Tuesday, December 9, 2008

Kale tili wana

Dzulo chakumasana kunagwa mvula yamvumbi. Ndidaima pazenera la nyumba yanga nkumasuzumira kunja mwachidwi. Mwana wanga woyamba adabwera nkudzandikhalira pakhundu nkundifunsa kuti "obaba mulupenyanji?" Ndinamuyang'ana ndisanamuyankhe. Kenaka ndinati "Chivumbi." Adaoneka odabwa zedi. Ndidadziwa kuti sadazindikire chimene ndimatanthauza. Wana okulira m'thoni ongadziwe chivumbi. Ndidamulozera ndikumufotokozera za chivumbicho- mtundu wambereswa zimene zimawuluka mvula yamvumbi ikamagwa. M'gululi muli mbereswa zenizeni koma izi zimatuluka mvula ikasiya kadzuwa katawala. Komanso pali anzenzemkutu ena amati agonthamkutu, tating'onoting'ono ndipo ambiri sadya. Mvumbi ndi mvula yosakata msanga koma imagwa pang'onopang'ono. Izi zidangondikumbutsa masiku amenewo tili wana. Mvula yotere ikamagwa timatuluka m'nyumba nkumakathamanga m'madzi oyenderera kwinaku tikutola chivumbi. Pena nkumadzitereretsa dala nkumagwa m’matope. Tikamachoka kumeneko tili thope lokhalokha. Zoti wanthu omadwala ndi nyansi za m'matope tinkangakumva. Kungokhala m'nyumba osatuluka tinkangoyesa ukapolo. Nanga m'nyumba mwaudzu, modonthanso uzitanimo masana. Kumangowerenga nzengo ndi ming'alu ya zipupa basi? Kodi mumadziwa kuti kumudzi sikwenikweni anthu kukhala m'nyumba zawo masana ngati amachitira anthu mthoni? Chifukwa choyamba nchakuti mumakhala mdima (ndi angati amatsekula mazenera kuti muloweko mpweya?). Chifukwa china nchakuti m’nyumba zambiri mumakhala mopanda mipando yoti munthu nkukhalapo nkumaphwetsa mkhuto. Nanga mphasa ulimbane nayo usiku, usananso? Ndiye anthu ambiri amakonda kukhala pakhonde kapena kukacheza ku Thileding'i, kapenanso kubwalo kukagoma ntchuwa (36 godi). Titakulako pang'ono kukacha tinkapita kudambo kukadyetsa mbuzi zomayi. Kudambo tinkaphunzirako zambiri: kutumika (kukakusa mbuzi zikalowa m'munda) kuwumba ziboliboli (nyama, magalimoto, anthu, nyau...) uzimba (ziwala: khwiya, noni,chamsipu) kudya (mondokwa (tong'o)), kuyimba, kulimbitsa matupi (kunali nkhonya zongoyamba popanda chifukwa bola mbusha wamkulu walamula- tinkangolemba mzere kutsogolo kwako. Amene afafanize mzere wamnzake ndiye kuti waiyambitsa ndewu. Panalibe kuleletsa mpaka wina achimine. Mukamakapisira mbuzi madzulo, mitu ili mbu ndi nkhonya ngati munagwa paphulusa). Tinkaphunzira kupirira (kunjala, kumenyedwa, kugwira ntchito nthawi yaitali (kunalibe zokadyera masana kapena kunyamula phoso).

Nthawi yovuta inali pamene mmera watuluka. Kwathu kunali anthu ena oipa mitima amene mbuzi zikangolowa m'munda mwawo umangodziwa kuti atemako mwendo mbuzi imodzi kapena mbusha wa mbuzizo awadzola makofi. Mmodzi wa bambowa anali o Sacheuka, omayi!!!. Munthu anali mfiti uyu (alipobe). Mukangokomedwa ndi Chatani (thera) mbuzi nkukalowa m'munda mwawo umangomvera nyimbo "Zalowaa zalowaaa mo Sacheukaaa! Ndiye ngati inali nthawi yako yokakusa umangoyambako kuthamanga mtima ulu thithithi. Pofika m'mundamo mikodzo itayenderera kale. Pobwera kumeneko khutu limodzi litasiya kumva chifukwa cha makofu. Popanda sankaona msinkhu kapena chibale. Izi zinkachititsa kuti tizikhala tcheru nthawi zonse powopa kukunthidwa. Nthawi yosangalatsa inali chimanga chikacha. Panalibenso zonyinyirika kukatsekulira mbuzi kukacha. Ikangofika 10 kaloko aliyense amalowera kumunda komake kapena kogogo wake kukatchola mondokwa. Tsiku limenelo mukangochiumira mtima chimanga aliyense amatha kukatchola 10 kapena 15 nkudzaunjika pamulu. Nkhuni zake tinkakhumula zithima zakhonje zowuma (kale kwathu kunali khonje wambiri ndipo amatulutsa mitengo imene ankamangira madenga ndi nkhokwe. Lero adachepa). Ndiye tikausonkha moto uja timaponyapo chimanga chija chosasenda. Chimapsa mophikika. Ndiyetu kumakhala kutafuna onomuna nyimbo zili pakamwa (Tong'o tong'o adapita tong'o, tong'o tong'o tong'o bwi wang’ana kuno wesa nkugaira) apa kunali kusililitsa amene sanakathyole kwawo chifukwa chakuti sichinache kapena omamuletsa makolo ake. Kunalibe zogawana! Kukamada kumangoti kwaderanji. Ukafika kunyumba nkupeza mkhwani wothira chiluwe ndi chinyenyero kapena kholowa wophikira matsukwa otamuphikira deya, umangodziwa kuti usku uno ndi ng'oma zokhazokha( ndikamvetsera nyimbo yonyamata onyembanyemba ya ‘mbatata ng'oma” ndimangoseka). Zakudya zina zinali mango. Lekani! Tinkayambira anthete odyera mchere. Koma omiyako okangodziwa kuti unatapa mchere, pobwera kumeneko umapeza otakupatulira ndiwo zako zopanda mchere! Makolo masiku amenewo ankalangatu. Ukakana ntchito nkuthawa omanguti "dzuwa linyenga mdima usaka". Pobwera kumeneko umangodziwa kuti lero sindiinyantha (ugona palira khwelu). Koma mango akapsa ndiye kumakhala kuyendera mtengo ulionse kulawa makomedwe. Ndiye kunali kuonetsa luso logenda. Mikono kuguluka koma osatcholako ndi limodzi lomwe. Koma akafika pachimake ndiye timangokwera mumtengo momwemo ndikuyamba kuteketa okapsungu. Potsika m'menemo pansipa pali mbwee anga munali ogologolo. Popita kumudzi mukwangugeya mango okhaokha mimba zili mnzuu, m'manjamu muli matemate msuzi wa mango utayenderera mpaka m’khwapa. Ilo linali kale kumudzi. Mawa tikamba za Khisimisi

No comments: