Wednesday, February 6, 2013
Madala: Mphawi Wachimwemwe
Kodi ndi chiyani chimakupatsani chimwemwe m'moyo mwanu? Chuma? Ntchito? Mkazi? Mwamuna? Maphunziro? Nzeru? Anzanu? Chiyani? Aliyense ali ndi chinthu chake chimene chimamupatsa chimwemwe komanso chimene amadana nacho kwambiri. Ena akapata ndalama sasowa, amafuna aliyense amupatse moni ndipo adziwe kuti zinthu zikuyenda. Anthu otere akapsa m'thumba ndi nkhope yomwe imakhala ya makwingwirima. Ndalama zimabweretsa anansi. Zikatha, anansinso amathawa. Komanso nthawi zina ndalama zimabweretsa adani. Kunja kunotu kuli kaduka kapena nkhwidzi. Wina asakwete, walakwa, avala ufiti kapena umbava. "Akusolola" timatero! Moyo wa masiku ano ndi wovuta, popanda ndalama, dziko limayima, ulemu umatha. Angakulemekeze ndani ulibe makobidi? Umasanduka chitselekwete! Koma bwanji ukangosanja? "Yes wamkulu, Zoona abwana, eetu achikulire, shuwatu big" mayina mbwee chifukwa cha ndalama. Koma kodi munthu angakhale wosangalala popanda ndalama?
Enafe tidakulira m'mavuto oposa a Majoti. Nkhani ya Majoti ndi yopeka koma yathu ndiyolula ndithu! Mutha kukamba za mavuto amtundu uliwonse amene munthu padziko lapansi pano amakumana nawo. Tadutsamo. Tatulukamo. Mukamationa kusalalaku sikuti tidakulira ku Nyambadwe! Ngakhale kwa Ntopwa kumene sikungayandikireko! Koma chinsinsi cha Mulungu amachidziwa ndani? Thupili sikuti ndi chambiko chalerochi. Ndilobadwa nalo. Takula nalo. M'mavuto omwewo. Koma chinthu chimodzi chimene ndidakula nacho ndicho kupeza chimwemwe m'mavuto! Simkuluwiko!
Umphawi supha munthu! adatero madala! adalasa penipeni. Bwenzitu enafe titatsogola. Malemu Opapa (madala mzimu wanu uwuse mu mtendere), ndiye chitsanzo chabwino cha munthu wosangalala pamavuto, pamtendere. Simisala. Koma kusalitsanza dziko. Kwa anthu amene amatidziwa bwino kubanja kwathu, kuseka sitiumira, ndichizolowezi. Kodi ndimayesa kuseka ndiulele, sochita kugula! Ndikumbuka masiku amenewo tikukula, titadya mgawiwa wamadzulo opapa ndi omama otafatsa kutilakatulira nthano za pa ubwana wawo, za ku sukulu, za ku Joni.. ife tikuseka chikhakhali. Uku ndiko kudali kukhala kwawo, kukula kwathu. Kuseka sikunkalira ndalama. Osati kuseka kwa masiku ano kopemphera khobidi!
Lero ndapukwa opapa: Richman Bwanali Kadango kwawo ku Chitundu kwa Che Tambala m'mudzi mwa a Chawala. Myawo wapaphata kukakwatira mchewa wa ko Mbuna ku Mpenu ko Mazengera ndikusiya Chisilamu n'kuyamba kudya kapado, mbewa, kupapira masese nkukathera mu Utimiki wa Dutch! Nthawi zina makolo akamapereka mayina kapena tikamadzipatsa mayina kaya chimakhala chiyani. Inetu bambo anga pobadwa anapatsidwa dzina loti Che Madayika. Koma atakula andziwika ndi dzina loti Richman! Kaya anali matemberero kaya. Anafa osauka. Koma wosangalala, wonjoya. Bambo anga atasiya sukulu anapita ku Joweni kukasewenza ku mgodi. Pobwera kumeneko ndipamene ankabwera ko Mbuna kenako nkukayamba ntchito ku Chongoni, ku nkhalango, ife nkumabadwa. M'banja mwathu tilipo ana asanu ndi anayi, onyamata osanu ndi mmodzi ndi otsikana otatu. Tonse tilipo. Anaigwiratu makolo. Koma sizinali zachibwana kusamalira mbumba yonseyi. Madala anali munthu wolimbikira ndi wogwiragwira. Kaya ntchito zinazi anazidziwa bwanji kaya? Kaya inali mphamvu ya uchawa kaya? Komatu ankatha chilichonse: kusoka, kusema, kuluka, kukhoma! Chilichonse chochita ndi manja. Mgaiwa ukapezeka magwero ake anali amenewa. Tikavala nkhani yake inali yomweyo. Luso lina tinaphunzirako - koma izi n'zatsiku lina. Analipo masiku owawitsa ndithu nthawi imeneyo. Kudikira madala kuti abweretse chimanga kapena ufa mpaka pakati pa usiku, tulo titachita chipongozi, nkhani zitatha, m'mimba mukubangula. Akafika munthu wamwamuna khosi litalowa mkati ndi chibinyira, kusaukira mbumba nkumati adandaula, ayi ndithu! Ayambepo kukuyalirani nthano za zimene waziona tsikulo, inu njala yonse kutha nkuseka! M'mawa sikuti agonereza ayi, buli wa kuntchito! Akasakenso. masiku n'kumapita, ana nkumakula.
Madala anali ndi anzawo ankhaniankhani! Akakhala pagulu, kwawo kunali kuseka ndi kuseketsa. N'kuti kulibe anzawo? Sianzawo a ku Mchinji aja adakonzetsa thupi lawo kuti lisaonongeke pa 20 July paja? Sitinalandire ulemu ndi mphatso kwa anzawo chifukwa cha kucheza kwawo? "Atate wanu nanzanga zedi, timacheza zedi anga munthu ni mphwake" ankaterotu anzawo. Ukapita kukawayendera ku Mchinji uko adasamukira atapuma pantchito amakuyendetsa benchi iliyonse mumsika kukuonetsa kwa anzawo, "mwana wanga wa ku Zomba uja ndi ameneyu". Palibe chimene chinkawasangalatsa madala koposa kunyadira ana awo. Kodi sitinapeze malo chifukwa cha anzawo? Kodi lero ku Mchinji sikwathu chifukwa cha anzawo? Kodi lero kuti tipite ku Chongoni, kwa Kankhomba, kwa Chiphazi, ku Mpalale, kwa Ndemela, kwa Nthenda sakatilandira? Suja adatikankhira galimoto ulele titatitimira ku Dzalanyama kuja atangodziwa kuti uyu ndi mwana wa Angozo (mifunda ndiye inalipo yankhaninkhani koma munthu anali mchawa)?
Lero ndikamaganizira za moyo wa bambo anga chimene ndimalingalira kwambiri ndikukhala wokondwa nthawi zonse mavuto angakule maka! Chachikulu bola uli ndi moyo ndipo moyo ndi waulele. Ukadakhala wogula bwenzi ife kulibe. Chimwemwe chili mumtimamu! Umphawi supha munthu. Ngati uli ndi moyo, manja ndi miyendo uli nazo yamika Namalenga, gwira ntchito upeze chakudya lero, usakwiyire ena ngati andiwo adakulodza.
Usani mumtendere opapa. Munatiphunzitsa zazikulu!
Subscribe to:
Post Comments (Atom)
No comments:
Post a Comment