Wednesday, December 10, 2008

Chitipa, Edeni wa ku Malawi





Pa Chichewa pali mawu akuti khotekhote ngwa njira kwaloza mtima nkomweko. Mawuwa ndimawakumbuka kwambiri panthawi imene ndili paulendo wopita kwathu ko Mbuna kapena kukaya ku Borero. Nthawi zambiri ndikaganizira mitunda imene ndimayenera kuidutsa kukafika kumene ndikupitako mphwayi ndi nkhawa zimandigwira. Koma ndikaganizira kwambiri zomwe ndikukachita komwe ndikupitako ndimakhala ndichilimbikitso. Ndikamapita ko Mbuna ndimayamba kudziwa kuti ndafika ndikayandikira pa Linthipe 1 chifukwa kaphiri ka kwathu ka Bathe kamaonekera monga adaimbira nyimbo ija. Zikangotero ndimayamba kuganizira zomwe ndikapeze ndikafika kumudziko. Ngati ndikukangowona anthu ndimayamba kuganizira za nkhuku yachikuda imene akandiphere. Koma ngati ndikupita kumaliro, tsozi limayamba kutsika.

Boma la Chitipa ndi malo amene ndakhala ndikumva mbiri yake kuchokera kwa anthu ena, pawayilesi komanso manyuzipepala. Chokhumudwitsa ndichakuti nthawi zambiri mbiriyi imakhala yosasangalatsa. Chithunzithunzi chimene chimaperekedwa ndichakuti ku Chitipa ndi kumalo kovuta kufikako chifukwa cha msewu, komanso kuti ndikotsalira chifukwa kulibe zinthu zambiri zamakono. Choncho sindinkakhala ndi chilakolako chopitako kumalowa. Koma tsiku lina mwayi udafika ndipo ndinalimba mtima kuti ndikaonako ku Chitipa.

Unali ulendo wokagwira ntchito ya kafukufuku wa ziyankhulo. Tinafika pa Karonga cham'ma 5 koloko madzulo. Titapuma pang'ono tinauyamba wa ku Chitipa. Inali nthawi yakuti mvula yangosiya kumene, m'mwezi wa April kotero kuti m'malo ena munali chinyezi. Kuyenda kwake kunali kwa pang'onopang'ono chifukwa malo ambiri anali ataonongeka. Mu galimoto yathu tinali ndi anthu awiri amene anali mbadwa za ku Chitipa ndipo anali kutisonyeza malo osiyanasiyana ndi mbiri zake panthawi yonse yaulendowu. M'njiramu tinadutsa galimoto zingapo zimene zinatchona m'matope kapena kuwonongeka kumene. Mdima unagwa koma tinali tisanayende mtunda wautali. Mantha ndi nkhawa zinayamba kutigwira makamaka poganizira kuti mwina nafe sitikanatha kukafika tsiku lomwelo. Komanso tinali ndi nkhawa kuti pofika ku Chitipa sitikapeza malo ogona. Ngakhale unali usiku timatha kuona kuti tikudutsa m'nkhalango zowirira kwambiri komanso m'mapiri. Ena anayamba kugona. Kuyenda kwa usiku ndikovuta kwambiri chifukwa suwona kumene ukupita ndi kumene ukuchokera. Patatha maola angapo tinauzidwa kuti tsopano tatuluka m'boma la Karonga ndipo talowa mu Chitipa. Nkhawa yathu inakula. Ambiri tinaganiza zongogona kuti mwina tisamve kuwawa ndi kutalika kwa ulendo.

Kenana tinauzidwa kuti tsopano tatsala pang'ono kufika. Apa panali pamphambano ya msewu wopita ku Misuku. Tinauzidwanso kuti ku Misuku ndikutali ndipo ndikovuta kupitako. Magetsi anaoneka kuwala. "Kuteroko kuli magetsi?" m'modzi wa ife anafunsa modabwa. Sitinayembekezere kuti ndi momwe anthu amakambira za ku Chitipa komanso ndi mtunda umene tinayenda munkhalango uja tingapeze magetsi. Posakhalitsa tinafika paboma. Ndi maso a usiku kunali kovuta kuti tikhale ndi chithunzithunzi chamalowo. Mwamwayi tinapeza malo ku Do or Die. Tinagona mpaka m'mawa. M'mawa ndinamwa thiyi wa masikono chifukwa anatiuza kuti Buledi kulibe. Mumtima ndinangoti tafikadi ku Chitipa. Tidya chilichonse chimene chipezeke.

Kenaka tinayamba kuyang'ana malo ena abwinoko. Ena anakhalira ku Do or Die koma ena anapeza malo Ku St Kizito ndi Ku Works Guest House. Masana a tsiku limenelo tinayamba kugwira ntchito. Tinalowera chakumpoto chakumadzulo, kwa Mwenekameme. Msewu wopita ku maloko unali wolambula bwino. M'njira monse tinatha kuona kutali ndipo tinaona sese lalikulu mpaka kukafika mumtsinje wa Songwe. Tinaonanso timapiri ta mu Tanzania ndipo tinauzidwa kuti ku Tanzania ndi pafupi. Titafika pa Kameme Trading Centre pomwenso panali Post Agency tinaona nyumba yosanjikizana imene bambo wina anamanga yekha. Inali nyumba yochititsa chidwi. Tinalowa m'nyumbayi mpaka muchipinda chapamwamba pomwe tinatha kuona kutali mpaka ku Tanzania. Tili pa Kameme pompo tinapita pamsika pomwe tinapeza chinaka (chikande). OOOOOh Ndinakumbuka masiku amenewo tikukhala ku Chongoni ku Dedza tikudya chikande. Ndiyetu kunali kulimbirana. Madzulo a tsiku limenelo nkhani inali ya ku Kameme.

Tsiku lotsatira ife tinapita kwa Mwenemwaulambiya pamene gulu lina linagwira ntchito malo ozungulira paboma. Kwa Mwenemwaulambiya ndi chakumpoto chakummawa. Pochoka ku boma mumatenga msewu wa Karonga ndikukhotera chakumpoto pa .... Choyamba kundipatsa chidwi chinali mitengo ya kanjedza imene inamera mosangalatsa m'madambo a m'derali. Titayenda tinadutsa pa... pamene panali msika. Tinagwirizana zopita kaye kwa Mwene ndipo kuti pobwera tidzayime pamsikapo ndikugula chinaka china. Nyumba ya Mwenemwaulambiya ili m'tsinde mwa phiri ndipo m'munsi mwake muli kamtsinje ndipo tsidya linalo kulinso phiri la mitengo yothithikana. Malo osangalatsa kwambiri. Titacheza ndi amfumu tinapitirira ulendo wathu mpaka pa Ifumbo (pali Post Office, koma tinapeza Police itatsekedwa). Tinayenda m'midzi yozungulira derali mpaka tinafika pa sukulu ya .... yomwe ili m'malire ndi Tanzania komanso mapiri a Misuku. Kumeneko tinacheza ndi aphunzitsi komanso ana a sukulu ndipo anthu am'derali amayankhula Cindali. Ku Kameme kuja anthu ambiri amayankhula Cinyiha. Pobwerera tinayima pa Ifumbo Police Unit ndikudya chinangwa chophika ndi mazira chomwe mmodzi mwa anzathu a ku Chitipa aja anaphika kunyumba kwa makolo ake. Titadya tinagwira ntchito m'midzi yozungulira mpaka madzulo tinafika pamsika paja pomwe tinagula chinaka, mapeyala okoma zedi, nthochi ndi zakudya zambiri. Pomalizira penipeni tinadzera kunyumba kwamnzathu wina kumene amayi ake anatizulira chinangwa. Tinali osangalala kwambiri tsiku limenelo chifukwa tinaona mtima wowolowa manja wa anthu a ku Chitipa. Komanso tinamva zinenero zosiyanasiyana: Cinyiha, Cilambya, Cinamwanga, Cindali, Cibemba ndi zina.

Tsiku lotsatira tinalowera mtunda wa ku Wenya makamaka ku Chinsenga, Malawa Ibughulira ndi malo ena. Ibugulira ali pafupi ndi malire a dziko la Malawi ndi Zambia msewu umene inkadutsa basi ya Nakonde yodzera mu Nyika. Kumeneko amayankhula Cinyika chomwe chimafananako ndi Cinyiha cha ku Kameme koma kusiyana kwake ndikwakuti Cinyika chimasakaniranapo ndi Citumbuka.

Titafika pa Malawa sukulu tinapita kunyumba kwa amfumu yomwe inali mtsindetsinde mwa mapiri a Mafinga. Mafinga ndi mapiri okongola kolapitsa. Awa ndi mapiri amene kumachokera madzi amene anthu a m'boma la Chitipa amamwa, madzi ozizira kwambiri. Tinayenda m'midzi yambiri komwe tinapeza madzi a m'mipope, zinthu zomwe sitinkayembekezera kuzipeza ku Chitipa. Tinamwa madzi apampopi m'mudzi mwa Malawa. Tikucheza ndi anthu m'mudziwu kunabwera mvula yamatalala. Tinadzizdimuka kwambiri popeza tinkaganiza kuti mvula inali itasiya. Titayenda mobwerera tinafika pa Chinsenga, malo okongola kwambiri. Nditapatsidwa mwayi wosankhanso kwathu, ndingathe kusankha ku Chinsenga. Chinsenga ndi malo amene ali m'munsi mwa phiri la Mafinga, nyengo yake ndi yozizira, nthaka ndi yachonde ndipo pali mitengo yabwino zedi. Palinso Police ndi tchalitchi zokongola. Pamenepa ndi pamene pali mphambano yopita ku Wenya ndi Nthalire. Chosangalatsa kwambiri ndi malowa ndichakuti ndi malo amene pali anthu oyankhula Cinyika ndi Citumbuka motero kuti kayankhulidwe kake kamakhala kosakaniza ziyankhulo ziwirizi. Pachifukwachi anthuwa akuti amayankhula Citumbunyika. Sindinafune kuchoka malo amenewa ndipo pobwerera tinayima mumsewu ndikumangosirira mapiri a Mafinga. Chilengedwe chokoma!


Madzulo a tsiku limenelo kunali kukambirana za malo amene tikagwire ntchito tsiku lotsatira. Panali malo awiri: Misuku ndi Nthalire. Tinauzidwa kuti malo onsewo anali ovuta kufikako komanso malo ogona ndi ovuta. Tinauzidwanso kuti sitikanatha kupita ku Misuku ndi ku Nthalire ndikubwerako tsiku lomwelo chifukwa konseko ndikutali kuchokera paboma. Tinayenera kukagona komweko. Ine ndinasankha kupita ku Misuku. Tinauzidwa kuti kulibe network choncho sitidzatha kuyankhula ndi anzathu panthawi yonse tidzakhale kumeneko. Tinanyamuka masana a tsiku limenelo wa ku Misuku anzathu ena wa ku Nthalire. Gulu lina linatsala paboma. Tinafika pamtsinje wina. Tinaima ndikusukusula m'maso. Kenako tinayamba kukwera mapiri a Misuku ndikudutsa munkhalango zokongola. Tinadutsa malo ambiri ochititsa chidwi. Pena tinali kutsika galimoto ndikumangowona chilengedwe chokongola: Mitengo, mapiri, zigwa, mitsinje. Tinaima pa Kawotola pamene tinachezapo ndi anthu ena. Iwowa amayankhula Cisukwa. Tinaona ng'ombe zomangirira mabelu zikudziyendera m'thengo. Kenaka tinafika m'minda ya khofi yomwe inaoneka mochititsa chidwi kwambiri. Titayenda tnaima pa nkhalango ya Wiringi (nkhalango yowirira kwambiri(rainforest)). Tinalowa m'nkhalangoyi kukatchola zipatso za Mafwisa. Ooooh! Ngati tisatuluke mnkhalangoyi. Kenaka tinayamba kutsetserekera m'Misuku! Zoti ndi Malawi yemweyu simungakhulupirire, malo ochititsa chidwi. Kunali kukwera, kutsika, kukwera kutsika. Tinafika ku nyumba yogona alendo ya Coffee Growers Association kumene tinapeza malo okongola kwambiri ogona. Madzi otenthetsa pamagetsi analipo. Ena anagona kumahostel a pamalopa. Chakumadzulo tinasewera mpira wokulunga ndikukasamba. Madzulo tinapita kunyumba ya mayi ndi bambo ena amene anatiphikira chakudya chifukwa kunalibe malo odyera. Tinapanga ubale ndi banjali kotero kuti pa masiku atatu amene tinakhala ku Misuku tinali kudya kunyumbako.

M'mawa tinapita ku Nyumba kwa Mwenemisuku, kutsetserekera chakumadzulo. A Mwene anali onyadira kuti tinafika kudera kwawo ndipo anatiuza kuti dera lawo limalandira alendo ambiri ochokera kunja chifukwa chakukongola kwa malowa. Pochoka tinalandira vibwaira va nthochi, chinangwa, nzimbe, mtedza ndi zakudya zosiyanasiyana. Koma kufika m'makomo chinali chovuta kwambiri chifukwa nyumba zili m'tsidya kotero kuti kufika kumeneko umayenera kutsetsereka ndikukwera mitunda. Koma pakutha pa masiku atatu tinali titazolowera kuyenda mothamanga komanso mowerama. Ku Misuku tinapeza kuti anthu amayankhula Cisukwa komanso Cindali. Tinapezanso nkhalango zowirira kwambiri ku Chinongo. Pobwerera tinaganiza zodzera njira zina zachidule zokatulukira ku mtunda kwa boma la Karonga. Ndiyetu kunali kutsetsereka kwambiri popeza tinali kupita kumalo otsika kunyanja. Unali msewu umene sikudutsa galimoto zambiri moti pena timaona ngati tasokera. Pamasiku onse tinali ku Misuku sitinayankhulane ndi wina aliyense pa foni chifukwa kunalibe network. Koma tinakhala mosangalala chifukwa zinthu zinali zotsika mtengo. Titayenda maola angapo tinafika pa Ngerenge m'dera la Kilupula ku Karonga. Tinangowona nyanja ili mbee. Tinasangalala kuti tafika kumene tidzatha kuyankhulana ndi kuonana ndi anzathu amene tinasiyana nawo masiku anayi apitawo. Podutsa ku Ngerenge tinaona ng'ombe ya miyendo itatu itamangiriridwa m'mabli mwa msewu.

Kunali chimwemwe chokhachokha pamene tinakumana pa Karonga. Tinauzana momwe tonse tinayendera komwe tinapita. Kunaoneka kuti aliyense anali wokondwa kwambiri. Kuchokera tsiku limenelo tinapeza chithunzithunzi chenicheni cha boma la Chitipa. Ndi boma limene chilengedwe chake sichinaonongoke, dziko lokongola, anthu ansangala ndi owolowa manja. Kuchokera pa nthawi imeneyo ndapitanso kuchitpa katatu ndipo ulendo uliwonse ndimabwera ndichimwemwe. Chitipa, Edeni wa Malawi

Malawi Dziko Lokongola






AMalawi anzanga, munthune ndimanyadira kuti ndinabadwira ku Malawi kuno. Poyamba ndinkasiririra ntakhala wakunja. Maganizo amenewa amabwera kamba kowonera kanema wowonetsa malo osiyanasiyana akunja kwa dziko lino. Makanemawa amangowonetsa zoipa zokhazokha za dziko lino ndi mayiko ena a kuno ku Africa. Koma nditayendera maboma onse a dziko lino ndinaona kuti Malawi ndi odala kwambiri kuposanso mayiko ena amene timawasirira. Kuli mapiri kunja kuno. mitsinje, nkhalango, nyama, nyumba, anthu okongola, magule (virombo), zigwa, ndi zina zambiri. Patsamba lino ndikhala ndikulembapo za malo ena amene ndidafikako m'dziko muno. Mwa malo amene amandichititsa chidwi kwambiri ndipo ndimawakonda kwambiri ndi boma la Chitipa, nyanja ya Malawi ndi phiri la Mulanje.

Tuesday, December 9, 2008

Kale tili wana

Dzulo chakumasana kunagwa mvula yamvumbi. Ndidaima pazenera la nyumba yanga nkumasuzumira kunja mwachidwi. Mwana wanga woyamba adabwera nkudzandikhalira pakhundu nkundifunsa kuti "obaba mulupenyanji?" Ndinamuyang'ana ndisanamuyankhe. Kenaka ndinati "Chivumbi." Adaoneka odabwa zedi. Ndidadziwa kuti sadazindikire chimene ndimatanthauza. Wana okulira m'thoni ongadziwe chivumbi. Ndidamulozera ndikumufotokozera za chivumbicho- mtundu wambereswa zimene zimawuluka mvula yamvumbi ikamagwa. M'gululi muli mbereswa zenizeni koma izi zimatuluka mvula ikasiya kadzuwa katawala. Komanso pali anzenzemkutu ena amati agonthamkutu, tating'onoting'ono ndipo ambiri sadya. Mvumbi ndi mvula yosakata msanga koma imagwa pang'onopang'ono. Izi zidangondikumbutsa masiku amenewo tili wana. Mvula yotere ikamagwa timatuluka m'nyumba nkumakathamanga m'madzi oyenderera kwinaku tikutola chivumbi. Pena nkumadzitereretsa dala nkumagwa m’matope. Tikamachoka kumeneko tili thope lokhalokha. Zoti wanthu omadwala ndi nyansi za m'matope tinkangakumva. Kungokhala m'nyumba osatuluka tinkangoyesa ukapolo. Nanga m'nyumba mwaudzu, modonthanso uzitanimo masana. Kumangowerenga nzengo ndi ming'alu ya zipupa basi? Kodi mumadziwa kuti kumudzi sikwenikweni anthu kukhala m'nyumba zawo masana ngati amachitira anthu mthoni? Chifukwa choyamba nchakuti mumakhala mdima (ndi angati amatsekula mazenera kuti muloweko mpweya?). Chifukwa china nchakuti m’nyumba zambiri mumakhala mopanda mipando yoti munthu nkukhalapo nkumaphwetsa mkhuto. Nanga mphasa ulimbane nayo usiku, usananso? Ndiye anthu ambiri amakonda kukhala pakhonde kapena kukacheza ku Thileding'i, kapenanso kubwalo kukagoma ntchuwa (36 godi). Titakulako pang'ono kukacha tinkapita kudambo kukadyetsa mbuzi zomayi. Kudambo tinkaphunzirako zambiri: kutumika (kukakusa mbuzi zikalowa m'munda) kuwumba ziboliboli (nyama, magalimoto, anthu, nyau...) uzimba (ziwala: khwiya, noni,chamsipu) kudya (mondokwa (tong'o)), kuyimba, kulimbitsa matupi (kunali nkhonya zongoyamba popanda chifukwa bola mbusha wamkulu walamula- tinkangolemba mzere kutsogolo kwako. Amene afafanize mzere wamnzake ndiye kuti waiyambitsa ndewu. Panalibe kuleletsa mpaka wina achimine. Mukamakapisira mbuzi madzulo, mitu ili mbu ndi nkhonya ngati munagwa paphulusa). Tinkaphunzira kupirira (kunjala, kumenyedwa, kugwira ntchito nthawi yaitali (kunalibe zokadyera masana kapena kunyamula phoso).

Nthawi yovuta inali pamene mmera watuluka. Kwathu kunali anthu ena oipa mitima amene mbuzi zikangolowa m'munda mwawo umangodziwa kuti atemako mwendo mbuzi imodzi kapena mbusha wa mbuzizo awadzola makofi. Mmodzi wa bambowa anali o Sacheuka, omayi!!!. Munthu anali mfiti uyu (alipobe). Mukangokomedwa ndi Chatani (thera) mbuzi nkukalowa m'munda mwawo umangomvera nyimbo "Zalowaa zalowaaa mo Sacheukaaa! Ndiye ngati inali nthawi yako yokakusa umangoyambako kuthamanga mtima ulu thithithi. Pofika m'mundamo mikodzo itayenderera kale. Pobwera kumeneko khutu limodzi litasiya kumva chifukwa cha makofu. Popanda sankaona msinkhu kapena chibale. Izi zinkachititsa kuti tizikhala tcheru nthawi zonse powopa kukunthidwa. Nthawi yosangalatsa inali chimanga chikacha. Panalibenso zonyinyirika kukatsekulira mbuzi kukacha. Ikangofika 10 kaloko aliyense amalowera kumunda komake kapena kogogo wake kukatchola mondokwa. Tsiku limenelo mukangochiumira mtima chimanga aliyense amatha kukatchola 10 kapena 15 nkudzaunjika pamulu. Nkhuni zake tinkakhumula zithima zakhonje zowuma (kale kwathu kunali khonje wambiri ndipo amatulutsa mitengo imene ankamangira madenga ndi nkhokwe. Lero adachepa). Ndiye tikausonkha moto uja timaponyapo chimanga chija chosasenda. Chimapsa mophikika. Ndiyetu kumakhala kutafuna onomuna nyimbo zili pakamwa (Tong'o tong'o adapita tong'o, tong'o tong'o tong'o bwi wang’ana kuno wesa nkugaira) apa kunali kusililitsa amene sanakathyole kwawo chifukwa chakuti sichinache kapena omamuletsa makolo ake. Kunalibe zogawana! Kukamada kumangoti kwaderanji. Ukafika kunyumba nkupeza mkhwani wothira chiluwe ndi chinyenyero kapena kholowa wophikira matsukwa otamuphikira deya, umangodziwa kuti usku uno ndi ng'oma zokhazokha( ndikamvetsera nyimbo yonyamata onyembanyemba ya ‘mbatata ng'oma” ndimangoseka). Zakudya zina zinali mango. Lekani! Tinkayambira anthete odyera mchere. Koma omiyako okangodziwa kuti unatapa mchere, pobwera kumeneko umapeza otakupatulira ndiwo zako zopanda mchere! Makolo masiku amenewo ankalangatu. Ukakana ntchito nkuthawa omanguti "dzuwa linyenga mdima usaka". Pobwera kumeneko umangodziwa kuti lero sindiinyantha (ugona palira khwelu). Koma mango akapsa ndiye kumakhala kuyendera mtengo ulionse kulawa makomedwe. Ndiye kunali kuonetsa luso logenda. Mikono kuguluka koma osatcholako ndi limodzi lomwe. Koma akafika pachimake ndiye timangokwera mumtengo momwemo ndikuyamba kuteketa okapsungu. Potsika m'menemo pansipa pali mbwee anga munali ogologolo. Popita kumudzi mukwangugeya mango okhaokha mimba zili mnzuu, m'manjamu muli matemate msuzi wa mango utayenderera mpaka m’khwapa. Ilo linali kale kumudzi. Mawa tikamba za Khisimisi

Onyamata

Ine ndine Alick Kadango Bwanali, mnyamata wa ko Mbuna ku Mpenu ko Mazengera.
Ine ndimakonda kucheza ndi kuseka kwambiri. Choncho tsamba lino ndi bwalo la nseketso komanso pa majiga podziwitsirana zochitika pakati pathu. Ndimakonda kuyenda ndikuona malo osiyanasiyana, kuwerenga komanso kuwonera kuti ndizidziwa zomwe zikuchitika kunjaku. Ndikukhulupirira kuti ticheza pabwaloli!

Onyamata AKB