Friday, February 22, 2013
Amalume Ndakhoza
Zinthu zimasinthadi. Kale silibwerera. Kodi lero mwana akakhoza mayeso a sitandede 8 makolo amachita chiyani? Ndikudziwa kuti kholo lililonse limasangalala mwana akakhoza. Mwana wanzeru asangalatsa makolo, atero Malemba. Komatu mwina makono kukhoza mayeso opitira ku sekondale kudasuluka! Simwakalenso ayi. Mumvere ife. Kaletu kukhoza mayeso a 8 siinali nkhani ya masewera. Chinali chinthu chopambana kwambiri pamoyo wamunthu! Ku Sekondale kunali kumwambatu, kopita owerengeka okha. Ena amapita atayimba sitandede 8 ka 8 kamene ena ka 14. Ee olipo kwathu odayamba 8 ife tisanabadwe, tidayamba sukulu mpaka kukawapeza. Ndi aphunzitsi omwe kumachita kuwalemekeza powaitana, oLove, oBatison! M'dziko muno mudali masekondale ochepa kwambiri. Ma MCC anali ang'onong'ono kwambiri mwinanso osakwana 10. Anthu amachoka kummwera kukaphunzira kumpoto - ku Borero MCC kapena ku Chawa MC kwa Lobi ku Dedza kapenanso ku Bilira ku Ntcheu. Ndiye ukalakwa mayeso a 8 panali zinthu ziwiri zoyenera kuchita. Kusiya sukulu kapena kubwereza basi. Kunalibe sukulu za wanthu zangoti mbwee lerozi. Zina zophunzitsira m'chilabu! Masiku amenewo kubwereza sitandede 8 sichinali chachilendo. Ndipo tinkakhulupirira kuti palibe angakhoze mayeso chaka choyamba. Koma mwina chaka chachiwiri kapena chachitatu. Ndiye kwinako tinkangosewera dala. Tikanavutikiranji ochimwene, omalume okadali m'kalasi momwemo ndiye iwe ukawapose? Kupanda ulemutu!
Ndidafotokoza kale za kwathu - mopaza momwemo. Koma lero ndifuna ndilanduleko za kumtima. Nkhani imene nthawi zina imakhetsa tsozi komanso imandipatsa phwete. Mavutowa amationetsa zambiri - zopimitsa moyowu. Ndinalemba mayeso anga a sitandede 8 kachiwiri mchaka cha 1988. Pameneo nkuti mkulu wanga ali folomu 3 ku Dzenza. Malipiro a sukulu inali nkhani yaikulu kwambiri. Ndaiwala kuti zinali ndalama zingati. Mwina K10 mwinanso osakwana. Koma wopeza K1 anali mwana wamunthu - pwepwete mponda matiki. Mchimwene wangayu ankamulipiria ndi Ochimwene - kafunseni kwathu kuti Ochimwene ndani? Olipo omodzi okha mudzi wonse. Paja ndidanena kale kuti Omayi, Omama oliponso omodzi okha. Mukawapeza! Ochimwene odali ophunzitsi o ku MCC. Pa Malawi pano mphunzitsi ndi mphunzitsi. Nthawi imeneyo Malemu mchimwene Richard analinso fomu 3 olipirianso nkukhala Ochimwene omwe aja. Ndiye ine ndikalowenso pomwepo? Koma nanga ndikadatani munthu nzeru ndili nazo! Ndinali wanzerutu ine. Mukafunse a Maliko ku Dzalanyama akakuwuzani "N'dadziwatu ine kuti m'dzadziwa; tsono m'dadziwira ku?" hahahahahaha! Ine ndidadziwadi chaka chimenecho ndipo ndidadziwira ku Mtendere, kwa Malirana.
Lidali lachisanu pa 14 October 1988. Sabata yathunthu yatha chilengezereni mayeso a sitandede 8. Ife osamva kuti mayeso anayenda bwanji. Titatsakamira m'nkhalango ya Dzalanyama. Lamya kunalibe. Kukaona mayeso ndiye kuti wina apite ku tawuni (100Km). Galimoto kunalibe. Ndiye kumangodzikhalira ngati makedzana. Tsiku limeneli linatalika kwambiri. A Hedi anapeza mwayi wokwera nawo galimoto ya Folositi kupita ku tawuni kukaona mayeso. Galimoto ikapita ku tawuni inali chaka isanapotoloke. Mbuzi mukaimasula sikumbuka kubwerera m'khola. Galimoto ikapamita kutawuni masiku amenewo imadzaza - opita kuchipatala, kuchigayo, ena akalaweko kazibeki, ena wa kwawo, ena obwerera. Galimoto inali imodzi. Timadziwa kulira kwake. Tinkaizindikira ngakhale ili mitunda isanu.
Nthawi inali cha m'ma 4koloko masana. Tinamva mzizima wa landrover kuti yafika ku ofesi. Kaya chinachitika ndi chiyani kuti ifike masana tsiku limenelo? Nthawi yake inali 10 koloko usiku zingavute chotani. Ine ndi mnzanga Innocent tinangodzambatuka kusiya mpira, wautali. Pakanakhala mphoto za mpikisano wothamanga tsiku limenelo tikanalandirako. Tikuti tizifika pa chipata cha ofesi, atulukira adalayivala bambo Lipenga, anzawo a bambo anga. Ndimacheza nawo kwambiri masiku ano. Munthu wopanda zibwana. Makofi saumira. "Ndiye mukuthamangira kuti ana opanda nzeru inu. Ntchito kumangosewera mpira ndikudya maula!" Anakalipa maso ali psu ndi ukali! Jega! Thukuta lonse gwa! Maso phethipethi! Nkhope zyoli -thupili silinalinso langa. ndinamuyang'ana Innocent! Anayamba kusisima! Thanthwe long'ambikatu ndibisale momwemo! Lili kuti? Lindimeze ine lero, dziko landida! "Ndikunamatu mwakhoza pitani kwa a hedi anu akakuwuzeni." Timve ziti? Mulungu aziwakhululukira ndithu!
Pa 14. Pakatikati pamwezi! Osati kuti masiku ena amakhala ngati pa 27 pakhomo pathu ayi. Ife nthawi zone panali pa 14. Koma nanga pa 14 khobidi ukabwereka kwa yani? Kwada! Tinakhala pakhonde.Pa siwa. Chimwemwe chija chinali chisoni. Ngati nthanotu! Aliyense kumangosisima. Kodi ndinalakwa kukhoza mayeso. Sukulu yonse tinakhoza anthu atatu okha ine ndekha wosankhidwira ku sukulu ya National, ya Katolika! Mulungu akandikondera bwanji kuposa pamenepa? Ndinawayang'ana amama. Anali chete. Ndinadziwa chimene chinali mumtima mwawo. Mwezi umenewo ndinali nditawasungitsa K20 (ananena kuti andisungire). Koma sanasunge. Anagula chakudya inenso ndinadya nawo! Mlandu wathu. Amama anali ndi manyazi mumtima! Musadandaule amama! Komatu ine ndalamazi ndinkakonzekera kudzapitira ku sekondale chifukwa chikhulupiriro ndinali nacho ndithu. Kumene ndinazipeza ndalamazi ndi nkhani ina. Komatu ine sindinali manjalende. Ukaipa dziwa nyimbo. Ndinkapeza kangachepe kothandizira pakhomo ngakhale ndinali wamng'ono. Zikomo madala pondiphunzitsa ntchito zanu zaluso. "Komatu paja amalume ako anati ukakhoza udzapite ku Kasungu akakupatsa fizi" Anatero amayi. Koma ku Kasungu ndipita ndi miyendo. Sikolira ndalama ya basi. Madala anali phee ngati sizikuwakhudza. M'thumba mwangamu munali K8. Ingakafike ku Kasungu? Usiku umenewo amama anayenda khomo ndi khomo kusakasaka khobi, olo! Chisoni chinakula. Ndakhozeranji ine?
Lachiwiri pa 18 sukulu zatsekulira. Anzathu alowa m'kalasi. Ife tikadali kosaka makobidi oyendera kupita ku Kasungu m'malo molowera mtunda wa Dedza. Mwana wamwamuna n'kabudula mbambadi. Ndi K8 yanga pathumba ndinanyamuka ku Dzalanyama pa lole yonyamula nkhuni yaulere! Pamwamba neng'a! Alemekezeke wamwambamwambayo. M'mene imati 9 koloko mnyamata wafika mu Lilongwe, K8 yake pathumba, khadi la Kongiresi mbali inayi, wa ku Kasungu. Ndinafika ku ofesi ya Khondowe pafupi ndi depoti ya basi - Khondowe wake yemweyu mukumudziwayu. Anali bwana wa amalume anga. Kumene kuja ndinafunsa ngati kunali galimoto yopita ku Esiteti imene amagwirako ntchito amalume anga. "Ayi kulibe koma ilipo ina yopita esiteti ina ku Kasungu komweko. Utha kukwera nawo ukatsikira pa Bua usanafike pa Kasungu kwinako ukakwera matola kapena basi" anatero alonda! Palibe vuto. M'mene imati 10 koloko wanyamuka mnyamata kusiyana ndi Lilongwe kuloza Kasungu. Galimoto yaulelenso iyo! M'mutumu maganizo khumi ndi asanu. Mulungu sataya wake. Khalekhaleni uyo tafika pa Bua. Akuti basi ife tikukhotera uku. Inu mupeze matola kufika paboma kwinako mukakwera basi yopita kwa Wimbe. M'mimbamu njala ndiye yayamba kuluma. Koma K8 ndikayamba kugulira nzimbe pano ndikafika nayo? Ndinalingalira amayi anga m'mbuyomu. Ndinadziwa kuti anadziona iwo olakwa pogwiritsa ntchito ndalama zimene anandisungira. Koma akanachita chiyani munthu wa mayi ana ali ndi njala. Akanasunga bwanji ndalama pakhomo palibe ufa. Amama musadandaule. Mulungu atisamalira tonse. Ali makono bwenzi nditawaimbira foni amama kuti ndili pa Bua kudikira matola, ndayenda bwino. Ha! 1988! Kwii yaima ya polisi. Landrover yakuda ija. "Ukupita kuti ayise?" Yaulelenso? Kwera, ulipira 30tambala! Dziko ili sungalimvetse. Mphindi zochepa ndafika pa Kasungu, ndatsala ndi K7.70 yanga.
Wimbe via Mtunthama! Chitero chikwangwani cha bsi pa Kasungu! Ndaipeza basi ija ili khirikhirikhiri! Mwana wamunthu atakungana pa depoti ya Kasungu. Thupi lonse tsembwe. Basi ndiye ndi imeneyi, koma ndikwera? Chipwirikiti chinali pakhomo la basicho n'nali n'sanachipenyeko m'moyo wanga. Mantha anandigwira. Kodi ikandisiya basi imeneyi ndikagona kuti? Ndiyenda bwanji? Ndiwauza bwanji amama? Amalume sakudziwa kuti ndikubwera. Mwina akadadzandichingamira pa boma pano. Poyang'anitsitsa ndinaona kuti pakhomo la basi paja panali mayufi, amene anali ndi khadi ndi amene amaloledwa kulowa. Inetu monga nzika yokhulupirika khadi ndinali nalo. Ndilephereranji kukwera basi. Ndinalimba mtima. Ndafika pakhomo, K7.70 yanga m'thumba khadi langa m'manja. "Talowa iwe!" Ine selelu, dyadyamphireni! Posakhalitsa wakhulula buleki dalayivala! Wapsa wa kwa Wimbe. Khadi langa m'thumba ndalama pamanja kuti kondakitala akafika ndimve kuti ananena kuti ndalama zingati? Kaya zikwana? Zikaperewera ndidandaula. Ndimuuza kuti ndangokhoza mayeso ndikukapempha fizi ko Malume. Monga samvetsa? Mtunthama, ikadali chidzadzire basi.
Dzidzidzi, Wimbe Trading Centre! Masitolo ali ndandanda. Yafika basi. Insipekitale, kondakitala sadzaoneka! Ine tsikuu, ze! Kupisa m'thumba, ilipo K7.70. Khadi mbali inayi. Ndafikatu ine kwa Wimbe. Ndalipira 50tambala kuchoka ku Dzalanyama kuja kudzafika kwa Wimbe. Kulipiranso ku galimoto ya polisi. Lili lero ndikanati ndipereka umboni pa zazikulu zomwe Mulungu anandichitira. Ku Dzalanyama kuja tinali ndi abwana a Banda amene kwawo kunali ku Kasungu ndipo ndi amene anandiuza momwe ndingayendere. Akazi awo anali aphunzitsi anga ndipo anandiuza kuti ndikafika pa Wimbe ndikapite ku sukulu komwe bambo awo a Kayembe ankaphunzitsa. Fikani kumene kuja, chisomo chokhachokha. "Ugone, Moses akabwera akuperekeza ku Kabuma mawa m'mawa sipatali." anatero mayi ake a Moses. Kwiyo yalira nkhukhu. Mwana wakhoza. Ambuye azilemekezeka ndithu. Usiku umenewo tinachezera kucheza ndi Moses. Moses anali mnzanga pamene ankakhala ndi achemwali ake ku Dzalanyama kuja koma tsopano anali kutchuthi kwa makolo ake.
M'mawa tinayenda pansi mitunda ingapo kundiperekeza kwa amalume anga. Kungondiona amalume, sichimwemwe chakecho. Moyo wanga unasinthiratu. Chimvereni zotsatira za mayeso kanali koyamba kuonetsa nkhope ya chimwemwe. Chisoni chonse chinatha. Koma amama kaya anali ali bwanji?
Ulendo wa ku sukulu sunalinso wachewuchewu. K300 pathumba - Leather and Luggage, gombeza, nsapato, patapata, sitonkeni. Mungawadziwe Oyaliki? Kufika kusukulu, kulipira fizi yunifolomu zonse kukwana K104. Chenji chambirimbiri! Ambuye azilemekezeka ndithu! Uwuse mu mtendere mzimu wa amalume, Harrison Bauleni Kuchiudza (HBK)!
Wednesday, February 6, 2013
Madala: Mphawi Wachimwemwe
Kodi ndi chiyani chimakupatsani chimwemwe m'moyo mwanu? Chuma? Ntchito? Mkazi? Mwamuna? Maphunziro? Nzeru? Anzanu? Chiyani? Aliyense ali ndi chinthu chake chimene chimamupatsa chimwemwe komanso chimene amadana nacho kwambiri. Ena akapata ndalama sasowa, amafuna aliyense amupatse moni ndipo adziwe kuti zinthu zikuyenda. Anthu otere akapsa m'thumba ndi nkhope yomwe imakhala ya makwingwirima. Ndalama zimabweretsa anansi. Zikatha, anansinso amathawa. Komanso nthawi zina ndalama zimabweretsa adani. Kunja kunotu kuli kaduka kapena nkhwidzi. Wina asakwete, walakwa, avala ufiti kapena umbava. "Akusolola" timatero! Moyo wa masiku ano ndi wovuta, popanda ndalama, dziko limayima, ulemu umatha. Angakulemekeze ndani ulibe makobidi? Umasanduka chitselekwete! Koma bwanji ukangosanja? "Yes wamkulu, Zoona abwana, eetu achikulire, shuwatu big" mayina mbwee chifukwa cha ndalama. Koma kodi munthu angakhale wosangalala popanda ndalama?
Enafe tidakulira m'mavuto oposa a Majoti. Nkhani ya Majoti ndi yopeka koma yathu ndiyolula ndithu! Mutha kukamba za mavuto amtundu uliwonse amene munthu padziko lapansi pano amakumana nawo. Tadutsamo. Tatulukamo. Mukamationa kusalalaku sikuti tidakulira ku Nyambadwe! Ngakhale kwa Ntopwa kumene sikungayandikireko! Koma chinsinsi cha Mulungu amachidziwa ndani? Thupili sikuti ndi chambiko chalerochi. Ndilobadwa nalo. Takula nalo. M'mavuto omwewo. Koma chinthu chimodzi chimene ndidakula nacho ndicho kupeza chimwemwe m'mavuto! Simkuluwiko!
Umphawi supha munthu! adatero madala! adalasa penipeni. Bwenzitu enafe titatsogola. Malemu Opapa (madala mzimu wanu uwuse mu mtendere), ndiye chitsanzo chabwino cha munthu wosangalala pamavuto, pamtendere. Simisala. Koma kusalitsanza dziko. Kwa anthu amene amatidziwa bwino kubanja kwathu, kuseka sitiumira, ndichizolowezi. Kodi ndimayesa kuseka ndiulele, sochita kugula! Ndikumbuka masiku amenewo tikukula, titadya mgawiwa wamadzulo opapa ndi omama otafatsa kutilakatulira nthano za pa ubwana wawo, za ku sukulu, za ku Joni.. ife tikuseka chikhakhali. Uku ndiko kudali kukhala kwawo, kukula kwathu. Kuseka sikunkalira ndalama. Osati kuseka kwa masiku ano kopemphera khobidi!
Lero ndapukwa opapa: Richman Bwanali Kadango kwawo ku Chitundu kwa Che Tambala m'mudzi mwa a Chawala. Myawo wapaphata kukakwatira mchewa wa ko Mbuna ku Mpenu ko Mazengera ndikusiya Chisilamu n'kuyamba kudya kapado, mbewa, kupapira masese nkukathera mu Utimiki wa Dutch! Nthawi zina makolo akamapereka mayina kapena tikamadzipatsa mayina kaya chimakhala chiyani. Inetu bambo anga pobadwa anapatsidwa dzina loti Che Madayika. Koma atakula andziwika ndi dzina loti Richman! Kaya anali matemberero kaya. Anafa osauka. Koma wosangalala, wonjoya. Bambo anga atasiya sukulu anapita ku Joweni kukasewenza ku mgodi. Pobwera kumeneko ndipamene ankabwera ko Mbuna kenako nkukayamba ntchito ku Chongoni, ku nkhalango, ife nkumabadwa. M'banja mwathu tilipo ana asanu ndi anayi, onyamata osanu ndi mmodzi ndi otsikana otatu. Tonse tilipo. Anaigwiratu makolo. Koma sizinali zachibwana kusamalira mbumba yonseyi. Madala anali munthu wolimbikira ndi wogwiragwira. Kaya ntchito zinazi anazidziwa bwanji kaya? Kaya inali mphamvu ya uchawa kaya? Komatu ankatha chilichonse: kusoka, kusema, kuluka, kukhoma! Chilichonse chochita ndi manja. Mgaiwa ukapezeka magwero ake anali amenewa. Tikavala nkhani yake inali yomweyo. Luso lina tinaphunzirako - koma izi n'zatsiku lina. Analipo masiku owawitsa ndithu nthawi imeneyo. Kudikira madala kuti abweretse chimanga kapena ufa mpaka pakati pa usiku, tulo titachita chipongozi, nkhani zitatha, m'mimba mukubangula. Akafika munthu wamwamuna khosi litalowa mkati ndi chibinyira, kusaukira mbumba nkumati adandaula, ayi ndithu! Ayambepo kukuyalirani nthano za zimene waziona tsikulo, inu njala yonse kutha nkuseka! M'mawa sikuti agonereza ayi, buli wa kuntchito! Akasakenso. masiku n'kumapita, ana nkumakula.
Madala anali ndi anzawo ankhaniankhani! Akakhala pagulu, kwawo kunali kuseka ndi kuseketsa. N'kuti kulibe anzawo? Sianzawo a ku Mchinji aja adakonzetsa thupi lawo kuti lisaonongeke pa 20 July paja? Sitinalandire ulemu ndi mphatso kwa anzawo chifukwa cha kucheza kwawo? "Atate wanu nanzanga zedi, timacheza zedi anga munthu ni mphwake" ankaterotu anzawo. Ukapita kukawayendera ku Mchinji uko adasamukira atapuma pantchito amakuyendetsa benchi iliyonse mumsika kukuonetsa kwa anzawo, "mwana wanga wa ku Zomba uja ndi ameneyu". Palibe chimene chinkawasangalatsa madala koposa kunyadira ana awo. Kodi sitinapeze malo chifukwa cha anzawo? Kodi lero ku Mchinji sikwathu chifukwa cha anzawo? Kodi lero kuti tipite ku Chongoni, kwa Kankhomba, kwa Chiphazi, ku Mpalale, kwa Ndemela, kwa Nthenda sakatilandira? Suja adatikankhira galimoto ulele titatitimira ku Dzalanyama kuja atangodziwa kuti uyu ndi mwana wa Angozo (mifunda ndiye inalipo yankhaninkhani koma munthu anali mchawa)?
Lero ndikamaganizira za moyo wa bambo anga chimene ndimalingalira kwambiri ndikukhala wokondwa nthawi zonse mavuto angakule maka! Chachikulu bola uli ndi moyo ndipo moyo ndi waulele. Ukadakhala wogula bwenzi ife kulibe. Chimwemwe chili mumtimamu! Umphawi supha munthu. Ngati uli ndi moyo, manja ndi miyendo uli nazo yamika Namalenga, gwira ntchito upeze chakudya lero, usakwiyire ena ngati andiwo adakulodza.
Usani mumtendere opapa. Munatiphunzitsa zazikulu!
Subscribe to:
Posts (Atom)