Friday, April 4, 2014
Mikatoni: Mnzanga Wakalekale
Ine paja ndinafotokoza kale kuti kwathu n'ko Mbuna. Chinthu chimodzi chimene chimandipukwitsa kwathu kapena kuti ndizikonda ndikunyadira kwathu ndi anzanga ndi abale amene ndinakula ndi kusewera nawo limodzi.Ngakhale kuti chaka chimene ndinakhalako kwathu ndili wamkulu ndi wozindikira ndi pamene ndinali ndi zaka 12 zakubadwa ndipo ndipahunzirako sukulu materemu awiri, ndili ndi anzanga ambiri amene ndimawakumbukira mpaka lero. Ena a m'mudzi wathu komanso a midzi ina makamaka amene ndinadziwana nawo ku sukulu kwa Kaundama.
Miston Chambadzana ndi mnzanga wakalekale. Iyeyu ngakhale sindinauzidwe kuti pali ubale wanji ndi ine koma ndimadxiwa kuti ndi mbale wanga ndithu chifukwa nyumba yawo inali kuseli kwa nyumba yathu panthawi imeneyo ndipo ife timadziwa kuti anthu onse a mudzi umodzi ndi pachibale. Amayi ake a Mistoni anamwalira iye ali wamngóno kwambiri ndipo enafe sitinawaone kapena kuwadziwa. Malinga ndi mwambo wa chikamwini, chifukwa chakuti bambo a Mistoni sanali a m'mudzimo atamwalira amayi ake iwo anachoka kubwerera kwawo. Choncho Mistoni anakula ngati mwana wamasiye ngakhale kuti bambo ake analipo. Mistoni anakula ndi achemwali ake akulu. Koma mwatsoka anamwaliranso mwadzidzidzi Mistoni ali wachichepere.
Akuluakulu akamati umphawi siupha, ndimakhulupirira popeza ndinaonera Mistoni. Ndipo moyo wa Mistoni umandizizitswa kwambiri ndikumasinkhasinkha kuti kodi nçhifukwa chiyani Namalenga amalola kuti anthu ena azivutika moyo wawo onse pamene ena akukhala mu ulemerero. Chimene chimandisangalatsa ndiponso chimene ndimaphunzirapo kuchokera kwa moyo wa Mistoni ndi kusadandaula ndi mavuto. Masiku ano timamva za anthu akulowa m'mavuto ena aakulu monga lkulowerera chifukwa cha umphawi. Ena amalorera kuchotsa moyo wawo chifukwa cha mavuto. Koma Mistoni snalabadire za mavuto ake ndipo anali munthu wachimwemwe tsiku lililonse. Akadzuka sanali kudziwa kuti kodi tsikulo adya chani kapena avala chani. Mistoni ankadya chililichonse. ndikuti chilichonse chimene wachipeza. Komatu sanali wa misala. Mutamuona Mistoni akudya kamphiripiri wamuwisi wodzadza chikhato chake simukanaona kawiri. Koma tsabola anali chakudya cha Mistoni. Mistoni akalawa nsima anali deya wopemphetsa m'makomo mwa anthu kapena kudyana nawo kwa amene amuyitanira.
Mistoni ndiye anali mnzanga wosewera naye mpira komanso phada. pakhomo pawo panali njira komanso bwalo lomwe ana ambiri tinkasewerapo. Nthawi yovuta kwambiri imene inkamusautsa Mistoni chifukwa cha mnyozo wa anzakefe inali yosewera mpira. Tikakhalapo ana ambiri ofukwa kusewera chikumasi (chikulunga) tinkagawa matimu awiri. Kuti tithe kuzindikirana tinkagwirizana kuti timu ina ivule malaya. Amene anali timu ya Mistoni ankalimbikira kuti iwo ndi amene avule malaya. Mistoni sankakhala ndi zovala nthawi zambiri makamaka malaya. Ankangoyenda mimba pamtunda. Nthawi zina ankakoleka kansalu ka kolala ndi momangamo mabatani kamene kanali ngati kotsalora malaya onse atatha. Sindidziwa ngati pogona ankavula koma tsiku lililonse amapezeka nako mkhosi. Ikafika nthawi yampira tinkamuvulitsa kuti tizitha kumuzindikira. Chinali chipongwe chabe ndipo ambuye azitikhululukira. Komatu Mistoni sankatekeseka nazo, iye kwakwe kunali kumwetulira ndipo ankachotsa ndikukayika potero, mpira ukatha nkukavalanso. Masiku nkumapita. Masiku amenewo a mishoni ankathandizako ana amasiye ndi zovala. Kawirikawiiri Mistoni ankalandra jekete lalikulu. Ndiye lomwelo limakhala gombeza lomwelo malaya. Tikamasewera mpira ngati ali mu timu yavala malaya ndiye kuti Mistoni ankasewera ali ndi jekete m'thupi.
Koma monga ndafotokozera zimenezi sizinkamukhudza Mistoni. Tinkatha kulisintha dzina lake kukhala Mikatoni kapena Mikabodo koma iye sankalabada. Mistoni anayamba sukulu ngakhale sanapite nayo patali. Koma anadziwa kulemba ndi kuwerenga motero kuti anachitanso maphunziro a Sunday school ndi kalasi nabatizidwa. Ndimahulupirira kuti chinthu chinyaditsa kwambiri m'moyo mwake chinali kumangitsa ukwati woyerea. Kwathu masiku amenewo ukwatitsa ukwati wa pa mpingo chinali chinthu chamtengo wapatali. Anyamata ambiri ankalolera kupita ku maesiteti ku Kasungu kwa a Khondowe kuti akapeze ndalama yodzachitsira ukwati. Ndipo Mistoni anachita chimodzimodzi mpaka anakwatitsa ukwati wake ku Nkhoma madyerero anachitikira kwawo kwa mkazi m'mudzi mo Mphonde. Posachedwapa nditakumana naye anandiuza kuti ukwatiwu unatha moti anali kuwunguza kamsoti kena koti atenge chifukwa akuvutika kukhala yekha.
Ine ndi Mistoni timacheza ndithu. Ngakhale kuti umphawi sunamuchokee kwenikweni Mistoni amadziwabe kuti ine ndi mnzake wakalekale. Akangomva kuti ndabwera amathamanga kuti mwina apeze ya sopo. Chinthu chimene chimandisangalatsa ndi chakuti sanatengeke ndi khalidwe lomwa mowa kapena kusuta fodya. Mistoni amapempherabe mpaka pano ndipo anandiuza kuti ndi mtsogoleri. Koma chisamaliro chapathupi ndiye chimamuvutirapo moti tikakumana chokhacho ndi chimene chimasonyeza kusiyana kwathu. Koma Mikatoni ndi mnzanga ndithu wakalekale!
Kwathu
Muno m'tawuni timangowonana. Anthufe tonse tli n'kwathu. Ena kwawo n'kumagomo, ena kwawo n'kunyanja, ena kwawo n'kuthegere, ena kwawo n'kuntherero kwa jiko, ena kwawo n'kumusha, ena kwawo n'kuthoni. Nthawi zina kwawo kwa munthu kumapanga munthu kuti akhale momwe alili. N'chifukwa chake nthawi zina ukadabwa ndi momwe akuchitira zinthu kapena momwe munthu wina akuyankhulira timafunsa ndithu kuti kwanu n'ku? Nanga inu kwanu n'ku. Ine kwathu n'kumsewu, ko Mbuna.
Nkhani ya kwanu pena pake imakhala yovuta pa zifukwa zosiyanasiyana. Anthu amasintha kwawo pa zifukwa zosiyanasiyana: kusamuka, maphunziro, ntchito, ndale, malonda, banja ndi zina zambiri. Ife zonsezo tadutsamo koma kwathu sikunasinthe. Kwathu n'ko Mbuna. ndipotu kwanu ndi kwanu, ngakhale kutaoneka kosasangalatsa m'maso mwa anthu ena, kwanu ndi kwanu basi.
Ine kwathu n'ko Mbuna, ku Mpenu ko Mazengera ku Nkhoma. Mudzi wathu uli m'mphepete mwa msewu waukulu wochokera ku Lilongwe kupita ku Blantyre pa mtunda wa makilomita 40 kapena mamayilosi 25 kuchokera mumzinda wa Lilongwe. Mudzi wathu wayandikana ndi midzi ina monga Bokonera, Mng'ona ndi Mdzinga. Kukhala pafupi ndi msewu waukuluwu ndi chinthu chimodzi china chimene timachinyadira kwambiri pa zifukwa zambiri. Mwachitsanzo, mayendedwe sizovuta. Kungokhala m'mbali mwamsewu nthawi ina iliyonse upeza galimoto yokwera kupita komwe ukufuna. Kulibe kabaza kwathu! Chokhacho ndimachinyadira kwambiri. Tikafuna kukamba za malonda a mumsewu ndiye pali nkhani koma siyabwalo lino!
Mwina ena n'kumangomangonena za kwawo chikhalilenicho kwawoko sanakhaleko. Ife kwathu tinakhalako ndipo tikukudziwa bwino. Ine kwathu ndinakhalako ndithu ndipo ndimapitako zedi. Pa ubwana wanga ndinakhalako pamene ndinaphunzira sukulu, sitanadede 1 kenako pamene ndinali sitandede 5. Sitandede 1 ndinaphunzira pa sukulu ya Kaundama yomwe masiku a m'mbuyomo makamaka cha m'ma 1980 inali yotchuka kwambiri ndikusankhitsa ana opita ku ku sekondale. ndi zinthu zochepa zimene ndimazikumbukira pamene ndinali mu Sitandede 1 chifukwa mwina ndinali wachichepere. Koma pamene ndinabwereranso kumudzi kukaphunzira Sitandede 5 pali zinthu zambiri zimene zinakhazikika m'mutumu. Zina ndi monga anzanga amene ndinkasewera nawo kunyumba komanso kusukulu, zakudya ntchito komanso zosangulutsa zina monga zilombo! hahahahahaha!
Pali anzanga ambiri amene ndinadziwana nawo nthawi imeneyo amene ngakhale pano timacheza kwambiri. Mnzanga woyamba ndi malemu Tenderetu (Sosten)... mzimu wake uziusa mumtendere. Za iyeyu ndinalemba kale. Tenderetu anali msuwani wanga amene anandilandira nditangofika kumudzi. Kuchokera tsiku limenelo tinkayenda ngati inswa. Ndidzamukumbukira mpaka kale Tenderetu!
Amayi anga ndi Omama (mukafika kwathu adzakuwuzani kuti Omama ndani. Olipo omodzi basi). M'bele mwawo anabadwa ana asanu, amuna atatu, akazi awiri (Omama ndi Omayi). Panopa amayi anga amakhala ku Mchinji pa Boma m'mudzi mwa Robert. Koma ngakhale makolo anasamukira ku Mchinji mçhaka cha 1995, kwathu ndi ko Mbuna ndithu. Ngakhale mudzi wathu sukuoneka kusintha kapena kutukuka, ndimanyadirabe kuti ndiko kwathu ndipo ndimakhulupirira kuti sindikadakhala momwe ndilili chipanda kubadwira ko Mbuna.Tikafika kwathu amati kwabwera Oyaliki kapena o ku Zomba. Kwathu ko Mbuna. Inu kwanu nku?
Subscribe to:
Posts (Atom)