Friday, April 4, 2014
Mikatoni: Mnzanga Wakalekale
Ine paja ndinafotokoza kale kuti kwathu n'ko Mbuna. Chinthu chimodzi chimene chimandipukwitsa kwathu kapena kuti ndizikonda ndikunyadira kwathu ndi anzanga ndi abale amene ndinakula ndi kusewera nawo limodzi.Ngakhale kuti chaka chimene ndinakhalako kwathu ndili wamkulu ndi wozindikira ndi pamene ndinali ndi zaka 12 zakubadwa ndipo ndipahunzirako sukulu materemu awiri, ndili ndi anzanga ambiri amene ndimawakumbukira mpaka lero. Ena a m'mudzi wathu komanso a midzi ina makamaka amene ndinadziwana nawo ku sukulu kwa Kaundama.
Miston Chambadzana ndi mnzanga wakalekale. Iyeyu ngakhale sindinauzidwe kuti pali ubale wanji ndi ine koma ndimadxiwa kuti ndi mbale wanga ndithu chifukwa nyumba yawo inali kuseli kwa nyumba yathu panthawi imeneyo ndipo ife timadziwa kuti anthu onse a mudzi umodzi ndi pachibale. Amayi ake a Mistoni anamwalira iye ali wamngóno kwambiri ndipo enafe sitinawaone kapena kuwadziwa. Malinga ndi mwambo wa chikamwini, chifukwa chakuti bambo a Mistoni sanali a m'mudzimo atamwalira amayi ake iwo anachoka kubwerera kwawo. Choncho Mistoni anakula ngati mwana wamasiye ngakhale kuti bambo ake analipo. Mistoni anakula ndi achemwali ake akulu. Koma mwatsoka anamwaliranso mwadzidzidzi Mistoni ali wachichepere.
Akuluakulu akamati umphawi siupha, ndimakhulupirira popeza ndinaonera Mistoni. Ndipo moyo wa Mistoni umandizizitswa kwambiri ndikumasinkhasinkha kuti kodi nçhifukwa chiyani Namalenga amalola kuti anthu ena azivutika moyo wawo onse pamene ena akukhala mu ulemerero. Chimene chimandisangalatsa ndiponso chimene ndimaphunzirapo kuchokera kwa moyo wa Mistoni ndi kusadandaula ndi mavuto. Masiku ano timamva za anthu akulowa m'mavuto ena aakulu monga lkulowerera chifukwa cha umphawi. Ena amalorera kuchotsa moyo wawo chifukwa cha mavuto. Koma Mistoni snalabadire za mavuto ake ndipo anali munthu wachimwemwe tsiku lililonse. Akadzuka sanali kudziwa kuti kodi tsikulo adya chani kapena avala chani. Mistoni ankadya chililichonse. ndikuti chilichonse chimene wachipeza. Komatu sanali wa misala. Mutamuona Mistoni akudya kamphiripiri wamuwisi wodzadza chikhato chake simukanaona kawiri. Koma tsabola anali chakudya cha Mistoni. Mistoni akalawa nsima anali deya wopemphetsa m'makomo mwa anthu kapena kudyana nawo kwa amene amuyitanira.
Mistoni ndiye anali mnzanga wosewera naye mpira komanso phada. pakhomo pawo panali njira komanso bwalo lomwe ana ambiri tinkasewerapo. Nthawi yovuta kwambiri imene inkamusautsa Mistoni chifukwa cha mnyozo wa anzakefe inali yosewera mpira. Tikakhalapo ana ambiri ofukwa kusewera chikumasi (chikulunga) tinkagawa matimu awiri. Kuti tithe kuzindikirana tinkagwirizana kuti timu ina ivule malaya. Amene anali timu ya Mistoni ankalimbikira kuti iwo ndi amene avule malaya. Mistoni sankakhala ndi zovala nthawi zambiri makamaka malaya. Ankangoyenda mimba pamtunda. Nthawi zina ankakoleka kansalu ka kolala ndi momangamo mabatani kamene kanali ngati kotsalora malaya onse atatha. Sindidziwa ngati pogona ankavula koma tsiku lililonse amapezeka nako mkhosi. Ikafika nthawi yampira tinkamuvulitsa kuti tizitha kumuzindikira. Chinali chipongwe chabe ndipo ambuye azitikhululukira. Komatu Mistoni sankatekeseka nazo, iye kwakwe kunali kumwetulira ndipo ankachotsa ndikukayika potero, mpira ukatha nkukavalanso. Masiku nkumapita. Masiku amenewo a mishoni ankathandizako ana amasiye ndi zovala. Kawirikawiiri Mistoni ankalandra jekete lalikulu. Ndiye lomwelo limakhala gombeza lomwelo malaya. Tikamasewera mpira ngati ali mu timu yavala malaya ndiye kuti Mistoni ankasewera ali ndi jekete m'thupi.
Koma monga ndafotokozera zimenezi sizinkamukhudza Mistoni. Tinkatha kulisintha dzina lake kukhala Mikatoni kapena Mikabodo koma iye sankalabada. Mistoni anayamba sukulu ngakhale sanapite nayo patali. Koma anadziwa kulemba ndi kuwerenga motero kuti anachitanso maphunziro a Sunday school ndi kalasi nabatizidwa. Ndimahulupirira kuti chinthu chinyaditsa kwambiri m'moyo mwake chinali kumangitsa ukwati woyerea. Kwathu masiku amenewo ukwatitsa ukwati wa pa mpingo chinali chinthu chamtengo wapatali. Anyamata ambiri ankalolera kupita ku maesiteti ku Kasungu kwa a Khondowe kuti akapeze ndalama yodzachitsira ukwati. Ndipo Mistoni anachita chimodzimodzi mpaka anakwatitsa ukwati wake ku Nkhoma madyerero anachitikira kwawo kwa mkazi m'mudzi mo Mphonde. Posachedwapa nditakumana naye anandiuza kuti ukwatiwu unatha moti anali kuwunguza kamsoti kena koti atenge chifukwa akuvutika kukhala yekha.
Ine ndi Mistoni timacheza ndithu. Ngakhale kuti umphawi sunamuchokee kwenikweni Mistoni amadziwabe kuti ine ndi mnzake wakalekale. Akangomva kuti ndabwera amathamanga kuti mwina apeze ya sopo. Chinthu chimene chimandisangalatsa ndi chakuti sanatengeke ndi khalidwe lomwa mowa kapena kusuta fodya. Mistoni amapempherabe mpaka pano ndipo anandiuza kuti ndi mtsogoleri. Koma chisamaliro chapathupi ndiye chimamuvutirapo moti tikakumana chokhacho ndi chimene chimasonyeza kusiyana kwathu. Koma Mikatoni ndi mnzanga ndithu wakalekale!
Subscribe to:
Post Comments (Atom)
No comments:
Post a Comment