Tuesday, January 8, 2013
Tachilowa nawo
Masiku atheradi kuchitseko. Anga bodza kuti tagonera. Ndife sundwe. 2012 tatseka tione kuti 2013 wafungatanji? Koma tisanathe mtunda mu 2013 tiyang'aneko kumbuyo. Chilumika chimenechi chinali ndi zake zosayiwalika.
Pali zinthu zingapo zimene zidzandikumbutsa za chaka cha 2012, zabwino ndi zoipa zomwe. Paja amati zimakhala bwino kuyambira zabwino.
Kabaza
M'mwezi wa February ndinagula njinga yanga ku 5 Miles - AfriCycle. Ndiyamika Nijo mnyamata amene anandisankhira njinga imeneyi. Maso kunyoza. Atandilozera njinga imeneyi ndinkaona ngati wandisankhira chikhokhololo! Koma ayi ndithu Nijo anandisankhira Mlalu weniweni!
Mlalu wanga wandionetsa malo m'chaka chimenechi. Mwa malo amene ndidzawakumbikire chifukwa cha mlaluwu ndi Mwandama (kuja kunakafika Mlembi wa Bungwe la Mgwirizano wa Mayiko onse a Ban Ki- Moon, ku Zomba kuno, mudzi wa Kansonga m'chigwa cha pakati pa mapiri a Zomba ndi Malosa - malo okongola kwambiri mudzi umene ukudyetsa tawuni ya Zomba ndi zipatso, komanso ku Phalombe. Mlaluwu wandionetsa Chingale, Mayaka, Ulumba ndi malo ambiri mu Zomba muno.
Imfa ya Bingu
2012 chinali chaka chosautsa kudziko lathu lino. Nthawi zina ukamaona momwe atsogoleri athu amatumbwira akakhala pampando maganizo amayamba kubwera kuti mwina n'takhala ine zimenezi zingathe. Koma zikuoneka kuti aliyense akakhala pachimpando chimenechi amaona ngati iye ndiye namalenga wa tonsefe. Komatu kumwambako Chisumphi alipo ndithu ndipo dongosolo lake palibe angalimvetse ngakhale amene mukuyti ndi aneneri olulawa! Iye ndi tsidya lina. Chili kuti lero chitsulo cha njanji? Mwina chidakathera pachipala! Achinyenyanyenya? Amayi samalani. Kuno ndi kunja kudayanja lichero!
Richard (uwuse mu mtendere mzimu wako)
M'bele la amayi wanga munabadwa akazi awiri, Omama ndi Omayi. Mukafuna kudziwa za mayina amenewa pitani kwathu ko Mbuna mukafunse. Akakuwuzani kuti Omama ndi Omayi ndani. Richard anali womaliza kubadwa m'nyumba moMayi. Ndi ine tinangosiyana zaka zochepa kwambiri pobadwa. Tinakulira ndi kusewera limodzi makamaka pamene tonse makolo athu ankagwira ntchito ku Ngoma (Nkhalango ya Chongoni). Atatsiriza maphunziro ku Kongwe analowa ntchito ya polisi ndipo anakwera pamaudindo mpaka kufika pa Superintendent. Koma m'mwezi wa August, Richard anatisiya kuchipatala cha Nkhoma, kwathu. Komatu dzikoli ndilovutadi kulimvetsa. Zambiri ndidzakambabe koma pano tizingopemphera kuti Mulungu asamalire ana ake, Anne, King, Tiya, Shireen ndi Yankho komanso mayi awo.
Yaounde
Chakachi ndinachitsendera ndi ulendo wa ku Cameroon ku msonkhano wokambirana za ziyankhulo za mu Africa makamaka pa ntchito yochita kalondolondo wa chiwerengero cha ziyankhulozi, chiwerengero cha anthu oziyankhula ndi malo amene zikuyankhulidwa mu Africa muno. Unali ulendo wosangalatsa kwa ine chifukwa chakuti kanali koyamba kupita dziko limene anthu ambiri amayankhula Chifaransa mu Africa muno. Inetu Chifaransa ndinachiphunzirapo kalekale ndili mu fomu 1 ku Mtendere zaka zimenezo. Pierre et Seydou woloweza yemwe uja anatipulumutsa mpaka ife kuoneka dolo madoda oyankhula Chingerezi chokha akulephera kunena chakudya chimene akufuna kudya mu resitilanti! Sindikunena munthu ine! Koma zinali zosangalatsa kwambiri. Pamene imatha sabata ayi ndithu ife tinali titalolera Chifalansa chokwanira kufunsira (njira).
2013 wolowa chiyimirire
Ngati ndikulemba lero pa 8 Januwale ndiye kuti ndalowa nawo. Koma sindinachiyambe bwino kwenikweni. Kaya ndi Namalenga kaya ndi Dyabu kaya koma ndinapezwa ndithu munthune. Pa 31 tinapita kwa anzathu kuti tikachilowere limodzi. Ndiyetu kunali kutafuna ndikukhwasula. Dansi inathyoledwa mosaona kuti apa pali mwana wanga kapena apa pali obaba ndi omama. Tangoganizani mabanja awiri ndi ana awo onse aliyense akuthyola sitepe! Panavutatu. M'mene imati 2kaloko m'mawa woyamba wa 2013 tinanyamuka wa kunyumba. Komatu chongoti lowu, pakama thasa, inu! Namo m'mimba dzambatuku! Poyerayeratu! Kuyesa kutembenukira uku, kapena uku, kapena chafufumimba, pola, nikisi! Madzi akumwa kapena? - ndiye kukolezera! Kuyesa kukanyonyomala pamtondo, kuti mwina mpweya wokha, ayi tele kuli zii! Tetetete! Kokoliko! Ukutu nkuti mnzanga wapamphasa akungouliza wa mtendere uja! Ndipite kuchipatala? Ndi adiimiti kale! Nanga zoona kuchipatalako buku tikachite kulitsekulitsa pa 1 januwale? Ndiyetu kunali gubidigubidi kuwunguza mtela. Wapezeka panadolo. Mpwintheni! Kuyesa kugona, ayi tele, tazemberatu tulo. 6 Koloko kwacha, wa kuchanjausi kukadzithira madzi kuti mwina kapena. M'mene imati 7:30 ndafika pakhomo la chipatala. Chikwangwani chikuti lero latchuthi amatsekula 8:30! Mtsonyo wakewo! Kubwerera kunyumba, mnzanga wadzuka akujijirika ndi zanyuwele! Mpamene ndimaulula kuti bwanawe mnzakone sindidatinyanthe tanyuweletu! Anangoti kukamwa yasa! Ndiyetu masana onse kunali kuliza mkonono! Koma ayi lero suyu tikupumayu! Koma wachewuchewu! Talowa ndithu ndipo tiyamika Lezayo kuti watikondera, Chichewa cha lero! Ticheza m'chaka chimenechi!
Subscribe to:
Posts (Atom)