Wednesday, February 6, 2013

Madala: Mphawi Wachimwemwe

Kodi ndi chiyani chimakupatsani chimwemwe m'moyo mwanu? Chuma? Ntchito? Mkazi? Mwamuna? Maphunziro? Nzeru? Anzanu? Chiyani? Aliyense ali ndi chinthu chake chimene chimamupatsa chimwemwe komanso chimene amadana nacho kwambiri. Ena akapata ndalama sasowa, amafuna aliyense amupatse moni ndipo adziwe kuti zinthu zikuyenda. Anthu otere akapsa m'thumba ndi nkhope yomwe imakhala ya makwingwirima. Ndalama zimabweretsa anansi. Zikatha, anansinso amathawa. Komanso nthawi zina ndalama zimabweretsa adani. Kunja kunotu kuli kaduka kapena nkhwidzi. Wina asakwete, walakwa, avala ufiti kapena umbava. "Akusolola" timatero! Moyo wa masiku ano ndi wovuta, popanda ndalama, dziko limayima, ulemu umatha. Angakulemekeze ndani ulibe makobidi? Umasanduka chitselekwete! Koma bwanji ukangosanja? "Yes wamkulu, Zoona abwana, eetu achikulire, shuwatu big" mayina mbwee chifukwa cha ndalama. Koma kodi munthu angakhale wosangalala popanda ndalama? Enafe tidakulira m'mavuto oposa a Majoti. Nkhani ya Majoti ndi yopeka koma yathu ndiyolula ndithu! Mutha kukamba za mavuto amtundu uliwonse amene munthu padziko lapansi pano amakumana nawo. Tadutsamo. Tatulukamo. Mukamationa kusalalaku sikuti tidakulira ku Nyambadwe! Ngakhale kwa Ntopwa kumene sikungayandikireko! Koma chinsinsi cha Mulungu amachidziwa ndani? Thupili sikuti ndi chambiko chalerochi. Ndilobadwa nalo. Takula nalo. M'mavuto omwewo. Koma chinthu chimodzi chimene ndidakula nacho ndicho kupeza chimwemwe m'mavuto! Simkuluwiko! Umphawi supha munthu! adatero madala! adalasa penipeni. Bwenzitu enafe titatsogola. Malemu Opapa (madala mzimu wanu uwuse mu mtendere), ndiye chitsanzo chabwino cha munthu wosangalala pamavuto, pamtendere. Simisala. Koma kusalitsanza dziko. Kwa anthu amene amatidziwa bwino kubanja kwathu, kuseka sitiumira, ndichizolowezi. Kodi ndimayesa kuseka ndiulele, sochita kugula! Ndikumbuka masiku amenewo tikukula, titadya mgawiwa wamadzulo opapa ndi omama otafatsa kutilakatulira nthano za pa ubwana wawo, za ku sukulu, za ku Joni.. ife tikuseka chikhakhali. Uku ndiko kudali kukhala kwawo, kukula kwathu. Kuseka sikunkalira ndalama. Osati kuseka kwa masiku ano kopemphera khobidi! Lero ndapukwa opapa: Richman Bwanali Kadango kwawo ku Chitundu kwa Che Tambala m'mudzi mwa a Chawala. Myawo wapaphata kukakwatira mchewa wa ko Mbuna ku Mpenu ko Mazengera ndikusiya Chisilamu n'kuyamba kudya kapado, mbewa, kupapira masese nkukathera mu Utimiki wa Dutch! Nthawi zina makolo akamapereka mayina kapena tikamadzipatsa mayina kaya chimakhala chiyani. Inetu bambo anga pobadwa anapatsidwa dzina loti Che Madayika. Koma atakula andziwika ndi dzina loti Richman! Kaya anali matemberero kaya. Anafa osauka. Koma wosangalala, wonjoya. Bambo anga atasiya sukulu anapita ku Joweni kukasewenza ku mgodi. Pobwera kumeneko ndipamene ankabwera ko Mbuna kenako nkukayamba ntchito ku Chongoni, ku nkhalango, ife nkumabadwa. M'banja mwathu tilipo ana asanu ndi anayi, onyamata osanu ndi mmodzi ndi otsikana otatu. Tonse tilipo. Anaigwiratu makolo. Koma sizinali zachibwana kusamalira mbumba yonseyi. Madala anali munthu wolimbikira ndi wogwiragwira. Kaya ntchito zinazi anazidziwa bwanji kaya? Kaya inali mphamvu ya uchawa kaya? Komatu ankatha chilichonse: kusoka, kusema, kuluka, kukhoma! Chilichonse chochita ndi manja. Mgaiwa ukapezeka magwero ake anali amenewa. Tikavala nkhani yake inali yomweyo. Luso lina tinaphunzirako - koma izi n'zatsiku lina. Analipo masiku owawitsa ndithu nthawi imeneyo. Kudikira madala kuti abweretse chimanga kapena ufa mpaka pakati pa usiku, tulo titachita chipongozi, nkhani zitatha, m'mimba mukubangula. Akafika munthu wamwamuna khosi litalowa mkati ndi chibinyira, kusaukira mbumba nkumati adandaula, ayi ndithu! Ayambepo kukuyalirani nthano za zimene waziona tsikulo, inu njala yonse kutha nkuseka! M'mawa sikuti agonereza ayi, buli wa kuntchito! Akasakenso. masiku n'kumapita, ana nkumakula. Madala anali ndi anzawo ankhaniankhani! Akakhala pagulu, kwawo kunali kuseka ndi kuseketsa. N'kuti kulibe anzawo? Sianzawo a ku Mchinji aja adakonzetsa thupi lawo kuti lisaonongeke pa 20 July paja? Sitinalandire ulemu ndi mphatso kwa anzawo chifukwa cha kucheza kwawo? "Atate wanu nanzanga zedi, timacheza zedi anga munthu ni mphwake" ankaterotu anzawo. Ukapita kukawayendera ku Mchinji uko adasamukira atapuma pantchito amakuyendetsa benchi iliyonse mumsika kukuonetsa kwa anzawo, "mwana wanga wa ku Zomba uja ndi ameneyu". Palibe chimene chinkawasangalatsa madala koposa kunyadira ana awo. Kodi sitinapeze malo chifukwa cha anzawo? Kodi lero ku Mchinji sikwathu chifukwa cha anzawo? Kodi lero kuti tipite ku Chongoni, kwa Kankhomba, kwa Chiphazi, ku Mpalale, kwa Ndemela, kwa Nthenda sakatilandira? Suja adatikankhira galimoto ulele titatitimira ku Dzalanyama kuja atangodziwa kuti uyu ndi mwana wa Angozo (mifunda ndiye inalipo yankhaninkhani koma munthu anali mchawa)? Lero ndikamaganizira za moyo wa bambo anga chimene ndimalingalira kwambiri ndikukhala wokondwa nthawi zonse mavuto angakule maka! Chachikulu bola uli ndi moyo ndipo moyo ndi waulele. Ukadakhala wogula bwenzi ife kulibe. Chimwemwe chili mumtimamu! Umphawi supha munthu. Ngati uli ndi moyo, manja ndi miyendo uli nazo yamika Namalenga, gwira ntchito upeze chakudya lero, usakwiyire ena ngati andiwo adakulodza. Usani mumtendere opapa. Munatiphunzitsa zazikulu!

Tuesday, January 8, 2013

Tachilowa nawo

Masiku atheradi kuchitseko. Anga bodza kuti tagonera. Ndife sundwe. 2012 tatseka tione kuti 2013 wafungatanji? Koma tisanathe mtunda mu 2013 tiyang'aneko kumbuyo. Chilumika chimenechi chinali ndi zake zosayiwalika. Pali zinthu zingapo zimene zidzandikumbutsa za chaka cha 2012, zabwino ndi zoipa zomwe. Paja amati zimakhala bwino kuyambira zabwino. Kabaza M'mwezi wa February ndinagula njinga yanga ku 5 Miles - AfriCycle. Ndiyamika Nijo mnyamata amene anandisankhira njinga imeneyi. Maso kunyoza. Atandilozera njinga imeneyi ndinkaona ngati wandisankhira chikhokhololo! Koma ayi ndithu Nijo anandisankhira Mlalu weniweni! Mlalu wanga wandionetsa malo m'chaka chimenechi. Mwa malo amene ndidzawakumbikire chifukwa cha mlaluwu ndi Mwandama (kuja kunakafika Mlembi wa Bungwe la Mgwirizano wa Mayiko onse a Ban Ki- Moon, ku Zomba kuno, mudzi wa Kansonga m'chigwa cha pakati pa mapiri a Zomba ndi Malosa - malo okongola kwambiri mudzi umene ukudyetsa tawuni ya Zomba ndi zipatso, komanso ku Phalombe. Mlaluwu wandionetsa Chingale, Mayaka, Ulumba ndi malo ambiri mu Zomba muno. Imfa ya Bingu 2012 chinali chaka chosautsa kudziko lathu lino. Nthawi zina ukamaona momwe atsogoleri athu amatumbwira akakhala pampando maganizo amayamba kubwera kuti mwina n'takhala ine zimenezi zingathe. Koma zikuoneka kuti aliyense akakhala pachimpando chimenechi amaona ngati iye ndiye namalenga wa tonsefe. Komatu kumwambako Chisumphi alipo ndithu ndipo dongosolo lake palibe angalimvetse ngakhale amene mukuyti ndi aneneri olulawa! Iye ndi tsidya lina. Chili kuti lero chitsulo cha njanji? Mwina chidakathera pachipala! Achinyenyanyenya? Amayi samalani. Kuno ndi kunja kudayanja lichero! Richard (uwuse mu mtendere mzimu wako) M'bele la amayi wanga munabadwa akazi awiri, Omama ndi Omayi. Mukafuna kudziwa za mayina amenewa pitani kwathu ko Mbuna mukafunse. Akakuwuzani kuti Omama ndi Omayi ndani. Richard anali womaliza kubadwa m'nyumba moMayi. Ndi ine tinangosiyana zaka zochepa kwambiri pobadwa. Tinakulira ndi kusewera limodzi makamaka pamene tonse makolo athu ankagwira ntchito ku Ngoma (Nkhalango ya Chongoni). Atatsiriza maphunziro ku Kongwe analowa ntchito ya polisi ndipo anakwera pamaudindo mpaka kufika pa Superintendent. Koma m'mwezi wa August, Richard anatisiya kuchipatala cha Nkhoma, kwathu. Komatu dzikoli ndilovutadi kulimvetsa. Zambiri ndidzakambabe koma pano tizingopemphera kuti Mulungu asamalire ana ake, Anne, King, Tiya, Shireen ndi Yankho komanso mayi awo. Yaounde Chakachi ndinachitsendera ndi ulendo wa ku Cameroon ku msonkhano wokambirana za ziyankhulo za mu Africa makamaka pa ntchito yochita kalondolondo wa chiwerengero cha ziyankhulozi, chiwerengero cha anthu oziyankhula ndi malo amene zikuyankhulidwa mu Africa muno. Unali ulendo wosangalatsa kwa ine chifukwa chakuti kanali koyamba kupita dziko limene anthu ambiri amayankhula Chifaransa mu Africa muno. Inetu Chifaransa ndinachiphunzirapo kalekale ndili mu fomu 1 ku Mtendere zaka zimenezo. Pierre et Seydou woloweza yemwe uja anatipulumutsa mpaka ife kuoneka dolo madoda oyankhula Chingerezi chokha akulephera kunena chakudya chimene akufuna kudya mu resitilanti! Sindikunena munthu ine! Koma zinali zosangalatsa kwambiri. Pamene imatha sabata ayi ndithu ife tinali titalolera Chifalansa chokwanira kufunsira (njira). 2013 wolowa chiyimirire Ngati ndikulemba lero pa 8 Januwale ndiye kuti ndalowa nawo. Koma sindinachiyambe bwino kwenikweni. Kaya ndi Namalenga kaya ndi Dyabu kaya koma ndinapezwa ndithu munthune. Pa 31 tinapita kwa anzathu kuti tikachilowere limodzi. Ndiyetu kunali kutafuna ndikukhwasula. Dansi inathyoledwa mosaona kuti apa pali mwana wanga kapena apa pali obaba ndi omama. Tangoganizani mabanja awiri ndi ana awo onse aliyense akuthyola sitepe! Panavutatu. M'mene imati 2kaloko m'mawa woyamba wa 2013 tinanyamuka wa kunyumba. Komatu chongoti lowu, pakama thasa, inu! Namo m'mimba dzambatuku! Poyerayeratu! Kuyesa kutembenukira uku, kapena uku, kapena chafufumimba, pola, nikisi! Madzi akumwa kapena? - ndiye kukolezera! Kuyesa kukanyonyomala pamtondo, kuti mwina mpweya wokha, ayi tele kuli zii! Tetetete! Kokoliko! Ukutu nkuti mnzanga wapamphasa akungouliza wa mtendere uja! Ndipite kuchipatala? Ndi adiimiti kale! Nanga zoona kuchipatalako buku tikachite kulitsekulitsa pa 1 januwale? Ndiyetu kunali gubidigubidi kuwunguza mtela. Wapezeka panadolo. Mpwintheni! Kuyesa kugona, ayi tele, tazemberatu tulo. 6 Koloko kwacha, wa kuchanjausi kukadzithira madzi kuti mwina kapena. M'mene imati 7:30 ndafika pakhomo la chipatala. Chikwangwani chikuti lero latchuthi amatsekula 8:30! Mtsonyo wakewo! Kubwerera kunyumba, mnzanga wadzuka akujijirika ndi zanyuwele! Mpamene ndimaulula kuti bwanawe mnzakone sindidatinyanthe tanyuweletu! Anangoti kukamwa yasa! Ndiyetu masana onse kunali kuliza mkonono! Koma ayi lero suyu tikupumayu! Koma wachewuchewu! Talowa ndithu ndipo tiyamika Lezayo kuti watikondera, Chichewa cha lero! Ticheza m'chaka chimenechi!

Thursday, July 19, 2012

July 20, 2011: Tsiku Losayiwalika m'Moyo Mwanga

Kulemba nkhani sichinthu chapafupi! Nthawi zina mtima umakhala ukufuna koma thupi limakhala lolefuka, nthawi imakhala yochepa, zosokoneza zimakhala zambiri. Nanji masiku ano a facebook, twitter, nyasatimes ndonzawo wokhala pansi n'kulemba nkhani kapena ndakatulo ndi munthu. ndimalakalaka ndithu nditamalemba pafupi[afupi ndipo nkhani ndi zambiri m'mutumu koma danga lochitira zimenezi ndilo lisowa ndithu. Choncho tsamba lino lakhala lili mbe chifukwa chotangwanika ndi zina ndi zina. Zina zaphindu, zina zopanda mpake pomwe. Chatsitsa dzaye ndi malingaliro amene ndakhala nawo sabata imeneyi. Kwa ine ndi onse a kubanja kwathu sabata ino chaka chatha (2011) inali nthawi yowawitsa chifukwa bambo athu anali ali m'chipatala. Mwezi wa June chaka chatha ndinapita ku Mchinji kukaona abambo anga nditamva kuti sanali kupeza bwino. Pobwerera ku Zomba chiyembekezeo ndinali nacho kuti adzapeza bwino. Patapita sabata zingapo, m'mawa wa pa 18 July ndinalandira lamya kuti madala agonekedwa m'chipatala. Mantha anandigwira chifukwa aka kanali koyamba m'moyo mwanga komanso mwa madala kugonekedwa m'chipatala. Kutacha ndinanyamuka wa ku Mchinji. Nditafika kuchipatala madala anauzidwa kuti ndafika ndipo anandiyang'ana. Ndinawayandikira kuti ndithe kuwafunsa momwe akumvera m'thupi mwawo, ndinaona pamaso pawo chilakolako chofuna kundiyankhula koma ndinadziwa kuti thupi linali lofowoka. Sindidziwa kuti madala anafuna kundiuza chiyani! Ndinawagwira dzanja koma sanasonyeze kuti ndawagwira! patapita mphindi pang'ono ndinachoka n'kukhala pambali n'kulonjerana ndi amayi komanso abambo aang'ono amene anali kudwazika matendawo. Anandipatsa uthenga wachilimbikitso koma sichinakwanire. Madala akadandiyankhula mwina ndikadalimba mtima kuti akupeza bwino. Usiku ndinapita kunyumba kukagona mtima uli wosweka ndithu. Unali usiku wautali. M'mawa kutacha pa 19 ndinapita kukawazonda. Sindinaopne kusintha kwenikweni. Mantha anandigwira ndipo ndinadziwa kuti madala sadzandiyankhulanso. Usiku wa pa 19 unandisautsa kwambiri. Sindinagone. M'mawa pa 20 July. Kutacha m'mawa ndinamva mauthenga akuti dziko la Malawi lili pamoto. Anthu anali kuchita zipolowe zosonyeza kukwiya ndi ulamuliro wa dziko lino. Mkazi wanga anali ali ku Mzuzu ndipo anandiuza kuti wakwera basi m'mawa koma akulephera kutuluka mumzindawu chifukwa cha mfuti zimene zinali kulira. Nkhawa inandigwira. Ndinamvanso kuti ku Lilongwe, ku Blantyre ndi maboma ena zinthu sizinali bwino. M'tawuni ya Mchinji munali bata ngakhale kuti m'misewu munali apolisi ochuluka kuposa nthawi zonse. 12 Koloko Masana Nthawi yowonera odwala itakwana cham'ma 12 ndinanyamuka kuti ndikazonde madala. nditatsala pang'opno ndinamva foni ya amayi kundiuza kuti ndifulumire. Mtima wanga unagunda, thupi linachite tsembwe! chongofika m'chipinda momwe munagona madala nkhope ya amayi inandiuza zonse. "Aliki bambo ako ulendo uwu"! Inali nthawi yowawitsa m'moyo mwanga! Ndinayandikira ndikuwagwedweza madala koma sanasunthe ngakhale pang'ono! Apita madala! Tsopano chaka chaka chatha. Madala anagona ku Mchinji mwakufuna kwawo. Sanafune kubwerera kwawo ku Chitundu ku Dedza. Ku Mchinji anasamukirako 1995 atapuma pantchito. Ku Mchinji kuanasanduka kumudzi kwawo, kumudzi kwathu. Anali ndi abale andi abwenzi ambiri. Onse anachitira umboni patsiku lowasunga madala pamene anafika mu unyinji wawo. Kufika kwa unyinji umenewu kunandikumbutsa ndipo kudzapitiriza kundikumbutsa moyo wa madala - kuseka ndi aliyense! Madala anali munthu wokondwa nthawi zonse ndipo ndiyamika Mulungu chifukwa cha mphatso imeneyi. Akanakhala wopanda mphatso imeneyi mwina bwenzi pano tikukamba nkhani ina. Ndi chikhumbokhumbo changa kuti ndikumbukire moyo wa bambo anga pofotokoza zina zimene zinawathandiza kukhala moyo wosangalala ngakhale atakumana ndi mavuto amtundu wanji pamoyo wawo. Tinakhalapo moyo wovutika kuthupi koma mu mtima mokha tinali anthu osangalala, achimwemwe nthawi zonse chifukwa cha madala. Mzimu wanu uziusa mumtendere Madala ndipo ngati kumene muliko ngati n'kotheka kuchita nthabwala nkumaseka, pitirizani mpaka tidzaonanenso nkusekera limodzi!

Thursday, June 9, 2011

TABWERANSO

Pepani kwambiri abale amene mwakhala mukutsatira tsamba lino kuti tinakhala ngati tati zii, osalemba kalikonse. Tinachita kuyiwala chizimba cholowera bwalo lino. Koma ndifuna kukulonjezani kuti tsopano bwalo lino talitsekulanso ndipo pakhala pakukambidwa nkhani zambiri. Masiku apitawa tinayenda kwambiri ndipo pali nkhani zosangalatsa zofunika kugawana. Ingopitirizani kuwerenga ndikupereka ndemanga. Tilandireni

Monday, July 19, 2010

Mwana wanzeru akondweretsa makolo




Kutsiriza maphunziro ndicho chinthu chimodzi chopambana m'moyo wa munthu. Iyi ndi nthawi imene munthu amatsiriza osangoti maphunziro okhawo ayi, komanso gawo la moyo limene wakhalamo nthawi yaitali ndithu. Komanso ndi nthawi imene munthu amayembekezera kuyamba moyo watsopano. Iyi imakhalanso nthawi yodziwunika ndikudzisanthula pamene unachita bwino komanso pamene sunachite bwino kuti mwina m'moyo wina umene ukukawuyambawo ukachite mosiyana ndi m'mbuyomo. Komanso imakhala nthawi yolingalira za moyo watsopano uli nkudza. Pachifukwachi ena amakhala ndichimwemwe poganizira kuti mwina tsopano asiyana ndi moyo wovuta ndipo akukayamba moyo watsopano. Koma ena amakhalanso ndi nkhawa kuti mwina akukayamba moyo wovuta kusiyana ndi wam'mbuyomu.

Ndikumbuka kuti pamene ine ndinali kutsiriza moyo wa ku sekondale, ndinali ndi chimwemwe kuti tsopano sindidzasambanso madzi ozizira m'mawa ndipo ndizidzadzuka nthawi imene ndikufuna. Panthawiyi ndinaona kuti tsopano ndapeza ufulu wochuluka ndipo moyo wa ku sukulu ndinawuona ngati ukapolo. Komabe ngakhale izi zinali chomwechi, ndinalibe ndi nkhawa pa za moyo wam'tsogolo. Choyamba chinali chakuti kodi mayeso ndikhoza? Nanga ndikhoza bwanji? Ngati sindikhoza bwino, ndidzachita chiyani? Kodi ndidzapeza mwayi wa ntchito? Idzakhala ntchito yanji? Ndizidzalandira ndalama zingati? Nanga ngati ndikhoza bwino, ndidzasankhidwa kupita ku Yunivesite? Kodi ndikasankhidwa kupita ku Yunivesite ndikachita maphunziro anji, nanga adzandipatse malipiro a sukulu ndani? Kodi ndikakhoza n'kudzapeza ntchito yapamwamba? Ndikhukupirirra awa ndi ena mwa mafunso amene achinyamata amene akukonzekera kutsiriza maphunziro awo nthawi ino akulimbana ndi kupeza mayankho ake.

Dzana Loweluka pa 17 July linali tsiku lotsanzikana ndi ophunzira a Fomu 4 pasukulu ya Mlanda ku Ntcheu. Tinayitanidwa ndi mwana wathu Priscilla kuti tikhale nawo pamwambowu. Sitinachione chofunikira kuti tichoke ku Zomba kukafika ku Ntcheu chifukwa cha mwambo umenewu chifukwa panthawi yathu makolo sankaitanidwa ku mwambo wamtunduwu. Komansotu panthawiyi ophunzirawa amakhala asanalembe mayeso awo ndipo sakudziwa ngati adzakhoze kapena ayi. Koma mwanayu anachonderera ndithu kuti ife tipite ndithu tikaonelere mwambowu.

Ndinanyamuka ku Zomba cham'ma 8 koloko m'mawa pamodzi ndi Onyamata ndipo tinafika ku Mlanda cham'mapasiti 10. Titangofika Priscilla anatithamangira akusekerea kudzatilonjera. Apatu n'kuti akukonzekera kulowa mu Holo imene mumachitikira mwambowu. Kenaka mtsikana wina anabwera kudzatitenga n'kutilowetsa muholomo. Kunabweratu makolo ambiri komanso anthu oyimira magulu osiyanasiyana monga mafumu (a T/A Masasa anali kumeneko), a mpingo komanso abizinesi. Mwambo wake unali wosangalatsa kwambiri. Kunali magule, kuyimba, masewero ndi zochitikachita zambiri. Alendo onse pamodzi ndi ophunzira analandira chakudya ndipo chinthu chosangalatsa makolo kudyera limodzi ndi ana awo kusukulu.


Ine ndinasangalala koposa kuona kuti mwana wathu anali mmodzi wochita nawo masewero. Mwana wathu ndi wofatsa kwambiri moti sitinkayembekezera kuti angathe kuyima pagulu la anthu n'kukamba zomveka. Koma ayi ndithu patsikuli iye anali kuchita gawo lowulutsa mawu kunyumba ya mphepo ya Zodiak! Ndinakondwera kwambiri. Koma nthawi yopambana kwambiri imene ine ngati kholo sindidzayiwala chifukwa ndinazizwa kwambiri inali pamene anali kupereka masatiketi kwa ana amene anachita zinthu zopambana panthawi imene anali pasukulupa. Masitifiketi oyamba anaperekedwa kwa mwana aliyense amene anali kutsiriza maphunziro ake pa sukulupa. Koma gulu lachiwiri la masatifiketiwa linali operekedwa kwa okhawo amene anachita bwino kuposa anzawo mu gawo lina lake monga pa phunziro lililonse, mavalidwe, mayimbidwe, ndi zina. Zinali zoseketsa ndizosangalatsa kumva kuti wina anasankhidwa kukhala wolawirira pochita china chilichonse, komanso wina anasankhidwa kukhala munthu wokonda kulangiza anzake. Panalinso mwana wina amene anasankhidwa kuti amakonda kumwetulira ndi kusekerera nthawi zonse. Mwana ameneyu ndi wachimwemwe ndipo kwake nkuseka basi. Mayi ake ndimawadziwa ngatinso munthu wokonda kuseka ndikuseketsa moti sindidadabwe nditamva kuti anasankhidwa kukhala munthu womwetulira nthawi zonse. Panalinso kamtsikana kamene kanasankhidwa munthu wodziwa kuyimba. Mwana ali ndi nthetemya uyo. Atalandira satifiketi yake anapemphedwa kuti angotilawitsako pang'ono luso lake. Holo yonse inamumbera m'manja mwanayu atangoyimba ndime imodzi yokha.

Tsopano olengeza mayina anali kufika kumapeto wa mndandanda ndipo ine ndinali kuganiza zonyamuka poganiza kuti mwambo wopereka masatifiketi tsopano watha. Kenaka ndinangomva kuti “wophunzira amene anachita bwino kuposa onse mu phunziro la Chingerezi, Priscilla Chimtolo.” Ine mtimawu unangoti myuuuu! Ndinadzidzimuka koposa ndipo sindinakhulupirire. Nditacheukira pamene anakhala Priscilla ndinangoona kamwana kanga kakubwera kali mwee kudzandikupatira. Ndinali ndi chimwemwe chodzadza tsaya. Ndinali ngati ndikulota. Ndinaonanso kuti naye ali wosangalala kwambiri kuti anapata mphoto imeneyi komanso chifukwa chakuti ine ndinafika kudzachitira umboni mwambo umenewu. Pamene ndimanyamuka ndinali munthu wosangalala ndipo njira yonse ndinayenda ndi chimwemwe chokhachokha. Ndili ndi chikhulupiriro kuti zimenezi zimuthadiza Priscilla komanso ana ena onse amene anachita bwino kuti alimbikire kuti pamayeso awo otsiriza adzachitenso chimodzimodzi. Mwana wanzeru akondweretsa makolo.

Wednesday, July 14, 2010

Mnzanga, Happy Wapita

Dzulo madzulo nditaweluka kuntchito monga mwachizolowezi ndinapita kokachita masewero olimbitsa thupi. Ndinabwerako cha m'ma7koloko usiku. Nditafika kunyumba ndinanyamula chisusu changa kuti ndikadzithire madzi kuchotsa chitungu. Polowa kuchipinda chogona ndinasangalala koposa chifukwa ndinapeza a Nyagondwe akundisitila zovala. Nditangolowa kubafa ndinamva kuyitana kuchokera kwa mayi. Ndinatuluka kuti ndikamve kuyitanako.

"Kodi paja Happy dzina la abambo ake ndani? anandifunsa nditangosuzumira pakhomo la kuchipindako. "Nyirenda?" Anapitiriza kufunsa ndisanayankhe funso loyamba lija.

"Ee, bwanji?" ndinafunsa ndi chidwi.
"Wamwalira, akulengeza pa wayilesi kuti Happy Chokoma Nyirenda wa ku Nkhatabay amene amadwala kuchipatala cha Zomba wamwalira."

"Hiii Happy inu. Mpaka wamwalira ndi mutu womwe uja" Ndinasendera ndikukakhala pa bedi kuti mtima ukhazikike.

Happy anali mnzanga ndipo tinadziwana m'chaka cha 2003 kuno ku Zomba. Tinadziwana chifukwa cha mnzanga wina Jonah Mphanda amene ine ndinaphunzira maye ku sekondale ku Mtendere. Panthawiyo Jonah ndi Happy ankagwira ntchito ku Interaide. Kenaka awiriwa anasiya ntchito ku Interaide ndipo Happy anayamba kugwira ntchito ku Spar.

Sabata zitatu zapitazo, Jonah anandiyimbira foni kundifotokozera kuti Happy wagonekedwa kuchipatala ndipo akudandaula mutu. Tsiku lomwelo ndinapita kukamuona ndipo tinacheza nandifotokozera kuti mutu ndi umene ukumusautsa koposa. Ndakhala ndikukamuona koma zimaoneka kuti matendawa sanasinthe mpaka pamene dzulo chakum'mawa amamwalira.

Happy amachokera ku Nkhatabay. Ndidzamukumbukira Happy chifukwa chokonda kuseka ndi nthabwala. Tikakumana timakonda kukamba zoselewula ndipo mwa dzina lake iye anali wosangalala nthawi zonse.

Mzimu wako uwuse mu Mtendere Happy.

Friday, July 9, 2010

oTenderetu


Nthawi zina ndikakhala phe, nzeru zimandithera ndikaganiza kuti kodi imfa imabwera bwanji pamoyo wamunthu ndipo kuti kodi analenga imfa ndani? Nanga kodi munthu akafa amapita kuti? Mwina nthawi zambiri pamene tili ndi moyo wangwiro, zonse zili myaaa timayiwalako zoti kunja kuno anthu amafa n'kutsikira kuli chete osadzamutemanso gaga. Koma zovutazi zikagwa pakati pathu mpamene timadzidzimuka n'kumati kodi paja moyowu umatha ndithu. Ine ndimaona kuti nthawi imene mnzathu akuyikidwa m'manda ndiyo nthawi yowawitsa chifukwa umakhala umboni woti basi mnzathuyu apa lake watseka. Nthawi zambiri ikafika nthawi imeneyi misozi imatsika ndithu ngakhale malirowo akhale kuti sakundikhudza kwenikweni. Imfa imene mpaka pano imandipweteka kwambiri ndi yamzanga, msuwani wanga, mchimwene wanga, Tenderetu (Tiyenderetu). Imfa imeneyi imandipatsa maganizo ndi mafunso ambiri amene mpaka lero sinditha kupeza mayankho ake.

Ine ndi Tenderetu tinadziwana m'chaka cha 1983 kumudzi kwathu ko Mbuna ku Lilongwe. Chaka chimenecho makolo anga anaganiza zoti mayi anga pamodzi ndi ine komanso mng'ono wanga Gregory ndi alongo anga Jestina ndi Chisomo tipite kumudzi kuti amayi akayang'anire ntchito za kumunda ndipo ife tikaphunzire sukulu komweko. Iyi ndi nthawi ina yowawitsa m'moyo mwanga chifukwa mpaka pano sindimvetsa chimene makolo anga anachitira zimenezi, kutisiyitsa sukulu yapamwamba, nyumba ndi moyo wabwino kupita kumudzi. Iyitu inalinso nthawi imene kunabadwa abale anga ena awiri amapasa, Symon ndi Sibongire. Kubadwa kwa ana amenewa sindidzakuyiwala chifukwa ine ndi amene ndinali mlezi wothandiza amayi anga. Lachitatu lililonse ndinkajomba kusukulu kuwaperekeza amama kusikelo ya anawa ku Chipatala cha Nkhoma chomwe chili pamtunda wa makilomita pafupifupi 10 kuchokera kwathu.

Titangofika kumudzi ko Mbuna kuchokera ku Dzalanyama Forest komwe bambo anga ankagwira ntchito panthawiyo, tinaona zinthu zambiri zosintha chifukwa aka kanali koyamba kwa ife kukhala kumudzi motero sitinasangalale nkomwe kuti tizigona m'nyumba ya udzu, kukakhala pansi kusukulu pamene tinasiya abambo okha m'nyumba yabwino ya malata. M'mawa kutacha ndinapita kukakhala pakhonde la nyumba ya agogoa anga okondedwa, Onganga (mzimu wawo uziwusa mumtendere ndipo ndidzalembanso za gogo ameneyu, amene ndimamukumbukira nthawi zonse chifukwa cha mtimwa wake wachifundo. Timakusowani Onganga). Ndikuothera kadzuwa pakhonde paja ndinaona kamnyamata kamsinkhu wanga katakhala pakhonde la nyumba ya Omayi (achemwali a amayi anga). Maso athu atangoti tha, tonse tinamwetulirana chifukwa tinazindikirana.

Tenderetu anali mphwawo wa bambo anga aakulu. a Mapondera (amuna a Omayi, achemwali a amama). A Mapondera ankachokera ko Mdzinga mudzi umene uli tsidya lina la mudzi wathu kungodumpha msewu wawukulu. Iwowa anali kukhala m'mudzi mo Mbuna ngati kuchikamwini. Amayi a Tenderetu anamwalira pakati pa 1980 ndi 1981. Choncho atangomwalira mayi ake, amalume akewo, aMapondera, anamutenga iye pamodzi ndi abale ake Nana ndi Maseko kuti azikakhala nawo ku Chongoni Forest ku Dedza komwe iwo ankagwira ntchito panthawiyo. Abambo anga anagwirakonso ntchito ku Chongoni ndipo ndikumene ine ndinabadwira koma tinasamukako 1980 kupita ku Dzalanyama. A Mapondera atapuma ntchito 1982 anakakhala kumudzi ko Mbuna pamodzi ndi mwana wawo Richard ndi aphwawo aja, Tenderetu, Nana ndi Maseko.

“Alick” anandiyitana Tenderetu nandikodola. Nthawi yomweyo ndinapita kukamupatsa moni ndikumufunsa kuti ali kalasi yanji. Iye anali sitandede 3 pamene ine ndinali sitandede 5. M'zaka zakubadwa iye anali wamkulu ndi zaka ziwiri koma tinali ofanana misinkhu. Kuchokera tsiku limenelo Tenderetu anali mnzanga waponda apa ine mpondepo. Sitinkasiyana kulikonse. Kusukulu tinkapitira limodzi, kuwelukira limodzi, kusewerera limodzi, kudyera komanso kugonera limodzi. Nthawi imeneyo tinkagona kumphala pamodzi ndi amalume anga aChadza. Usiku pogona tinkafunda bulangete limodzi, ndipo nthawi zambiri timacheza mpaka mwina aChadza kumachita kutiletsa kuti tigone. Panthawiyi n'kuti iwowo anali mu sitandede 8 koma anali kubwereza kachisanu ndi katatu. Tikakondwa kwambiri tinkafika pomaphaphalitsana makofi kapena kutibulana zibakera ndithu mpaka wina athawe. Izi zinkangokhala zosewera ndipo sitimadana ngakhale wina atamenya mnzake kwambiri. Nthawi yamango itakwana ine ndi Tenderetu tinasula timipeni kuchokera ku misomali ya 12 ichesi kuti tizikasendera maboloma. Timati tikangokonza kuti lero tikakhaulitsa mango timayambira ku Bathe (kumunda kwathu), kuchoka apo tili ku kuseli kwa Bathe (kumunda kwa Omayi) mpaka kukamalizira ku Dondo (kumunda kwa amalume ake a Tenderetu). Tikamabwera kumeneko mimbazi zili mzuu, kukhuta, pakamwapa pali noninoni, m'manja monsemu midondolozi ya madzi a mango italemberera. Tikatero ndiye kuti nsima yamadzulo kumangokhala kuyikandakanda basi usiku kumangogeya ndi kutuluka panja kukataya madzi.

Kumapeto a chaka chimenecho titatsekera sukulu komanso titakolola dzinthu abambo anga ananena kuti tonse tibwerere ku Dzalanyama. Inali nthawi yovuta kwa ine kuti ndisiyane ndi mnzanga wapamtima. Komabe sindafune kuphunziranso kumudzi. Nditafika ku Dzalanyama ndinamulembera Tenderetu kalata kumufotokozera momwe ndinayendera. Koma nthawi imeneyo kunali kovuta kuti tizilemberana makalata pafupafupi chifukwa tinali pamsinkhu umene sitinkatha kudzipezera ndalama zogulira masitampa. Kwa zaka zitatu ine sindipitenso kumudzi ndipo sindinaonanenso ndi Tenderetu.

M'chaka cha 1986 abambo anga ananditenga kuti akandionetse kwawo ku Chitundu ku Dedza. M'banja mwathu palibe amene ankadziwa kwawo kwa abambo anga ndipo amayi akuti anapitako kotsiriza m'chaka cha 1976. Choncho ine ndinasangalala kuti ndidzapita kukaona kwawo kwa abambo anga chifukwa kunali abale awo amene ankakonda kudzationa koma ife tinali tisanaone kumene ankachokera. Popita kumeneko tinayima kumudzi ko Mbuna. Aka kanali koyamba kuonana ndi Tenderetu m'zaka zitatu. Pochoka ku Chitundu ine ndinatsalira kumudzi kuti ndichezeko ndi mnzanga. Tonse tinali titakula tsopano, zosewera zathu zinali zitasintha. Panalibenso zomenyana. Tsopano timangosewera mpira basi. Panthawiyi n'kuti Tenderetu atasintha dzina, kukhala Sosten. Komanso anali atameta kugule ndye ena ankamuyitana kuti oTenderetu kapena oSositeni monga mwa mwambo wake. Amalume ake anamwalira chaka chomwecho (1986) m'mwezi wa March. Koma pamene ankamwalira n'kuti atamupatsa ndalama yoyambira bizinesi yogula mafuta a galimoto kwa magalimoto odutsa mumsewu popeza mudzi wathu uli m'mbali mwamsweu wawukulu wa Blantyre-Lilongwe. Iyi inali bizinesi imene inali yolula oanthawi imeneyo. Panthawiyi nkuti amalume ake atasamuka m'mudzi ndikukamanga nyumba yaikulu m'mbali mwa msewu. Amalume ake asanamwalire anapempha oMayi kuti iwo akadzamwalira adzasunge ana onse atatu amasiye) Tenderetu, Nana ndi Maseko). Choncho Tenderetu anapitiriza kukhala ndi oMayi komanso msuwani wake weniweni, Richard. Ndinapemha kuti chaka chimenecho ndiphunzire kumudzi komweko koma abambo anga anandikaniza. Nditacheza kwa mwezi umodzi ine ndinabwerera ku Dzalanyama kukapitiriza sukulu. Nditalemba mayeso a Sitandede 8 mu 1987 ndinapempha kuti ndikachitenso tchuthi kumudzi ndipo anandiloleza. Chaka chimenecho tinacheza kwambiri ndi Tenderetu. Apatu tsopano iye anali kupeza ndalama zambiri chifukwa cha bizinesi ija. Nthawi zina ndinali kumuthandiza kukochola magalimoyo komanso kupopa ndikunyamula mafuta. Chaka chotsatira ine ndinasankhidwa kupita ku Mtendere secondary school ku Dedza. Uwu unali mwayi wanga chifukwa ulendo uliwonse popita ndipobwerera kusukulu ndimayima kumudzi kwathu kwa masiku angapo ndipo izi zinandipatsa mwayi womacheza ndi Tenderetu pafupipafupi mpaka nditamaliza maphunziro anga mu 1992. Nthawi zina popita kusukulu ankandipatsako ndalama zokadyera ndipo ulendo wina anandigulirako malaya. Ndinanyadira koposa.

Nditangolemba mayeso anga a Fomu 4 ndinapempha makolo anga kuti ndikadikire mayeso kumudzi. Iwo anandilora ndipo ndinasangalala kwambiri. Nthawi imeneyi ndinamuthandiza kwambiri Tenderetu pa bizinesi yake ya mafuta. Analinso kugula ndi kugulitsa mbewu, ufa ndi zinthu zabiri zopezeka m'magalimoto odutsa. Tenderetu sanasowe chilichonse. Anali kusamalira pakhomopo tsopano ndiye. Anali wopatsa kwambiri. Mudzi wonse unamudalira. Iye anali wakhama pantchito ndipo samalola zibwana kapena zaulesi. Panthawiyi n'kuti Sadam Husein yemwe anali mtsogoleri wa dziko lija la Iraq atatchuka kwambiri chifukwa chokaputa dziko la Kuwait m'chaka cha 1990. Tenderetu anali munthu wokonda kumvera wayilesi kuti azimva zomwe zikuchitika kunjaku. Kulimba mtima kwa Saddam kunamusangalatsa ndipo chifukwa chakuti naye sanafune kuti anthu azimutola poti ndimwana wolemera anadzitcha kuti Sadam. Iye sikuti anali waukali kapena wokakala moyo ngati Sadam koma anamusilira Sadam chifukwa cholimba mtima. Dzina la Sadam anatchuka nalo kwambiri.

Mayeso anga atatuluka ndinasankhidwa kukapitiriza maphunziro ku Chancelllor College. Apa tsopano ndinadziwa kuti tidzatalikirana ndi Tenderetu. Chaka chomwecho iye anasiya sukulu mu Sitandede 8 ndikupitiriza bizinesi yake. Anapeza malo ake ndikumangapo nyumba. Mu 1995 Tenderetu anakwatira. Ukwati unachitika ndili kusukulu motero sindinathe kukhala nawo. Ndinakhumbira kwambiri. Ngakhale Tenderetu anakwatira, anapitiriza kuthandiza oMayi komanso anthu ambiri am'mudzi mwathu ngakhalenso achilendo. Anapala maubwezi ambiri chifukwa cha bizinezi yake. Analimbikira kulima komanso kugula mbewu zosiyanasiyana. Atazindikira kuti bizinesi ya mafuta inali yosadalilika chifikwa cholondedwa ndi apolisi iye anaganzia zotsekula sitolo. Anamanga sitolo yake yayikulu momwe munali katundu wosiyanasiyana. Anthu ambiri anali kudzagula katundu ena pangongole. Tsiku lina tikucheza nditapita kukamuona kuchokera ku Zomba anandiuza kuti nthawi zina saona kufunika kwa maphunziro chifukwa aphunzitsi amene an'kamuphunzitsa ku pulayimale anali kuvutika kwambiri ndipo kuti ena mwa iwo anali kulephera kubweza ngongole zimene anakatenga musitolo yake. Iye ananena kuti ana sangalimbikire sukulu ngati aphunzitsi akukakongola ndalama kwa anthu amene sanapitirize maphunziro. Pena ndinagwirizana naye makamaka ngati timapita kusukulu kuti tidzakhalae ndi moyo wabwino. Koma nkhani ya aphunzitsi ndi ina yapadera. Tenderetu anali ndi mfundo zake ndipo anali wokonda mtsutso pa nkhani zosiyanasiyana. Chinthu china chimene iye ankakanitsitsa kuti sangachite ndiye kusunga ndalama zake ku banki. Mawu ake anali akuti iye saona chifukwa choti azikakhalira pmazele chifukwa cha ndalama zake zomwe.

Pasitolo pake panali pachibulo. Sipankasowa munthu. Panali posewerera ntchuwa, panali pogulitsira nzimbe, nthochi, panali pomwera fanta, panali powusira anthu apulendo. Ena mwa iwo maka oyenda panjinga kuchokera mitunda ya Chitundu anali kusungitsa njinga zawo n'kukwera magalimoto wa m'tawuni. Tenderetu anali mlerakhungwa chifukwa sanasankhe anthu ocheza nawo, akulu, ana, achinyamata, olemera, osauka, owadziwa, achilendo. Chifukwa cha mtimawu anthu tsopano anamutcha Bakili. Chifukwa cha ichi, anthu anamudalira koposa. Anamusankha kukhala wapampando wa sukulu komiti komanso wapampando wa chipani ku Bathe Area. Uwutu sunali udindo wamba. Nthawi imeneyo phungu woymira derali anali Wolemekezeka a Louis Chimango moti pamene iwowa anali kuyendera derali aakuluakulu ake amene amayenda nawo anali a Tenderetu. Chinali chinthu chopambana kuwona mnzanga atafika pamenepa. Nthawi zambiri tikamacheza anali kukamba nkhani za ndale ndi chidwi ndipo kawirikawiri anali kufuna kudziwa kuti ine ndili mbali iti chifukwa chakuti ndimakhala kummwera. “Ndale zikuyenda bwanji kum'mweraku?” Ankakonda kufunsa choncho tikakumana. Iye ankakonda kupitiriza kunena kuti, “kunotu ndiye ndi Kongiresi basi, ife onzathu ndoChimango basi, tambala wakuda! Ochawa songawine kuno” Tikatere tinkaseka.

M'mwezi wa July, 2004 mwana wanga atagonekedwa kuchipatala . Tsiku lina chakumadzulo ndinkakonzekera kukamuona mwanayu pamene ndinalandira telefoni yochokera kwa mchimwene wanga Richard Mapondera amene ankakhala ku Blantyre. 'Tenderetu wamwaliratu" anatero Richard, mosisima. 'Wagundidwa ndi galimoto..." anapitiriza. Ndinaponya foni pansi n'kulowa kuchipinda. Ndinalira mokweza. Thupi langa lonse linanyowa ndi chitungu cha chisoni ndi mantha. Sindinakhulupirire kuti zingatheke kuti mnzanga Tenderetu n'kumwalira. Patatha ola limodzi ndinatuluka kuchipinda n'kunyamuka kupita kuchipatala kukaona mwana wanga. Nditafika, mkazi wanga anandilandira ndichimwemwe kufuna kunditsimikizira kuti mwana anali kupeza bwino tsopano. Koma anadabwa kuona kuti misozi inali kutsika m'masaya mwanga. Anandigwira n'kundiuza kuti ndisade nkhawa mwana ali bwino ndipo amatulutsa tsiku lotsatira. Ndinamuwuza kuti Tenderetu wamwalira. Sindinathe kuwagwira mawu ndipo izi zinadabwitsa anthu ena onse m'chipatalamo chifukwa anayamba kuganiza kuti mwina mwana uja wamwalira. Tinatuluka panja.

M'mawa, Richard uja anabwera kudzanditenga pa galimoto yake kupita kumudzi. Njira yonse tinayenda mwachinunu. Titangowoloka Diamphwe tonse misozi inayamba kutsika. Galimoto isanayime nkomwe azimayi anali atayiwunjirira uku akuloza tsidya lamsewu akulira mokweza. Zinali zomvetsa chisoni. galimoto yonyamula mowa wa Chibuku imene inatenga moyo wa mbale wanga inali gada! tsidya la msewu moyang'anana ndi siwa. Mtima wanga unasweka ndipo ndinalakala nditakangoyatsa galimotoyo. Azimayi analira mokweza ngati akuti 'chonde kabwezereni ku chigalimotocho.' Titapuma tinakazungulira galimotoyo yomwe tsopano apolisi anali kuyilondola powopa mkwiyo wa anthu.

Imfa ya Tenderetu inali yomvetsa chisoni. Patsikulo, akuti chakum'mawa kunafika galimoto yogulitsa buledi kuchokera ku tawuni ku Lilongwe. Ndipo ogulitsa bulediwo sanamupeze Tenderetu ndipo anangosiya buledi n'kunena kuti ndalama adzatenga madzulo popotoloka kuchokera ku Dedza. Galimotoyo inabweradi madzulo cha m'mapasiti 6. Inamupeza Tenderetu ali m'nyumba ndipo atamva hutala iye anatuluka ndi mwana wake m'manja kukayankhulana ndi wogulitsa buledi uja. Atauzidwa mtengo wa buledi amene anasiyayo iye anabwerera m'nyumba kukatenga ndalama. Pobwerera mwana uja anamusiya ndi amayi ake. Atafika pagalimotopo anaona kuti mbali inayo yamtunda wa Lilongwe kunali kubwera galimoto yonyamula mowa wa Chibuku yomwe inali pa liwiro lalikulu komanso linali litataya mbali yake nkulunjika mbali imene inayima galimoto ya bulediyo. Ataona izi, Tenderetu anaganiza zothawira mbali inayo. Asanamalize n'kudmphira mbali inayo, chigalimoto chija chinamuvungira limodzi, kum'khwekhwereza n'kukamuponya pafupifupi pamtunda wa malipande 100 uku chigalimotocho chikunkhulira mpaka kukagudubuzika m'munda. Mdima n'kuti utagwa. Ndiye kunali kuyitana kwinaku anthu akusaka Tenderetu. Pamene Tenderetu amapezeka kumizele anali atamwalira ndipo thupi lake litanyenyeka kwambiri. Adapita n'chigalimoto Tenderetu.

Kunali namtindi wa anthu patsiku loyika maliro a Tenderetu. Anthu anapereka maumboni a moyo wa Tenderetu. A kumpingo, kusukulu, abizinesi, kuchipani komanso makasitomala. Ena odutsa pamagalimoto awo amati akamva zoti malirowo anali a Tenderetu anali kuyima kukhuza nawo ndikusiya chipepeso. Ambiri anabwera kudzakhala nawo pamwambo woyika malirowo. Mwa anthu ongodutsawo wina anapempha kuti ayankhuleko m'malo mwa anthu ena onse amene ankamudziwa Tenderetu. Iwo anali kungodutsa paulendo wawo wopita ku Lilongwe koma anayima ataona kuti pachitika zovuta. Atamva kuti womwalirayo anali Tenderetu, sanamvetse. M'kuyankhula kwawo iwo anati: “ife tatayika chifukwa cha imfa imeneyi. Ife mwana uyu ankang'unga mnzathu, sankaona kuti tachokera kuti, tavala chiyani, tili ndi chiyani, koma an'kangotilandira n'kumacheza nafe ngati akucheza ndi anzake. Timayima panyumba pakepa n'kumwa madzi, kusungitsa njinga zathu n'kumapita ulendo wa ku Lilongwe, pobwera amatilandira mwaulemu. Ndiye lero n'kumati Tenderetu wamwalira? Tatayika ife! Bakili wathu wapita, ineee! Tikapumira kuti ifeee..." ndiye panabukatu chiliro; “Bakili wathu wapita, Bakili wathu watisiya ife.”

Lero pamalo a Tenderetu ndi pabwinja pomvetsa chisoni. Mkazi wake anabwerera kwawo ndi ana ake atatu ndipo anakwatiwanso ndi mwamwuna wina. Mng'ono wake, Maseko anatsala pamlopo anagulitsa malata zitseko ndi katundu wina yense amene anasiyidwa. Naye anamwalira atamenyedwa chifukwa chakuba. Nyumba zonse zinagwa. Mlongo wake Nana anabwerera kwawo ndipo anakwatiwa. Koma ndidzakumbukira Tenderetu nthawi zonse ndipo palibe amene angafufute Tenderetu m'moyo mwanga. “Ndimakusowa mnzanga Tenderetu. Ambuye asunge mzimu wako mu mtendere.”