsatira. Panali malo awiri: Misuku ndi Nthalire. Tinauzidwa kuti malo onsewo anali ovuta kufikako komanso malo ogona ndi ovuta. Tinauzidwanso kuti sitikanatha kupita ku Misuku ndi ku Nthalire ndikubwerako tsiku lomwelo chifukwa konseko ndikutali kuchokera paboma. Tinayenera kukagona komweko. Ine ndinasankha kupita ku Misuku. Tinauzidwa kuti kulibe network choncho sitidzatha kuyankhula ndi anzathu panthawi yonse tidzakhale kumeneko. Tinanyamuka masana a tsiku limenelo wa ku Misuku anzathu ena wa ku Nthalire. Gulu lina linatsala paboma. Tinafika pamtsinje wina. Tinaima ndikusukusula m'maso. Kenako tinayamba kukwera mapiri a Misuku ndikudutsa munkhalango zokongola. Tinadutsa malo ambiri ochititsa chidwi. Pena tinali kutsika galimoto ndikumangowona chilengedwe chokongola: Mitengo, mapiri, zigwa, mitsinje. Tinaima pa Kawotola pamene tinachezapo ndi anthu ena. Iwowa amayankhula Cisukwa. Tinaona ng'ombe zomangirira mabelu zikudziyendera m'thengo. Kenaka tinafika m'minda ya khofi yomwe inaoneka mochititsa chidwi kwambiri. Titayenda tnaima pa nkhalango ya Wiringi (nkhalango yowirira kwambiri(rainforest)). Tinalowa m'nkhalangoyi kukatchola zipatso za Mafwisa. Ooooh! Ngati tisatuluke mnkhalangoyi. Kenaka tinayamba kutsetserekera m'Misuku! Zoti ndi Malawi yemweyu simungakhulupirire, malo ochititsa chidwi. Kunali kukwera, kutsika, kukwera kutsika. Tinafika ku nyumba yogona alendo ya Coffee Growers Association kumene tinapeza malo okongola kwambiri ogona. Madzi otenthetsa pamagetsi analipo. Ena anagona kumahostel a pamalopa. Chakumadzulo tinasewera mpira wokulunga ndikukasamba. Madzulo tinapita kunyumba ya mayi ndi bambo ena amene anatiphikira chakudya chifukwa kunalibe malo odyera. Tinapanga ubale ndi banjali kotero kuti pa masiku atatu amene tinakhala ku Misuku tinali kudya kunyumbako.

M'mawa tinapita ku Nyumba kwa Mwenemisuku, kutsetserekera chakumadzulo. A Mwene anali onyadira kuti tinafika kudera kwawo ndipo anatiuza kuti dera lawo limalandira alendo ambiri ochokera kunja chifukwa chakukongola kwa malowa. Pochoka tinalandira vibwaira va nthochi, chinangwa, nzimbe, mtedza ndi zakudya zosiyanasiyana. Koma kufika m'makomo chinali chovuta kwambiri chifukwa nyumba zili m'tsidya kotero kuti kufika kumeneko umayenera kutsetsereka ndikukwera mitunda. Koma pakutha pa masiku atatu tinali titazolowera kuyenda mothamanga komanso mowerama. Ku Misuku tinapeza kuti anthu amayankhula Cisukwa komanso Cindali. Tinapezanso nkhalango zowirira kwambiri ku Chinongo. Pobwerera tinaganiza zodzera njira zina zachidule zokatulukira ku mtunda kwa boma la Karonga. Ndiyetu kunali kutsetsereka kwambiri popeza tinali kupita kumalo otsika kunyanja. Unali msewu umene sikudutsa galimoto zambiri moti pena timaona ngati tasokera. Pamasiku onse tinali ku Misuku sitinayankhulane ndi wina aliyense pa foni chifukwa kunalibe network. Koma tinakhala mosangalala chifukwa zinthu zinali zotsika mtengo. Titayenda maola angapo tinafika pa Ngerenge m'dera la Kilupula ku Karonga. Tinangowona nyanja ili mbee. Tinasangalala kuti tafika kumene tidzatha kuyankhulana ndi kuonana ndi anzathu amene tinasiyana nawo masiku anayi apitawo. Podutsa ku Ngerenge tinaona ng'ombe ya miyendo itatu itamangiriridwa m'mabli mwa msewu.

Kunali chimwemwe chokhachokha pamene tinakumana pa Karonga. Tinauzana momwe tonse tinayendera komwe tinapita. Kunaoneka kuti aliyense anali wokondwa kwambiri. Kuchokera tsiku limenelo tinapeza chithunzithunzi chenicheni cha boma la Chitipa. Ndi boma limene chilengedwe chake sichinaonongoke, dziko lokongola, anthu ansangala ndi owolowa manja. Kuchokera pa nthawi imeneyo ndapitanso kuchitpa katatu ndipo ulendo uliwonse ndimabwera ndichimwemwe. Chitipa, Edeni wa Malawi